Macheza lifestyle

Macheza lifestyle Entertainer
Pa macheza page πŸ€—
Kusangalala 24Hrs
The Official Page of Moyenda πŸ”
(2)

17/06/2026

Big shout out to my newest top fans! ΔŽΕ™Γͺezy ÇømpΕ₯âň, Eneles Jeremaya, Catherine K Maseya, Promise Chikalipo, Holiness Mlenga, Priscillah Mdabwi, Mayamiko Andrade, Modester Mukawa, Agie Ntonya, Chizmo Phiri, Dan Raone Chik*ta Kalimba, Thindi Luba, Tapiwa Jamu, Sphart Limbe, Mphatso Mopiwa Maudedi, Memori Wakhenge Jailos, Coffee Veronah Bandah, Esnart Muluda, Zione Kelelesi, Arexander Arexander Tiyesi, Lomoce Matope, Lynah Kazembe, Bertha Lameck Binton, Nicce Chimeza Jnr, Sinature Mavuto, Esther Chimbayo, Steven Roben, Veronna Pretty Banda, Lindiwe Mto, Jean Chisale, Aucean C Katsabola

16/06/2026

REAL LOVE 4

Suzen atacheza kwa mphindo zingapo anaganiza zotsazika k*t azipita ku nyumba akaoneso zina ndioo anamupempha Akuzike k*t amupelekeze. Akuzike anatsazika kwa mayi ake ndipo mayi ake anathokoza Suzen pobwera kuzamuona Akuzike kmaso pazomwe iye amamuchitila akuzike. Apa ananyamuka ulendo kumavaya komuoelekeza suzen. Ali munjira Suzen anayamba kuwaphaphalitsa mafuso kumufusa Akuzike zokhudza tsogolo lake. Suzen anamufusa Akuzike , kod mwayi opita ku sukulu utapezeka ungathe kuputa? Kmaso anamufusa iye ngat atapeza mkazi oti alindalama angalore kwatira naye. Zonsezi Suzen amamufusila dala akuzike chifukwa iye nda mene anali akufuna k*t zitachitika pakati pawo. Akuzike atava mafuso awa akuzike anakhala kaye chete mdipo anayamba kuganiza mmene angayankhele mafuso amene. Kma mwachangu ndimwa nzeru akuzike anayankha mafuso onse bwino bwino.

Akuzike anamuyankha Suzen avekeere ndi khumbo langa kumaliza sukulu kmano vuto ndilot malipilo ndi omwe amasowa kma monga wanena k*t patapezeka onduthandiza nditha kupitiliza maphuziro anga ku sukulu yawukachenjede ndipo ndine munthu osangalala kwambiri ndi chimenechi kma kunkhani yondikwatirayo nditha kungopanga chifukwa cha mavuto kma atati andilipilire maphuziro anga kamaliza tizatengane nditha kuvomera chifukwa chitha kukhala chinthu chabwino kwambiri mmoyo mwathu. Suzen atava izi anakondwa kwambiri chifukwa anawona mmene anayankhira akuzike ndipo zinamugwira mtima. Apa shanil anayandikira kwawo ndipo anamupempha akuzike k*t atha kubwerera iye wafika kale apa. Akuzike anavomele ak*t abwelere kma ak*tepmbenuka suzen anazamugwira kaye dzanja akuzike ndipo akuzike anali odabwa kwambiri ndi momwe anamugwilira, pompo suzen anamuuza Akuzike k*t amapase hagi kma akuzike anali ndi mantha ndipo anapeleka ulemu pokana k*t ayi ndimak*tengan ngat amayi anga.

Kenako akuzike ananyamuka koma Suzen anali atakhumudwa kwambiri chifukwa sanalandile hagi. Kmabe ngakhale zinali choncho Suzen anadziwa k*t tsiku lina adzalandira ndithu. Akuzike mmnenamapita anayamba kuzifusa mafuso opanda ya kho ndipo apa anazindikira k*t mkazi ujayo ali naye nchikondi kma sakufuna kuwonetserara. Akuzike anapitiliza ulendo wake ndipo milu mtima mwake anangoti tizaona tikazakymanaso. Pamene akuzike anali kuganiza izi naye Suzen anali kuganiza k*t akumaneao naye lit ndipo azamutengere k*t akasangalale. Suzen anafika kuden ndipo anasiya kaye kuganiza za izi kotero k*t anayamba kuganiza za zina. Akuzike atafika kunyumba mayi ake anamuyitana ndipo anayamba kumufusa zot pali ubale otan pakati pa iye mdi suzen kma akauzike anati palibe ubale wina oposera chizake. Mayi ake a Akuzike anafusa izi pokuonanchikondi chomwe suzen amaonetsa k*t alibacho pa mwana wawo ndipo ma akuzike anamulangiza mwana wawo k*t apitilize kucheza bwino ndi Suzen chifukwa ndi mtsikana opindulitsa. Apa anayamba kukoza chakudya chamadzuro k*t adye kenako agone. Atamaliza kyphika anadya ndipo onse anagona................................. To be continued Please
@



EVERYTHING IS POSSIBLE ✍️✍️

15/06/2026

REAL LOVE 3

MMAWA watsiku limene Suzen anayamba ntchito anadzuka mmawa k*t apite ku ntchito ndipo anakozeka nkhunyamuka ulendo ovaya ku ntchito. Atakafika ku ntchito Suzen anayamba kugwira ntchito ndipo analandilidwa kwambiri moti anali ndi sangala zochuluka kwambiri. Atava malipilo ake apa mwez Suzen anasangalala kwambiri chifukwa anadziwa k*t ndalama zina atha kumamuthandizira Akuzike pa zinthu zina ku family ya kwawo. Suzen anaganiza zot akaweluka apite kwa Akuzike akamuone k*t akawone mavuto omwe akukumana nawo kmaso k*t anagamuthandize motani mavuto.

Cholinga cha Suzen chinali choti amusamalire Akuzike ndikumuthandiza k*t amalize maphuziro ake ndipo azamukwatile. Ndipo Suzen ananenetsa mu mtima mwake k*t mamuna atenge (In short Suzen meant SHE GOT THIS). Patsikuliatsikuli Suzen anagwila ntchito yake mokhulupilika ndimotamandika kwambiri. Ataweluka anawuyamba ulendo wake opita kunyumba. Ndipo atafika kwawo Anasinthanasintha zovala zake ndik*tsazika kwa mayi ake k*t akukamuwona kaye nzake. Ananyamuka ulendo wake opita kwa Akuzike.

Suzen atafika kwa Akuzike anapeza ana akusewela panja ndipo anawodira mwa ulemu posatengera k*t ndi ana anawalonjera mwa ulemu wake ndipo anawafusa k*t Akuzike mukumudziwa. Ana aja mwasangala anayankha amvekere alipo, asanamuyitame mayi ake Akuzike anatulukira chifukwa anali odabwa k*t nda zimayi akuyitana mwana wawo, atatuluka anawona k*t anali mtsikana wamaonkedwe ake abwino kmaso wa ulemu ndipo iwo anamulomjera ndikumuyitana Akuzike. AKUZIKE atawona k*t anali Suzen anali odabwa ndipo samakhulupilira k*t suzen angabwere kwawo chifukwa anali mtsikana ochokera ku banja lochita bwino. Akuzike anamulonjera Suzen ndipo anati;

AKUZIKE: Mwaswera bwanj bwana wanga

SUZEN: Akuzike sindine bwana iwe ndi ine ndife ofanana pajatu dzina langa ndi Suzen. Usamanditanireso k*t bwana.

AKUZIKE: Ndakuva bwana, eeeeashi chabwino Suzen Kma mwaswera bwanj.

Suzen anaseka mu mtima akuziyankhulira amvekere mamunayi ndi wawupemu ndiipo amachokera ku banja losachita bwino zinangovuta Chabe. Kenako Suzen Anayamba k*t ndabwera uzakuona ndimafuna nditakumana nawe nde ndayamba ntchito nde nditaweluka ndaganiza zakuwone mwina undichezetseko. Akuzike anathokoza pomukumbukira ndipo anamuyamikiraso Suzen k*t ndiwa mtima wabwino. Akuzike anayitana mayi ake ndikuwafotokozera k*t Suzen ndi bwana yemwe amamugaira ndalama ija k*t azigulira zinthu, ma Akuzike anamuthokoza pa zabwino zomwe amachita Suzen. Suzen anawawuza asadandaule ndipo anapempha ma akuzike k*t amulangize Akuzike azimutitanira dzina lake la Suzen osat Bwana.

Kenako suzen anatsazika ndipo anamupempha akuzike k*t amupelekeze kwawo kma ali munjira anayaamba kucheza nkhani zosiyana siyana kuphatikiza kumufusa za tsogolo lake. Iwo macheza awo anayenda chonchi....... It will continue soon

Ndakusiyani mmalere πŸ€£πŸ€£πŸ’”πŸ’”

15/06/2026

GOOD MORNING AGULU

12/06/2026

REAL LOVE 2

AKUZIKE atachoka kosaka ganyu ndipo anapeza ka mtonyo komwe anapasidwa ndi Suzen anabwelera kunyumba sanafuneso kukasaka ganyu kwina. Iye cholinga chake chinali kukadyesra anthu omwe akhala kunyumba. Atango choka Akuzike, Suzen anali ndi malingaliro kwambiri kumuganizira mnyamata amene k*tengera ulemu wake omwe anawonetsa ndipo suzen anayamba kulingalira mwakuya k*t mamuna uja ndiwabwino atha kumusamala atakhala naye pa banja. Kmatu suzen anayamba kupemphelera k*t adzabweleso ndipo adzachezeso patsikulo.

Akuzike atafika kwawo anatenga ndalama ndikuwapasa mayi ake k*t akagule zofunika pakhomo ndipo iye sanakhale ndikalikose. Mayi ake anathokoza kwambiri kuona momwe akuchitira mwana wawo. Tsiku lina mmawa k*tacha, Akuzike anaganiza zopita kwa Suzen kukasakaso ganyu malingana ndi mmene anagwilizirana. Ndipo ananyamuka ulendo atakafika anapeza ma Suzen ndipo anayankula motere;
AKUZIKE: zikomo zikomo kuno

MA SUZEN: Eya zikomo

AKUZIKE: Takupezan mayi

MA SUZEN: Eya khalan omasuka

AKUZIKE: Mayi ndimasaka saka kaganyu nde mayi ena anati zabwereso

MA SUZEN: Aaaaaa dikiran ndimuyitane

Ma suzen anayitana mofuwura akumuyitana mwana wawo k*t abwere azakambirane ndi waganyu amene anamuuza k*t abwereso tsiku limeneli. Suzen anatuluka mwasangala kwambiri chifukwa anadziwa k*t kwabwera mnyamata uja amkamufuna uja. Apa suzen anayankhula motere
SUZEN: Takulandilan khalan omasuka

AKUZIKE: Zikomo madam, ndabweraso monga munandiuzira ulendo ujawo k*t zabwere tsiku la lero

SUZEN: Mwachita bwino mwabwera, ndipo ndimadikila tsiku ili k*t tizakumaneso ndipo ndimafuna kudziwa dzina lanu kmaso zawumoyo wanu kod ndizotheka?

Akuzike anamufotokozera k*t iye ndi Akuzike ndipo akuchokera banja losawuka kma maphiziro ake akuyenda movutika vutik, komaso k*t walemba mayeso a Boma mwez watha. Suzen atava izi chison chinamupeza ndipo anafunitsitsa atazakaona komwe kumakhala akuzike. Patsikuli Suzen anamuuza akuzike k*t abwerereso kunyumba ndipo anamupasa ndalama yochulukirapo. Suzen anamuuzaso akuziike k*t amusinyeze nyumba ya kwawo k*t tsiku lina Suzen azakamuyendere. Apa akuzike anathokoza ndipo anabwerera kumapita kwawo.

SUZENN atakalowa nyumba analandira foni kuchoka ku kampani ina k*t wapeza mwayi wa ntchito ndipo akuyenera kukayamba tsiku lotsatira. Suzen anasangalala ndipo anadziwa k*t azimuthandiza akuzike mosavutikira chifukwa azikhala k*t ali ndi ndalama. Suzen anayamba kulingalira zot akayamba ntchito azamugulire chani Akuzike.

Tiyen tipange share kmaso like k*t Tipitilize kukupatsiran nkhan Zokomazi πŸ™πŸ«‚πŸ«‚

12/06/2026

Good Morning
Ndikuziziraku tawerengan aka πŸ”₯πŸ”₯

10/06/2026

REAL LOVE 1

Panali mtsikan wina amene anali ndi mawonekedwe ake achikoka mmudzi mose kmaso madera ena ozungulira, kotero k*t anthu ambiri amamufuna kwambiri. Mtsikana ameneyi dzina lake linali Suzen. Suzen anali mwana wa wulemu wake mot makolo ambiri amamusilira k*t mwana wawo akanakhala wakhalidwe ngat limeneli. Suzen anabadwira khomo lochita bwino kwambiri kotero anthu amakusilira kwawo chifukwa kunali ku khomo kwa mwana alilenji. Ngakhale zinali choncho Suzen anali atamaliza ma phuziro ake kotero k*t amkangodikira k*t apeze mwayi wa ntchito. Suzen anali wa size ya bwino yoti atha kukhala pa banja. Kma chifukwa anasankha kuphizira sukulu iye anazisunga kma azake a msinkhu umodzi anali atakwatira.

Suzen wakhala akufusilidwq ndi anyamata ochuluka kwambiri kmaso ochokera mmabanja abwino andalama zawo. Kma Suzen sanawavomela chifukwa chinali ku mtima kwake sichimenecho. Mmudzi momwe munali mnyamata wina yemwe anali olimbikira kwambiri maganyu kma sukulu inamuvuta chifukwa chakusowa thamdizo. Mnyamatayi amachokera ku banja losachita bwino kotero makolo ake sakanatha kumamulipilira sukulu. Mnyamatayi dzina lake linali Akuzike. Akuzike atawona mmene makolo ake akuvutikira anawona k*t akalemba mayeso amu fomu 4 asiye sukulu kma k*t ayambe k*thandiza makolo ake kusaka chuma kmaso k*thandiza azing'ono ake sukulu.

Atamaliza kulemba mayeso ake, mmawa wa tsiku lina anadzuka kukayamba kusaka maganyu. Akuyenda anafika pakwa suzen ndipo anakumana ndi suzen ndipo macheza awo anali chonchi;
AKUZIKE: Mwadzuka bwanj madam

SUZEN: Ndadzuka bwino kaya inu

AKUZIKE: Madam ndakupezan ndimafuna kaganyu ngat kangapezeke k*t mwina ndipezeko chithandizo, ndipo ganyu aliyese mungandipase ndigwira musadele nkhawa.

Suzen anamuyang'ana Akuzike ndipo suzen anagwa nchikondi ndimaonekedwe ake. Ngakhale ganyu kunalibe suzen anali ndi ndalama inayake ndipo anatenga ndikumupasa nkumuuza k*t akagwilise ntchito panopa ganyu kunakalibe kaye. Akuzike anathokoza kwambiri ndipo anawonjezera k*t mulungu amudalise. Suzen anakhala ndikulingalira k*t nyamatayi anali bwino kwambili ndipo anali wakhalidwe labwino. Apa anagwa naye nchikondi koma zinali zovuta k*t angofikira kumuuza mmene akufunira. Apa suzen anakanika kumumasukira ndipo anangomuuza k*t mudzabwereso mkuja. Akuzike wnanyamuka ulendo wakwawo apa sanapitilize kukasa ma ganyu kma kukapeleka ndalama ya ndiwo kwa mayi.

Mukuyiwona bwanji imeneyi?
Pleasee like k*t titulutseso part 2 ✍️✍️✍️✍️

10/06/2026

Pomwe Shanil ik*ther 105, Tipitiliza Real Love nde Tingokumbusana πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯ Mwakozeka ?

Mwina mbali yakumeneko akufunika πŸ˜‚πŸ˜‚πŸ˜‚πŸ’”πŸ’”
10/06/2026

Mwina mbali yakumeneko akufunika πŸ˜‚πŸ˜‚πŸ˜‚πŸ’”πŸ’”

Address

Ashford

Telephone

+447745599491

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Macheza lifestyle posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Macheza lifestyle:

Shortcuts

Share