21/11/2025
Pomwe timu ya Goshen City Dedza Dynamos, ili pachiopsezo chowonetsedwa nsana wa njira mu ligi yaikulu ya TNM, akuluakulu a timuyi alengeza kuti akukhazikitsa ndondomeko yosaka osewera obisika m'madera.
Malingana ndi kalata yomwe wasainira Aubrey Kusakala wofalitsa nkhani ku Shepherd Bushiri Foundation, ndondomekoyi yomwe akuyitcha Shepherd Bushiri Foundation, Talent Scouting Football Bonanza, ayikhazikitsa loweruka sabata ya mawa pa 29 November, m'boma la Mchinji.
Kusakala wati dziko la Malawi silosauka ku mbali ya osewera mpira koma wati vuto limakhala pozindikira ndikubweretsa osewerawo pa mbalambanda, zomwe wati ndondomekoyi ibweretsa mayankho ake.
“Malawi ili ndi akatswiri osewera mpira ochuluka, koma kuwazindikira ndikuwabweletsa poyera ndilo vuto," yatelo mbali ina ya kalatayo. "Ndichikhulupiliro chathu kuti ndondomekoyi siipindulira Goshen City Dedza Dynamos yokha, koma dziko lonse la Malawi."
Pa mwambo wokhazikitsa ndondomekoyi pa bwalo la zamasewero la Mchinji komweso oyimba Driemo ndi Lady Aika akakhale akuthyapa mingoli, timu ya Boma Strikers ikachotsana chimbetete ndi timu ya Ludzi Hammers, pomwe Mchinji Villa ikasewera ndi timu ya Mkanda Youth.