03/06/2026
#107.4 FM
Nduna yazachuma a Joseph Mwanamveka ati pali ndondomeko zosiyanasiyana zomwe boma likutsatira zothandizira kukonzaso chuma cha dziko lino.
Poyankhula mu mzinda wa Lilongwe pa mkumano owunikira chuma cha dziko lino ndi nthambi zokhudzidwa, a Mwanamveka ati njirazi zithandizira kuti ndalama zakunja zisamasowe, mankhwala adzipezeka mzipatala komaso kuti ntchito zisamasowe kwa omwe amaliza sukulu zawo za ukachenjede.
Iwo ati unduna wawo uwonetsetsa kuti ukutsatira mfundo zomwe akambirana ku mkumanowu ndicholinga choti zinthu ziyambeso kuyenda bwino.
Wolemba: Joyce Luwani - Lilongwe
(3 June, 2026)