08/08/2025
MWAMBO OWONETSERA PLAN YA MANSE.
Mpingo wa Mount Moriah CCAP ku BCA mu Mzinda wa Blantyre motsogozedwa ndi m'Busa wa Mpingo Reverend Lyton Kilowe, Lamulungu lapitali anali ndi mwambo wapadera owonetsera plan ya Nyumba ya Abusa yomwe akufuna kumanga.
Malingana ndi Reverend Kilowe, ati ndi chokhumba cha Mpingowu kukhala ndi MANSE yawoyawo chifukwa kwa nthawi yaitali, Abusa omwe akhala akutumikira pa Mpingowu amakhala pa Rent.
Plan ya Nyumba yomwe akufuna kumangayi inawonetsedwa ku Mpingo ngati njira imodzi yotsimikizira Akhristu kuti Ntchito yomanga nyumbayi iyamba posachedwapa.
Poyankhula ndi mkulu oyang'anira za mamangidwe pa Mpingowu, Bambo Hawkins Munyenyembe, ati ngakhale akhazikitsa ntchito yomanga Manse yi, alibe ndalama zokwanira zoti atha kumalizira Nyumba yonse. M'mawu awo bambo Munyenyembe ati khomo ndi lotsegula kwa akufuna kwabwino kuti atha kuthandizapo pa ntchito yi. Ntchito yonse kuti ithe ifuna ndalama zokwana 50,000,000 Malawi kwacha ndipo akuyerekeza kuti ntchito yonse itha kuzamalizika pofika December chaka cha 2026.
Mpingo wa Mount Moriah CCAP omwe kwambiri umathandizidwa ndi Akhristu ake komanso ena akufuna kwabwino, ukupezekera m'mudzi mwa mfumu Chipagala, ku BCA mu Mzinda wa Blantyre.