12/10/2025
Akhristu a Mphakati wa St Daniel ku Parish ya Don Bosco awapempha kuti atengeleko chitsazo kwa nkhoswe ya Mphakatiwu Daniel Comboni Oyera pokhala anthu odzichepetsa nthawi zonse.
Bambo Mfumu Mnthandizi wa Parish ya Don Bosco Fr. Elijah Lewole ndiwo apereka langizoli Loweruka pa mwambo wa Misa yokumbukila Daniel Comboni Oyera yomwe ndi nkhoswe ya Mphakatiwu.
Fr. Lewole anati Daniel Comboni Oyera adasankha kudzalalikila Uthenga Wabwino wa Chauta kuno ku Africa pa nthawi yovuta kwambiri komabe sadaope imfa popeza maso awo adali kubweretsa chipulumutso ku Africa.
Iwo anapempha akhristu kuti azikhala moyo odzipereka ndi kudzichepetsa pakati pa anthu ndicholinga chotengera anthu ambiri kuchipulumutso.
Polankhula pa mwambowu, wapampando wa Mphakati wa St Daniel Comboni a Issac Banda, anati chakachi chimachitika chaka chilichonse pa 10 October ngakhale kuti chaka chino chachitika pa 11 October.
Iwo anathokoza akhristu onse potengapo mbali kuti chakachi chitheke koma anati nkhani yayikulu pa chakachi ndikuunikila mozama moyo wa Daniel Comboni Oyera ndi cholinga chopititsa patsolo moyo wa uzimu.
Pambali pa mwambo wa nsembe ya Misa akhristuwa anali mphwando la zakudya ndi nyimbo za uzimu.
Daniel Comboni anabadwa m'chaka cha 1831 ndipo adadzozedwa unsembe pa 31 December 1854. Pa 17 March 1996 Papa John Paul 11 adatcha Daniel Comboni Odala ndipo pa 05 October, 2003 adamutcha Oyera. Daniel Comboni Oyera adamwalira pa 10 October 1881 ali ndi zaka 50.
Wolemba: Victor Chikwawe