29/12/2025
ANTHU OKWANA ATATU AFA NDIPO MAKUMI ANAYI NDI CHIMODZI ( 41 ) AVULALA.
✍️Wolemba_Kupatsa_Manyozo
Anthu okwana atatu amwalira ndipo anthu 41 avulala kaamba ka mvula yamphanvu yomwe inagwetsa zipupa kuyambira pa 22 December mpaka pa 28 December.
Izi ndimalingana ndi kalata yomwe mkulu wa bungwe la DODMA Wilson Moleni wasayinira yomwe ikufotokoza nso kuti anthu pafupi fupi 32,422 ochokera maanja okwana 7,205 akhudzidwa ndi ngozi yi m'maboma okwana 13.
Moleni wati pakadali pano Nthambi ya DODMA ikupereka thandizo loyenerera kwa anthu okhudzidwa -wa monga chakudya, mapepala ofolera nyumba, komanso zofunda mwazina.
Iwo atinso ngati nthambi akugwira ntchito limodzi ndi gulu lomwe limathandiza kupulumutsa anthu panthawi yomwe ngozi ikuchitika, nthambi yopeleka chitetezo mdziko muno ya MDF nthambi ya polisi a Malawi Red Cross komanso nthambi yoona zanyengo kungotchulapo ochepa.
Press