30/08/2026
Mtsogoleri watimu ya Mighty Wanderers a Thom Mpinganjira agula mpira omwe bungwe la Football Legends Association (FLA) lidzigwiritsa ntchito pamtengo wa 15 million kwacha komanso tracksuit yamakaka a bungweli pa mtengo wa 7 million kwacha ngati njira limodzi yothandizira bungweli pachilinganizo chawo chofuna kupeza chuma choyendetsera ntchito zabungweli.
Mwambowu wachitika Ku Bingu International Convention Centre (BICC) munzinda wa Lilongwe.
Pamwambowu panabwera alendo olemekezeka monga anduna azamasewero ndichitukuko cha achinyamata a Alfred Gangata, mtsogoleri watimu ya Mighty Wanderers a Thomson Mpinganjira, mlembi wamkulu wa boma a Justin Saidi, phungu wanyumba yamalamulo kudera la Blantyre Chilomoni a Noel Lipipa mwa ena.
Bungweli likufuna kupeza ndalama zosachepera K250 million pandondomeko yawo yofuna kuonetsetsa Ku umoyo wa osewera akale ukusamalilidwa.
Wolemba Mphatso Nkhoma