
29/10/2024
Bungwe loyendetsa masewero ampira wamiyendo mdziko muno lalengeza kuti lathetsa mgwirizano omwe unalipo ndi mphunzitsi wamkulu wa timu ya Mpira wamiyendo yadziko Patrick Mabedi
Muchikalata chomwe bungweli latulutsa, ati ganizoli lachitika kutsatira mkumano omwe unalipo lolemba pa 28 October 2025 omwe cholinga chake chinali kuunikira zamene timuyi yachitira mumpikisano ozigulira Malo ku ndime yomaliza yampikisano wakuno ku Africa.
Bungweli lati asankha aphunzitsi ena mongogwirizira pamene timuyi ikupitilirabe ndi masewero osiyanasiyana
Padakali pano timu yadziko yagonja masewero ake onse omwe asewera mugulu lawo pofuna kuzigulira Malo opita ku Morocco ku ndime yomaliza.
Wolemba Mphatso Nkhoma (Blantyre)