07/06/2025
NJIRA ZOPHERA MWAMUNA UKATOPA NAYE
```Mzimai wina atatopa nalo banja lake anafuna kungopha mwamuna wake ndipo anapita kwa amayi ake kukafunsa njira imene angamuphere mwamuna wina aliyense popanda wina aliyense kuziwa kuti wachita izi ndi iye.
Ndipo atauuza amai ake anam***andiza motere, mzotheka mwana wanga zomwe ukufunazo koma, ziwa ukuenela kupanga kaye zinthu zoti anthu asakhulupilire kapena kuganiza kuti wachita ndi iwe, nde ukuenela kuchita izi
_💠Uzimukonda kwambiri mwamuna wako, kuposa wina aliyense.
_💠Usapange zinthu zoti m***a kuyambana nyumbamo kwa miyezi itatu.
_💠Uzimuchitila nsanje kwambiri.
_💠Akakupasa ndalama osamanyinyi ngakhale ili yochepa.
_💠Uzimulemekeza kwambiri.
_💠Usapange zinthu zomuphyesa mtima.
_💠munthawi ina iliyonse mupase mwachikondi.
_💠Mukamakangana chonde osamakweza mau, ndipo iwe kwako kuzikhala kupepesa basi kuopa kuti anthu angakumvereni kuti mukukangana.
_💠Uzionesesa kuti mtendere ndiumene ukumanga nthenje nyumba mwako.
Ndipo mai anafunsa ukwanisa? mzima anayankha eya ama, ndipo anampasa tiufa ndipo anati uyu ndi tamerc ndipo uzithira muchakudya cha mwamuna wako daily kwa masiku makumi atatu.
Patangodusa makumi atatu mzimai uja anapitaso kwa amayi ndipo anati ama, mwamuna wanga uja wasinthiratu sindikufunanso kumupha chonde pangani zoti tarmec uja asagwirenso ntchito chonde ama, ndikamupha sindizapezanso mwamuna wabwino ngati amene uja.
Ndipo amai aja anaseka, ndipo anati:
kkkkkkk kuterokotu ufa uja sanali tarmec ayi, unali ufa chabe
chimene chimasowekela mwa iwe anali malangizo amene ndinakupasa aja, waona? Mwamunayotu sanasinthe ayi ndi yemwe uja... koma iwe ukumuona kusintha chifukwa iwe mwini wasintha chikhalidwe, mwana wanga banja ndi chikhalidwe, chikhalidwe mchomwe chimapangisa kuti banja likhale lokoma.
Kuyambira lero uzisatila malangizo amene ndakupasa kuti banja likhale lolongosoka```