
09/04/2025
Oikonda timu ya Real Madrid akuzifunsa kuti agwire mtengo wanji?
Timu ya Real Madrid yaphedwa ngati nkhuku ya Christmas pa bwalo la Emirates dzulo mu chikho cha UEFA Champions League ndi timu ya Arsenal ndi zigoli zitatu kwa duu!
Declan Rice ndi Merino ndiomwe anagoletsa zigoli za timu ya Arsenal ndikuzizimutsa timu ya Madrid.
Zateremu timu ya Real Madrid ikuyenera kukapeza zigoli zinayi pa bwalo lawo la Santiago Bernabeu kuti ikapitilire mu chigawo china.