
03/07/2025
Bungwe la National Initiative for Civic Education - NICE Trust lapempha anthu omwe akupikisana nawo m'maudindo osiyanasiyana pa chisankho cha pa 16 September chaka chino kuti asunge bata mu nthawi yomwe adzichita misonkhano yokopa anthu.
Mkulu woyendetsa ntchito za bungweli ku Blantyre, Glory Ngosi Maulidi, wanena izi lero pa bwalo la sukulu ya pulaimale ya South Lunzu ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre pa mtsutso omwe bungweli linakonzera anthu omwe akupikisana pa uphungu komanso ukhansala ku deralo.
Iye wati ndi kofunika kuti anthu akhale ndi chidwi pomva mfundo za adindo omwe akhale akuwafikira ku madera awo ndi kudzasakha moyenera.
Pothilirapo ndemanga, mkulu wa bungwe la Institute for Policy Interaction (IPI), Nandin Patel, wapempha aphungu omwe akuyimira pa chisankhochi kuti akadzasakhidwa adzawonetsetse kuti akumapezeka mu nyumba ya malamulo komanso ku dera komwe akuyimira, osati kutanganidwa ndi zinthu zawo monga zakhala zikuchitikira m'mbuyomu.
Omwe anatenga nawo mbali pa mtsutsowu ndi aphungu oyima pawokha komanso a chipani cha United Democratic Front (UDF) pamene makhansala anali ochokera m'zipani za UTM, Odya Zake Alibe Mlandu ndi ena oyima pawokha.
fm