05/01/2025
: Kafukufuku watsopano wapeza kuti kusuta kumachepetsa nthawi yokhala ndi moyo kuposa m'mene madotolo amaganizira.
Malingana ndi kafukufuku yemwe anachitika pa anthu osuta fodya mdziko la Britain, ndudu imodzi ya fodya imachotsa pafupifupi mphindi 20 pa moyo wa munthu, kutanthauza kuti paketi ya ndudu 20 ingafupikitse moyo wa munthu ndi pafupifupi maola asanu ndi aΕ΅iri.
Pambuyo powerengera nkhani ya za chuma komanso zinthu zina, Ochita zofufuza pa sukulu ya University College London apeza kuti amayi amachepetsa moyo wawo ndi mphindi 22 pa ndudu iliyonse yomwe asuta pamene amuna amachepetsa moyo wawo ndi mphindi 17 pa ndudu iliyonse.
-Alex Batison-
Source: CNN