FUKIZ MW

FUKIZ MW Home of good stories

SHE'S NOT MY SISTER _______________________PART 6_______Written by Fukiz mw _____________________Amayi amatiweva akuseke...
17/06/2026

SHE'S NOT MY SISTER
_______________________


PART 6
_______


Written by Fukiz mw
_____________________

Amayi amatiweva akusekera poganiza kuti tikupita kumudzi kokacheza koma ife m'mutu mwathu muli maganizo okataya mimba. Titafika pa Nchalo trading tinakwera minibus yopita kwa Ngabu . Kwa mphindi zingapo tinali titatulukira kumudzi kwawo kwa adad . Agogo anatilandilabwino ndipo tinachezanawo masana onse . Madzulo atafika David anandipatsa mankhwala okuti ndimwe. Ndinalandira mkono wanga ukunjenjemera , sindikudziwa kuti anali mankhwala anji koma ndinamwa pofuna chitsikana, kuwabisila makolo komanso ndicholinga chokuti ndipitilize school. Nditamwa mankhwala aja botolo lake ndinalitaya mu toilet, kenako tinabwerera mnyumba . Titalowa nyumba tinapeza chakudya, sitinachedwe tinadya. Titamaliza kudya tinayamba kucheza uku m'mimba mwanga mukungolira gugulu gugulu. Itafika nthawi yogona, Agogo amuna anamuuza David kuti akagone mugowelo pamodzi ndi anyamata amzake . Pamene ine anandipatsa chipinda mnyumba ya Agogo kuti ndikagone . David atamva izi anakana.

"Agogo ine ndizigona pa sitting room p***a."
Sindikudziwa kuti anapanga zimenezi chifukwa chani . Agogo anamukakamiza zokagona mugowelo koma anakakamila mpaka anamulora kugona pabalaza paja. Itakwana nthawi yogona, David anachotsa zinthu zina ndizina pabalaza paja kenako ndikuyala mphasa ndikugona . Kenako ine ndinapita kuchipinda changa kukagona koma m'mimba mwanga ndisakupezako bwino. Mosataya nthawi Agogo amuna anazimitsa torch ๐Ÿ”ฆ ndipo tinayamba kugona. Pakati pa usiku m'mimba mwanga munayamba kupotokola kwambiri. Ndimati ndikagonera mbali iyi osagwira kuyesera kukhala pansi mtendere osapeza , ndinatopa ndikupilira ndinafika poyamba kulira koma mosisima . Ndinatenga phone kuziunika ndinaona magazi akutuluka . Apa zinakolezera mantha anga ndipo misozi yamoto inayamba kutuluka mkumatsikila m'masaya mwanga. David anandimva mwachangu kuti ndikulira. Anadzuka pogona pake paja ndikubwera kuchipinda changa chija mwanyang'anyang'a(tiptoe ) cholinga Agogo asamumve . Atafika anandifusa akuyankhula monong'ona .

"Thandie , chavuta ndichani? "

Sindinamuyankhe ndinamuonetsa pogona panga . Ataona kuti zovala zanga komanso pogona panga pali magazi okhaokha anandiyang'ana mosonyeza kutinayeso zamuopsa , koma amangozilimbitsa ntima pokuti ndiwamamuna . Nthawi imeneyi mtendere ndinalibe chifukwa ndimamva ngati wina wake akukoka matumbo m'mimba mwanga. Kenako David anayankhulanso monong'ona.

"Ndikupita pogona pangapo , ndye uwayitane Agogo kuti ukufuna kukodza tikatero ndikuperekeza. wamva ?"

Ndinamuvomera ndimutu uku nditazolika pansi manja anga nditagwira pamimba. David anabwera pogona pake kenako ndinayitana.

"Ago!!, Agogo!!"

"Eeh ukuti bwanji Nana?."
Anavomera akunditchula kuti Nana . Sindikudziwa kuti dzina la Nana limatanthauza chani koma ndimangovomera. Kenako ndinati:

"Ndikufuna ndikakodze ."

"Gututu ilikomweko pakonapo."

"Iiiii sorry , ndikufuna ku toilet."

Posakhalitsa ndinawamva akudzuka pogona kuwasiya Agogo akazi . Apa mantha anandipeza kuti ayitulukila plan yathu chifukwa akubwera . Nthawi yomweyo ndinamva mau a David.

"Ago, dzigonani ndimuperekeza ndineyo."

Mwamphamvu ya Mulungu Agogo anamvetsetsa ndipo sanabwerenso pogona. Mosataya nthawi ndinatenga zomwe ndinagonera komanso zovala zanga zonse ndinapitanazo kuti toilet . Nditafika chilichonse chomwe chinapakika magazi ndinachitaya toilet . Ndinakhala mu toilet pafupifupi 2 hours ndikudikila zinthu zonse zituluke lucky enough inali ya mwezi umodzi ndi week. Kenako ndinatulu kupita panja pomwe ndinayamba kugudubuka ndim'mimba. Pomwe zimachitika izi David anali pambali panga phone ilim'manja. Nditayang'ana nkhope ya David ndinaona mantha pankhope yake . Ululu omwe ndimamumva ndinayamba kumazimva kuti nditha kufa . Nthawi yomweyo ndinamupempha Davie.

"David, ayimbire Mamie p***ano."
Ndinayankhula ndikulira chifukwa ndimaona ngati kutaya mimba ndikwa simple . Maganizo anga ndimati ndikangomwa mankhwala , zonse zituluka mosavuta. Ndye David nditamuuza zowayimbira Amayi zija iye anati:

"Ingopilira babe, watsala ndiululu okha koma zonse zathekakale."

Atayankhula mau awa ndinamuyang'ana David uku ndikudzifusa . "Chifukwa chani Davie akunditchula babe? Week yatha ndikumuuza za mimba anati tidakali ana moreover ndilibe podalira. Zimenezi zikutanthauza chani?"

Ndinayamba kugudubuka panja chifukwa mtendere ndinalibe . Agogo akazi ndi amuna poona kuchedwa anatuluka ndipo anandipeza ndili pakhonde nditalefuka. Atandiona anandifusa.

"Nana , chavuta ndichani?"
Ndisanayankhe anayankha ndi David mwachangu kwambiri.

"Akutsekula m'mimba . I think madzi apachitsimewa amuda"

"Iiiii pepa Nana. Ifetu madzi apa Mjigo , pachitsime timangomwa sitionanso vuto."
Anatero akusisita dreadlocks yanga.

"Ndye ndim'mene alilimu kulibwino tidzipita kuchipata akakupatse Thanzi ORS kuti madzi anthupi abwerere."

Atankhula nkhani ya kuchipatala ndinayankhila.

"Ayi Ago, bola pano ndikumva bwino."
Ndinatero pozemba kuchipatala kuti akaulula zinsisi zomwe tikubisa . Kenako ndinaona Neba wina akubweretsa Nthazi ORS . Agogo anasungunula mwachanguchangu ndikundipatsa. Ndinazikakamiza kumwa Thanzi uja , kenako ndinayimilira modzilimbitsa ndikulowa mnyumba . Ndinapita pogona panga . Ndinakhala pansi uku ndikulumbira kuti sindizakhalanso malo amodzi ndi mnyamata aliyense.

Pamene nthawi imakwana chama 3 m'banda kucha ndinapezamo kamtendere mpaka tulo linandipeza ndikugona.

M'mawa kutacha Adad anayimba phone kwa Bambo awo . Atacheza kwakanthawi anafusa zaanafe . Kenako Agogo anati:

"David ekha alibwino , koma Nana sitinagonenaye bwino wachezera kutsekula m'mimba usiku onsewu."

Anayankhula a pang'ono kenako anayidula phone ija. Panangodutsa maola awiri(two hours) ndinaona galimoto ya amayi ikutulikila kumudzi kuja. Atafika anatsika galimoto mwaphuma uku atavala zovala mosonyeza kuti achokera kuntchito . Kenako anafikila kwa Agogo

"Ama ndi adad mulibwanji ?"
Anatero popeleka moni kwa Agogo onse awiri.

Atapatsana moni ananditembenukira.

"Thandie, ndamva bambo ako akuti ukudwala. Pakadali pano ukupezabwanji?"

"Bola panopa , koma dzulo sindinagone ndinatsekula kwambiri ."

"Unadya chani?"

"I think nsima yamapira ndi madzi akuchitsimewa, ndiomwe sanandiyanje."

"Ndye tipite kuchipatalatu eti?"

"Ayi , ndikumwa Thanzi ORS apapa ndye ndikuona kusintha."

Amayi amafuna atanditenga kuti ndizipita kunyumba limodzi koma anachita manyazi poopa kuti akhala ngati abwera kuzatenga mwana wawo kuti mwina sindikusamakilidwabwino. Kenako tinapita ku shop komwe anakagula Ufa 50kg ndimabotolo amadzi 4 ma 5L ndizinthu zina.

"Zikatha zinthu zomwe ndagulazi undiyimbire phone, usamamwenso madzi akuno ukumva ?"

Ndinavomera kenako anandipatsa kiss patsaya . Anapitanso kwa David ndikumuhaga . Mosatenga nthawi ananyamuka kukakwera galimoto yawo kumabwerera ku Nchalo.

----

Sabata imodzi itatha , ndinayamba kuzimva bwinobwino koma thupi langa limaonekabe kuti ndimadwala . Kenako tinapita kokaonela mpira ku ground . Tinaonera Mpira onse mpaka unatha . Kenako tinayamba kubwerera kunyumba kamdima katagwa. Tilinjira David anandigwira mchiuno , mosataya nthawi ndinachotsa dzanja lake lija.

"Bwanji Thandie?"

"Mmmm ayi David zibwana inde tizipanga koma zibwana zinazi zitha kuchotsa moyo wamunthu sure . Ndye panopa ndilibenso chikhumbokhumbo chogwiragwirana ndimamuna . "

Nditakamba izi David anandisiya kundigwira kuja . Tinayenda osandilankhulanso . Ndikayambitsa nkhani iye amangondiyankha modula "eya , ayi , mwina, sindikudziwa." Apa ndinadziwa kuti wakhumudwa . Kenako ndinamugwira mkono . Nditamugwira mkono anandiyang'ana . Mosataya nthawi ndinamufusa.

"Wakhumudwa?"
Ndinamufusa momudela nkhawa monga mukudziwa zachikondi . Kenako iye anati.

"Ayinso."
Anayankhula mau awa uku asakusangalala. Kenako ndinamutembenukira ndikumukumbatira. Kenako ndinamufusa

"Pamenepo ukumva bwino?"

"Yeah"

"Ngakhale ukumva bwino koma ndiife pachibale Davie."

Sanandiyankhe chifukwa phone yake inayitana . Atapanga check anaona kuti ndi adad. Atayiyankha , adad anamuuza kuti atumiza ndalama mu phone yake yokuti mawa tipangere transport tizibwerera ku Nchalo. Kenako tinayenda mpaka kukafika kunyumba komwe ndinapeza Agogo akuphika. M'malo motifusa tonse anandifusa ine.

"Nana , kutauniko mumayenda chonchi kumabwera ndi mdima pakhomo?."

"Pepani Ago , mpira unatha mochedwa."

"Dzuwa lisanalowe mwana wamkazi amayendera azikhala atafika pakhomo cholinga tizizaphikila limodzi chakudya."

"Anandichedwetsa ndi David-yo ndimamudikira."

"Awa ndanyamata osamawadikila chifukwa amakhala akusaka zitete."
Ndinangoseka pansi pantima ndikudziwa kuti chitete cha David ndine ndemwe. Kenako ndinakhala khitchini muja uku ndikuwaunikila pomwe amaphika mpaka chakudya chinapsa. Kenako ndinanyamula kukalowanacho mnyumba ndipo mosataya nthawi tinayamba kudya . Titamaliza kudya tinacheza pang'ono kenako tinapita kokagona.

M'mawa kutacha tinatsamzikana ndi Agogo kumabwerera ku Nchalo mission yomwe tinabwerera itayendabwino mopilira momwemo. Nditafika ku Nchalo tinalowa kumpanda wakunyumba . Nditatsekula chitseko , ndinawaona amayi ndi adad ali pampando . Amayi atandiona anandithamangira ndikuzandihaga . Uku akulankhula

"Queen wanga mkuzatulukira , umwe madzi abwino komanso ndiwauza Anaphi akuphikire zakudya zabwino uzitolere ."

Pomwe amayi amakamba izi Anaphi amandiyang'ana mondikweza ndikunditsitsa . Izi zinawadabwitsa amayi . Amayi anandiyang'ana kenako anawayang'ana Anaphi. Kenako Anaphi anachoka pamalo paja kulowera ku kitchen uku akupukisa mutu kwinaku akumwetulira............


Tikumanenso mu part 7

FUKIZ MW

Kotaya mimba kwavuta , a Thandie ayamba kuwafuna mayi  chonsecho amawathawa kuti asadziwe hhhhmmm ๐Ÿ™Œ๐Ÿ™Œ๐Ÿ™Œ
17/06/2026

Kotaya mimba kwavuta , a Thandie ayamba kuwafuna mayi chonsecho amawathawa kuti asadziwe hhhhmmm ๐Ÿ™Œ๐Ÿ™Œ๐Ÿ™Œ

17/06/2026

Zotsatila za unofficial, zayamba kufika Ku Tally centre ๐Ÿคธ๐Ÿคธ๐Ÿท๐Ÿค”

SHE'S NOT MY SISTER _______________________PART 5________Written by Fukiz mw _____________________Ndinapanga izi chifukw...
16/06/2026

SHE'S NOT MY SISTER
_______________________


PART 5
________


Written by Fukiz mw
_____________________

Ndinapanga izi chifukwa masiku amenewa ndinamuona kuti Thandie wayera m'maso kwambiri, ndye ndinawathamangitsa anyamata aja poopa kuti angamupatse mimba mwana wanga chifukwa anali Namwali osayamba wa packet ndipo period yake ndimayitsatila mwezi ndi mwezi. Olo asandiuze kuti wayamba period, ndekha ndimamudziwa chifukwa amandipempha ndalama yokuti akagule mankhwala chifukwa m'mimba mumamuvuta kwambiri.

Tsiku lina ndilipa sitting room ndili busy pa laptop ๐Ÿ’ป yanga , ndinawaona Anaphi akuoneka kuti alindinkhani koma amasowa poyambira . M'malingaliro mwanga ndimaganiza kuti mwina akufuna andipemphe zopita kwawo akaone anthu . Kenako ndinawakodola kuti abwere pomwe ndinakhala paja . Atafika ndinawafusa ndikuwamwetulira.

"Lero mukuoneka ankhawatu bwanji? Tidziti mwawasowa ana anu kapena mukufuna mutawaona eti?"

"Kuwasowako sikungalephere madam."
Anatero akuseka kenako anapitiliza kundilankhula.

"Koma Madam , pepani polowerera za m'banja mwanu."

"Don't worry Anaphi inunso ndi part imodzi ya banja lathu . Tayankhulani mukuti bwanji? "

"Kodi mukumawaona bwanji anawa?"

"Kumbali yanji? "

Ndinafusa uku ndikusiya glass ๐Ÿท lachokumwa lomwe linali m'manja mwanga iku ndikuwayang'ana mwachidwi kwambiri. Kenako anati:

"Ah, ine machitidwe awo akumandibalalitsa penapake . Pena ndikumawaona ngati ndipachibale koma pena ndikumawaona ngati alimchikondi."

Atayankhula izi ndinawayang'ana mowakweza ndikuzawatsitsa chifukwa zinandinyasa. Kenako ndinati:

"Anaphi , inuyo muzigwira ntchito yomwe ndinakuyitanirani pano , musakhale camera yotijambula ayi . Mukudziwa kuti ndavutika motani kuti ana amene aja ayanjane? "

Anaphi anagwedeza mutu kusonyeza kukana kuti sakudziwa . Kenako ndinafusanso.

"Mukudziwa kuti zomwe amapanga Thandie zija zikanandithetsera banja?"

"Pepani madam sindi......."

Asanamalize kulankhula ndinawadula mau mkamwa.

"Inuyo ndimboni Thandie ndakhala ndikumumenya kangati kuti agwilizane ndi David? Lero ana aja agwirizana lero mukubwera ndi nkhani za nonsense ngati izizi."

"Pepani Madam sindimadziwa kuti nkhaniyi ifika kumeneko mundikhululukire ."

"Inuyo gwirani ntchito yomwe ndinakulembani , chifukwa mulibe udindo ulionse pa ana anga ndipo ndikudziwa ndekha m'mene ndingawalele mwandimva?."

"Koma Thandie wakulira m'manja mwangamu ndye ndikamamuona ndinamuona ngati mwana wanganso."

"Ndimakulipilani sikuti Thandie mumamulera ulele ayi , ndye mundisiye ndimulele mwana wanga m'mene ine ndikufunila."

"Sorry madam"

Atayankhula mau awa ananyamuka kupita panja kumakasesa masamba omwe anagwa m'mitengo. Nthawi imeneyi ntima wanga unali utatentha kwambiri chifukwa anandikhumudwitsa. Kenako ndinamuyitana Thandie kuti azatenge ma pad anga omwe anatsala chifukwa nthawi imeneyi ndimadzimva ngati Salimu wagoletsa chigoli.

"Mamie ndabweratu mumati bwanji?"

"Ndikawerengera 28 days yako , zikundionetsa kuti period uyamba lero kapena mawa ndye tenga izi ukagwiritse ntchito."

Ndinatenga ma pad aja kumupatsa komanso mankhwala. Kenako ndinatuluka panja kukatenga galimoto yanga kupita kwa mzanga kuti ndikapitulidwe mphepo ina chifukwa Anaphi anandibowa ndinkhani zawo zopanda umboni zija.

THANDIE'S POV

Nditalandira katundu yemwe anandipatsa amayi , ndinapita ku chipinda changa kuyamba kuwerengetsa masiku anga opangira period. Nditawerengetsa bwinobwino ndinaonadi kuti amayi aja samanama . Ngakhale tsiku langa linakwana koma m'mimba simunandipweteke munaliziii komanso sindinaone chizindikiro chilichonse chokuti ndipanga period anytime. Kenako ndinaziponyera pa bed langa ndilibenso nkhawa chifukwa munthu umakhoza kusintha nthawi yopangira period.

Madzulo atafika ndinaona period yanga yayamba koma simunandionetse chizindimilo chilichonse chokuti ndipanga . Sindinachedwe ndinapanga madongosolo anga kenako ndikumagona

Mam'mawa kutacha ndinamva munthu akugogoda pa chitseko changa . Ndinadzuka ndikukatsekula chitseko, nditasuzumila ndinaona kuti ndi amayi avala zovala zawo kusonyeza kuti akupita kuntchito . Analowa kuchipinda changa ndikutseka chitseko . Atafika anandifusa.

"Wayamba?"

Nditamva fuso ili sindinafuse kuti ndayamba chani chifukwa mwezi ulionse amandifusa fuso limeneli ndipo amandilonda sindikudziwa kaya ndimawakayikitsa kaya. Mosatenga nthawi ndinawayankha.

"Eya ndayamba."

"Tapanga ndione."

"Aaah Mamie ingomvani kuti ndayamba."

"Mwayamba manyazi, mwakuka eti?"

Atandifusa fuso ili ndinawaonetsa pad ija mwaukadaulo chifukwa mwezi umenewo period yanga inali yochepa kwambiri kusiyana ndinthawi zonse. Ndipo izi zinali zondidabwitsa koma sindinawafuse amayi. Kenako ndinawaona amayi akutsekula chitseko kumapita kuntchito.

Masiku awiri anadutsa osasambaso . Izi zinayamba kundipatsa mantha chifukwa ine ndi David chinali chizolowezi chathu tikasowa zochita timakabindikila kuchipinda chake makolo athu akakhala kuntchito.

Masiku anapanga masabata awiri, panthawi imeneyi David anali atsala pang'ono kumaliza kulemba mayeso ake . Ine ndinali ndilipa holiday yodikili zotsatila zamayeso athu. Panthawi yomweyi ndinayamba kumva zizindikiro zamimba . Mtima wanga unayamba mantha . Ndinakhalaphee pa bed uku ndikuzifusa. " Ngati ilimimba ndipangenayo bwanji? Ndye akamandifusa ndizinena kuti ya David? Ayi noo ndikuyenera ndimuuze David akabwera ku school." Ndilimkati moganiza nselu inandipeza . Ndinatuluka kuchipinda changa kuthamangira ku toilet . Kumeneko ndinakasanza madzi okhaokha . Pomwe ndimatuluka ndinakumana ndi Anaphi. Anaphi sanandifuse kalikonse amangopanga zawo aliphee. Kenako ndinabwerera kuchipinda changa kukagona. Sindikudziwa kuti ndinatopa ndichani koma ndinagona tulo mpaka Anaphi anandidzutsa kuti ndikadye chakudya chamasana. Ndinadzuka kupita pa sitting room, nditavundukula ndinapeza aphika nsomba ndi masamba . Ndinangovindikila sindinadye chifukwa mkamwa mwanga mumafuna Nyama . Kenako ndinapita mu fridge kukatenga zipatso kubwerera kuchipinda changa . Chama 4 koloko itakwana ndinamva mau a David akulankhula ndi Anaphi. Apa ndinadziwa kuti David wabwera kuchokera ku school kolemba mayeso . Nthawi yomweyo ndinamuyimbira phone . Itayitana kangapo anayiyankha .

"Hello"

"Hello , tabwera ku chipinda changa kuno."

"Ok ndikubwera."

Patadutsa kanthawi pang'ono ndinamuona akulowa pa chitseko uku m'bale ya Nsima ilim'manja akudya . Kenako anatseka chitseko ndikuzati:

"Umati bwanji?"

Ndisanamuyankhe ndinapumila m'mwamba kulikusowa poyambira . Kenako ndinangofikila pa point.

"David, ndikudzimva ngati ndili ndi mimba ?"

"Chani?๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜ณ"

Anandifusa modabwa uku akusiya mbale ya Nsima ija pansi. Kenako ndinabwerezanso.

"Ndili ndimimba ndye ndikulingalira kuti Kodi ndiwauze amayi?"

"Ayi usawauze."

"Ndye nditani?"

Tinakhala mchipinda changa chija kwakanthawi ndithu koma panalibe yemwe amayankhula mzake . Kenako ndinamumva David akuti :

"Thandie, ukuyenera uchotse mimba imeneyi wina aliyense asanadziwe . Chifukwa amayi ndi adad akangodziwa ivuta nkhaniyi."

"Ayi ine sindichotsa ndingothawa ndizipita kwagogo anga ku Mulanje."

Nditakamba izi ndinamva mau amayi. Izi zinakolezera mantha mkati mwa ntima wanga . Kenako David anati :

"Thandie , ukudziwa chani?"

"Ayi sindikudziwa."

"Tidakali ana moreover ndilibe podalira. "

Atayankhula mau awa ndinamuyang'ana modabwa David ndipo ndinamufusa.

"Ukutanthauza chani ukati tinakali ana komanso ulibe podalira?"

"Aaah basi nkhani imeneyo yatha tiye tingopanga zotaya mimbayi. Ndye chomwe chikufunika apapa ndichokuti, tinyamuke tipite kumudzi kwathu ukataye mimbayi. "

"Amayi sangandilore."

"Unene kuti ukufuna akakudziwe kwathu."

Kenako ndinamva mau amayi akuyankhula kusonyeza kuti akubwera kuchipinda changa chija . Tinasiya zokambirana zathu zija ndikukhala pa bed ndikuyamba kusewera ma game ๐ŸŽฎ pa screen yomwe inali kuchipinda changa. Amayi anatsekula mokhalangati motidzidzimutsa ndipo anatipeza tili busy ndi game ๐ŸŽฎ. Kenako anamulankhula David.

"David m'malo mowerenga uli busy ndima game ?"

"Ndikuchoka powerenga ndye ndikufuna ndipange refresh brain."

"Alright, ndimadabwatu ..... Mayeso mumaliza liti?"

"Ine ndatsala ndi pepala limodzi . Ndye ndikabwera nthawi yabwino ndizizapita kwa Ngabu ndikawaone Agogo."

"Mmm kungomaliza mayeso kunyamuka? Ayi uzapite weekend.... "

Asanamalize kulankhula inenso ndinayankhila .

"Inenso ndipita kumudzi ku Mulanje ndikawaone Agogo."

"Uzapita kumulanje ndiine mwezi wamawa."

"Kodi ine mumandikhomerera chifukwa chani? Ok chabwino ndipita ndi Davie kwa Ngabu ndikakudziwe kwawo kwa adad."

Anapumila m'mwamba kenako anati :

"Kaya tiona weekend."
Anatero akutuluka kuchipinda kuja.

----

Weekend itafika David anakomzeka zopita kumudzi kwawo . Inenso ndinakakamira kuti ndikakudziwe kwawo kwa adad . Amayi ataona kuti ndili serious ndizakumudzi zija , anamuyitanila pambali David . Ndipo anamuuza kuti .

"David , achemwali anuwa akakamila kuti akakudziwe kwabambo anu . Ndye mukapita kumeneko chonde uzikamuonetsetsa asakatengeke ndanyamata kumeneko . Pepatu ndakuuza izi chifukwa atsikana amavuta kulera kusiyana ndi anyamatanu."

Kenako ndinamumva David akuti :

"Don't worry mom , ndikakaona china chake chokayikitsa ndidzakuyimbirani phone kuti mudzamtenge ."

Kenako amayi anabwera komwe kunali ine kuja kuzandipatsa OK kuti nditha kupita kumudzi. Nthawi yomweyo ndinavala zovala zina ndikubelekera bag yazovala . Kenako tanyamuka ulendo wakwa Ngabu. Amatiweva akusekera poganiza kuti tikupita kumudzi kokacheza koma ife m'mutu mwathu muli maganizo okataya mimba...........


Tikumanenso mu part 6

Ndangolemba mokuti zithele iya. That's why ndaponya mochedwa.

Muli inu  Anaphi, mungadzayankhulenso zokhudza Thandie ndi David? ๐Ÿค”๐Ÿค”---Koma mwaswera bwaa?
16/06/2026

Muli inu Anaphi, mungadzayankhulenso zokhudza Thandie ndi David? ๐Ÿค”๐Ÿค”
---

Koma mwaswera bwaa?

SHE'S NOT MY SISTER _______________________PART 4________Written by Fukiz mw _____________________Thandie anasiya kundip...
15/06/2026

SHE'S NOT MY SISTER
_______________________


PART 4
________

Written by Fukiz mw
_____________________

Thandie anasiya kundipeza kuti ndimuthandize Homework, m'malo mwake amapita kuchipinda cha David ndikumaphuzitsana. Apa umoyo wanga unayamba kumva kukoma polingalira kuti ana anga ayamba kumvana. Kunena zoona zomwe amapanga Thandie masiku am'mbuyomu , zimandinyasa chifukwa zimakhala ngati ineyo ndimachita chomutuma kuti azimulalatira David, kotero zimandipatsa pressure kuti mwina Salimu atha kusintha makhalidwe ake banja langa ndikusokonekera.

THANDIE'S POV

Ndinali ndili kuchipinda cha David phee kundiphuzitsa mathematics. Chidwi changa chonse chinalikwa David kuona m'mene akusovera maths. Chifukwa chokuti mchipinda cha David munalibemo mipando , izi zinatipangitsa kukhala pa bed lake. Posakhalitsa ndinamulozeranso Samu yomwe imandivuta ndipo iye anati:

"Semitenious equation ndiyosavuta timangotere.

3x + 2y = 21
y=x+3

substitute y and solve to find x

3x +2 (x -3)= 21
3x+ (2x + 6)=21
5x + 6=21
5x=15
X=3

Wamvetsetsa m'mene tamupezera X kuti ndi 3 eti?"

"Yeah ndamvetsetsano."

Ndinalankhula mau awa uku ndikutolera mabukhu ndi scientific calculator yanga . Pomwe ndimatolera mabukhu anga , David amangondiyang'a mwachidwi sindikudziwa kuti m'mutu mwake mumayenda chani. Nditatenga ma book anga ndinamutsamzika .

"Basi ndapita tionana."
Ndinatero uku ndikulunjika pakhomo . Koma ndisanafike pachitseko ndinaona David akundigwira mkono kwinaku akundifusa .

"Ndye wati ukupita?"
Anayankhula akundiyang'ana straight m'maso mwanga. Mosataya nthawi ndinayankha motsitsa mau

"Yeah. Bwanji?"

Sanavutike kundiyankha fuso langali , m'malo mwake anandiyandikira kupangitsa kuti mabere anga azimubaya pantima pake. Ndinabwerera m'mbuyo koma iye amangonditsatirabe mpaka ndinakafika ku khoma . Kenako ndinati :

"David, don't you know that you are my ....."

Ndisanamalize kulankhula anayika chala chake pakamwa panga uku akuti shiiiiii. ๐Ÿคซ๐Ÿคซ๐Ÿคซ cholinga ndisalankhulenso.
Apa ndinadziwa zomwe amafuna . Ndye pokuti amayi samandilora kutuluka kumpanda komanso school yomwe ndimaphunzira ine inali ya atsikana tokhatokha, ndinamutsamzira David maganizo ake๐Ÿ™ˆ.


MARY'S POV

M'dima utagwa madzulo , wantchito anabweretsa chakudya la dinning room. Ndipo tonse tinapita kukayamba kudya . Pomwe timadya Thandie ndi David amakamba nkhani zawo ndikumaseka . Pomwe ndinawaona anawa akusekererana muntima ndinazilankhulira ndekha . "Ambuye mukule ine ndichepe sindimadziwa kuti ana awa angagwirizane."
Titatha kudya tinacheza pang'ono kenako tinapita kokagona. Ine nditafika pogona sindinagone mwachangu ndinamudikila Salimu agonekaye . Atagona ndinatenga phone yake ndikupita ku WhatsApp cholinga ndikaonenso zomwe akumambirana ndimwana wake . Nditafika ku chat cha David, ndinapeza Salimu atayankha message yomwe mwana wake anamulembera ija. Ndipo iye anati:

"Pepa mwana wanga sindimadziwa kuti ukudutsa muzimenezi , koma dziwa kuti sindingakutaye. Popeza iwe ndi Thandie simukumvana, palibe vuto pamenepo ndipeza njira ."

Mau amenewa anandipweteka muntima . Ndinakhala pheee uku ndikubwereza mau omwe analemba Salimu. " Popeza iwe ndi Thandie simukumvana, palibe vuto pamenepo ndipeza njira. Salimu akutanthauza chani pamenepa?" Kenako ndinapanga scroll down kuona message yotsatira ya David ndipo anati:

"Adad , basi zinthu zija zinasintha tikukhalabwino kwambiri. Izi zilichonchi chifukwa cha amayi akhala akutiyanjanitsa ndipo ndikuona kusintha kwambiri."

"Okay mphwanga."

Salimu anayankhamotero.
Nditamaliza kuwerenga message iyi ntima wanga unatsika pansi uku ndikuzilankhulira ndekhandekha . "Zoonadi apowo ndimizu yakachere amakumana pansi." Ndinakamba izi chifukwa Salimu samaonetsa makhalidwe oyipa aliwonse , ndipo amapanga act ngati zomwe zikuchitika pakhomopo sakudziwa kalikonse koma chonsecho amadziwa chilichonse kudzera kwa mwana wake David . Kenako ndinasiya phone pomwe ndinayipeza kenako ndikugona.

M'mawa kutacha ndinadzuka mochedwa chifukwa ndinagonanso mochedwa. Ndinatsekula chitseko ndikusuzumila pa sitting room, ndinapeza Thandie atavala bathing towel yokha uku akupanga clean carpet ndi Vacuum cleaner. Izi zinali chonchi chifukwa ndinamuuza kuti aziphunzira ntchito asamangokhala. Mosatenga nthawi ndinabwereranso kuchipinda kuja pomwe ndinamuona Salimu atadzuka. Kenako ndinapita kukakhala m'mbali mwa bed uku ndikumufusa.

"Kodi babe , zampingo ukutinazo bwanji?"

"Tamangopitani ku church-ko inu , ikazakwana nthawi ndizakuuza kuti unditsaye ku chipembedzo changa."

"Zomwe zikutanthauza kuti ukwatinso tizapanga mukazayamba kupita ku Nzikiti?"
Ndinafusa chifukwa Salimu amadzitchula kuti Msilamu koma chiyambireni kukhala ndiine sanapondepo khomo la Nzikiti. Ndye nditafusa fuso ili anati:

"Zidzaoneka."

"Babe, tandipatseni yankho logwira ntima . Munthune ndimapita m'maukwati amzanga kupangira kuti nawonso azanditsatire ndikazakhala ndi ukwati wanga."

"Kodi imakhala ngongole?"

"Ndye umaganiza kuti anthu ndizingowafupa ndalama zaulele ? Nawonso akuyenera azandibwezere."

Chifukwa cha pressure yomwe Salimu ndinamupatsa , anavomera zopanga ukwati. Ndipo pamkambirano wathu , tinagwirizana kuti ukwati wathu uzachitikira ku Blantyre mu Multi-purpose hall ku HHI (Henry Henderson Institute) . Izi zinali chonchi chifukwa Blantyre ndipakati pa Mulanje ndi Chikwawa , kotero tinapangira akuchimuna ndi akuchikazi azayende half-half. Titatha kukambirana ndinatuluka kuchipinda kuja kupita pa sitting room komwe ndinamupezanso Thandie akungoyendayenda atavala bathing towel yomweyija. Kenako ndinamufusa.

"Kodi ukufuna ukasambe?"

"Ayi."

"Tsono kungovala bathing towel m'mawa uno zovala zatani?"

"Palibe."

"Tapita ukavale zovala uko . Usiyanitse moyo omwe timakhala akazi okhaokha uja ukumva?
Mnyumba muno muli bambo ako ndi brother wako, ndiye zomayenda utavala bathing towel yokha zilekeke."

Ndinamulankhula ndili okwiya. Kenako anati:

"Iiiiiiii koma amayi Masiku ano mwayamba kuvuta mwamva?."

Anatero akuzithyolathyola monyanyala uku akulowa ku chipinda chake. Ndinamutsatira kuchipinda chake komko.

"Tapitani mukasambe tizipita ku Church."

"Lero sindipita ndikufuna ndiziwerenga notes pajatu Lachiwiri tikuyamba mayeso."

Atayankhula izi sindinamukakamile podziwa kuti ali class ya mayeso a JCE. Nthawi yomweyo ndinabwerera kuchipinda changa kukasamba chifukwa inali ndi bathroom komweko. Nditamaliza kusamba ndinavala zovala zaku church. Pomwe ndimatuluka mchipinda muja , Salimu-nso anatulukanawo chifukwa amapita kokagulitsa drum ๐Ÿ›ข๏ธ la Ethanol. Titatuluka panja ndinamupeza David ali ndi amzake awiri akucheza kwinaku horse pipe ili m'manja mwake akuthilira maluwa. Mosataya nthawi Salimu analiza galimoto yake kumapita. Inenso ndi wantchito tinakwera galimoto yanga kumapita ku church kuwasiya David ndi amzake panja komanso Thandie mnyumba akuwerenga notes.

----

Ma week awiri anadutsa , pa nthawi imeneyi Thandie anali ali pa holiday akudikira zotsatila zamayeso a form 2, pamene David amakomzekera zokalemba mayeso ake a MSCE. Panthawi imeneyi ndinayamba kumuona Thandie akumamuchitira manyazi David akayang'anizana olo akamayankhulana . Izi sindinakhalenazo odabwa poganiza kuti mwana wamkazi amakhala wamanyazi akafika adolescent stage .

Masiku anapanga week , pakhomo palibe chisokonezo chilichonse . Koma chomwe chimandinyasa ndichokuti: Kumpanda kumabwera anyamata awiri amzake a David ndye pomwe pali Davie , Thandie amakhala pambali pakepo kumacheza. Izi zimandinyasa muntima ndipo ndinamuyitana Thandie alimkati mocheza.

"Tha.. Thandie!!!"

"Yes , mom."
Anatero akuyimilira pomwe anakhala paja kulowa mnyumba . Atafika ndinamufusa.

"Ukutani panjapo?"

"Tikucheza."

"Ukutani mwana wamkazi pagulu la anyamata? Mukucheza nkhani zanji?"

"Akukamba zaku school kwawo."

"Ok chabwino kucheza kwathera p***a . Pakadali pano upite ku kitchen Anambe(Nanny )akukufuna."

Ndinatero cholinga akakhale busy ndi wantchito ku kitchen. Kenako ndinamuyitana David.

"Davie!! David"

"Yes mom."

"Tabwerani achimwene."

Atabwera ndinati:

"Sindikufuna mzako wina aliyense azilowa kumpanda kuno . Mukafuna kucheza iweyo uziwayendera kwawo komko koma usamamutenge Thandie popita kumeneko."

"Ok mom"

"Yeah ndipo uwauze azimzakowo azipita p***ano."

"Ok mom."

Ndinayankhula mokupsa ntima poganiza kuti mwina m'modzi wa mnyamatayo ndichibwezi cha Thandie ndipo David amamugwiritsa ntchito ngati mtumiki otumikira . Amabwera kunyumba yanga ngati akuzacheza ndi David koma akuzembera mwana wanga. Ndinapanga izi chifukwa masiku amenewa ndinamuona kuti Thandie wayera m'maso kwambiri, ndye ndinawathamangitsa anyamata aja poopa kuti angamupatse mimba mwana wanga chifukwa anali Namwali osayamba wa packet ndipo period yake ndimayitsatila mwezi ndi mwezi......................



Tikumanenso mu part 5


Mary akuteteza mwana wake kuthamangitsa anyamata omwe sizikuwakhudza hhhhmmm azakhumudwa ๐Ÿ™Œ๐Ÿ™Œ ๐Ÿ™Œ


Mary akuyesera kuongola mtengo utakulakale, koma bola mtengowo usatchoke . ----Lero ndalephera kuponya nkhani coz magobo...
14/06/2026

Mary akuyesera kuongola mtengo utakulakale, koma bola mtengowo usatchoke .

----

Lero ndalephera kuponya nkhani coz magobo anakula nsinkhu. Tionane mawa usiku wabwino. ๐Ÿ™ˆ

SHE'S NOT MY SISTER _______________________PART 3________Written by Fukiz mw _____________________David ndi Thandie anay...
13/06/2026

SHE'S NOT MY SISTER
_______________________


PART 3
________


Written by Fukiz mw
_____________________

David ndi Thandie anayang'anizana kwakanthawi chifukwa aka kanali koyamba kuonana chiyambireni ubwezi wa ine ndi Salimu. Sindikudziwa kuti m'mutu mwawo mumayenda chani koma amene amayang'ana mzake kwambiri anali Thandie. David anatuluka mgalimoto kungoyima chete mudziwa munthu ukafika kuchilendo umakhala omangika. Kenako ndinamuona Thandie akupita mbali yomwe kunali Salimu . Salimu anatuluka atanyamula Doritos chifukwa anamuzoloweza Thandie kuti tsiku lililonse lomwe amabwera, amamupatsa Doritos. Mosataya nthawi ndinawaona atatengana kubwera pakhonde nkhani zawo zilipakamwa . Kenako tinalowa mnyumba ndikukakhala m'mipando koma Salimu anapitilira mu Fridge kukatenga drink ndima glas๐Ÿท 4 . Braai chicken ndikusiya m'mbale . Kenako anatenga botolo la chakumwa ndikuthila glass iliyonse . Mosatenga nthawi anayamba kuyankhula.

"Pomwe takhala chonchimu ndife banja limodzi , kotero tizikhala okondana. Koma podziwa kuti pomwe pali anthu awiri, atatu sipalephera mapokoso , tiziyezetsa kukhala ololerana ndikugonjerana. Pakapezeka vuto tizikambilana mwachangu. Uthengawu ukupita kwa inu awiri."

Anatero akuloza David ndi Thandie. Kenako anapitiliza kulankhula.

"Kuyambira lero ndinupachibale chifukwa chamgwirizano wabanja omwe tinapanga makolo anufe. Kotero iwe David ukamamuona uyu ndi sister wako ndati ndindani? "

"Sister wanga."
Anatero David pobwereza zomwe ananena bambo ake. Kenako anatembenukiranso kwa Thandie .

"Thandie, uyu ndi brother wako, ndati ndindani? "

"Brother wanga."

Kenako anatembenukira kwaine ndipo anati:

"Babe, ife ndye mitu ya banjali , zomwe tizipanga ife anawanso azitengera zomwezo . Love my child and I will love yours too."

Atayankhula mau awa anandipatsa kiss patsaya kenako anati:

"Tiyeni timwere."

Aliyense anatenga glass ๐Ÿท lake ndikupangana Cheers ๐Ÿฅ‚ ndi mzake ndikuyamba kumwa.
Kubwera kwa Salimu pakhomo panga , anandichepetsera ntchito yomakamusiya Thandie ku school. Izi zinali chonchi chifukwa Thandie amaphunzira pa St Lawrence Girls Catholic secondary school pa Dyeratu . Koma sindinafune kuti azigonera komweko (boarding )pamene David amaphunzira pa Chikwawa Secondary school. Ndye Salimu akamapita kuntchito amanyamula ana onse kukawatula m'ma school kenako iye amapita ku ntchito kwake ku Press cane limited.

----

Masiku anapanga sabata limodzi , pa week yomwe tinakhalayi , ndinapanga note kuti David ndi Thandie panali kusagwirizana . Sindikudziwa kuti ndichifukwa chani amadana. Koma mukafukufuku wanga ndimaona kuti Thandie ndamene amayambitsa mapokoso koma David samabweza chipongwe chifukwa chakudzimva chilendo mnyumbamo.

Unali usiku wa Lachisanu nthawi imeneyo Salimu alikubafa akusamba. Ndinatenga phone yake kuyamba kuona ma messages ku WhatsApp ndicholinga chokuti ndigwire ndekha. Kenako ndinayamba kuona message ina iliyonse yomwe amacheza ndi anthu tsiku limenero. Kenako ndinalowa chat cha David . Nditalowa ndinapeza message yomwe David anawatumizila bambo ake koma iwo sanayiyankhe . Message-yo inali yokuti:

"Adad , zikomo kwambiri ponditengera mnyumba ino kuti ndizizakhalananu, koma ndisakunamizeni mnyumba muno ndikukhala momangika . Chilichonse chomwe ndingagwire mnyumba muno Thandie akumandilankhula udyo akuti sizikundikhudza . Ndye ndimaona kuti bwanji mutandipangira self boarding ndizikakhala kufipi ndi school . Pa holiday ndizikakhala ndi Agogo kwa Mgabu? "

Message-yi inaonetsa kuti Salimu wangoyiwerenga koma sanayiyankhe . Nditamva izi moyo unandipweteka kwambiri. Kenako ndinamumva Salimu akubwera, mosataya nthawi ndinasiya phone pomwe anayika paja ndikungokhala phee . Atalowa tinacheza pang'ono kenako ndinatuluka kuchipinda kuja kukalowa kuchipinda cha wantchito wathu . Ndinafika momudekhera ndikumufusa mwachifatse zokhudza David ndi Thandie m'mene akukhalira. Iye anandiuza mosandibisila kuti Thandie ndi trouble maker. Kenako ndinanyamuka kukalowa kuchipinda cha Thandie. Ndinamupeza aliphee kuwerenga mabukhu aku school . Ndinatseka chitseko ndikuyima pachitseko p***aja kumangomuyang'ana. Izi zinamupangitsa kundifusa .

"Mom, bwanji mukundiyang'ana chincho?"

"Thandie, ukufuna ine ndi adad ako tiziyambana eti?"

"Ayi , bwanji? Ndatani ama?"
Anatero akusiya ma bunkhu ake aja ndikundiyang'ana.

"Ndi David mukukhalitsana bwanji pakhomo pano ? "

"Tikukhalitsana bwinobwi...."

"Chokaa!! Kodi ukufuna uzizitenga ngati Queen mnyumba muno eti?
Zomamamuletsa David kuti asamagwiritse zinthu mnyumba muno zayamba liti?"
Ndinayankhula pang'ono pang'ono kuti wina aliyense asatimvere.

"Iiiii koma David ndiwabodza ine....

"Iwe iwe iwe "
Ndinatero ndikukumuloza chala changa pa mphuno yake. Kenako ndinati:

"Ndiye undimvetsere bwinobwino. Chilichonse chomwe chili nyumba muno ndichaine ndi adad ako . Iwe ndi David muzingogwiritsa ntchito nonse koma sizanu ayi ukundimvetsetsa. Ngati ukufuna kutenga ulamuliro , nawenso uphunzire, uyambe ntchito uzagule katundu wako ."

Nditayankhula mau awa, Thandie anaoneka okhumudwa ndipo anati:

"Ama , chibwerereni David mnyumba muno mwasiya kundikonda chifukwa chani?"

"Ine ndimakukonda koma please usapangitse kuti ine ndi adad ako tiyambane ukundimva? Ndikangomvanso kuti izi zikupitilira Thandie ndizakupweteka. "

Nditayankhula izi ndinatuluka mchipinda muja kupita kuchipinda changa. Nditafika kuchipinda changa Salimu anandifusa .

"Unalikuti babe?"

"Ndinali kuchipinda cha Thandie ndimamuthandiza homework."
Nditayankhula mau awa tinayamba kucheza nkhani zathu mpaka tinagona.

M'mawa wa loweluka kutacha tonse tinadya chakudya cha m'mawa . Kenako ine ndi Salimu tinachoka pakhomo paja kupita ku Bangula kokagulitsa Ethanol yemwe Salimu anatenga kuntchito kwawo ndye ine ndinamuperekeza chifukwa Loweluka sindimagwira ntchito. Pakhomo panatsala wantchito ndi ana awiri aja. Tinayenda kukafika ku Bangula komwe tinakasiya drum ๐Ÿ›ข๏ธ imodzi ya Ethanol. Mosataya nthawi ndinaona anyamata atayamba kusungunuka Ethanol uja ndimadzi. Akamusungula anandiyika m'mabotolo ndikuwathila flavour yomwe kuti anthu azimwa . Ndisanafike ndinaona anthu ena akubwera kumazapikula . Izi zinandidabwitsa mpaka ndinamufusa Salimu.

"Babe, anthu amamwa Ethanol-yu."

"Ndi business yotentha imeneyi ndipo umaphula (umalemera) mwachangu koma vuto ndiyosaloledwa ndi boma chifukwa mowa umenewu timautcha Ambuyemtengeni."

"Ambuyemtengeni uja ndameneyu?"

"Yeah"

"Kodi asilamunso amakulolani muzigulitsa mowa?"

"Mary mafuso athera p***a basi, tiyeni tidzipita kunyumba."

Atayankhula mau awa tinakwera galimoto kumabwerera kunyumba . Tinayenda ndikufusa nkhani za ethanol zija mpaka tinakafika kunyumba. Titafika pa gate ndinatsika ndikukatsekula gate . Koma ndili mkati mokankha gate ndinamva kulankhula mnyumba koma mosonyeza kukalipa. Ndinasiya gate ija kupita kukayima pakhonde pomwe ndinamva mau a Thandie .

"Ala ukufuna ndizikhala omangika nyumba yamayi anga? Iwe osamapita kwa mayi ako bwanji? "

Mau awa anandiwawa muntima, nthawi yomweyo ndinalowa mnyumba mwachangu Salimu asanatsike galimoto. Thandie atandiona kuti ndalowa , anayenda chothawa ndikukalowa kuchipinda chake . Asaloke chitseko ndinamulowera komko ndikuyamba kumugunguta.

"Umamva iwe ? Umamva iwe? "
Ndinatero ndikumumenya

"Basi ndasiya amayi. Basi sindizayambiranso."

Nditamaliza kum'menya ndinatuluka kuchipinda kuja . Nditatuluka ndinangoti gululu ndi Salimu ma key agalimoto alim'manja . Mosataya nthawi anandifusa.

"Babe phuma limeneli bwanji?"

"Palibe."

"Tsono Thandie akulira chani?"

"Thandie masiku ano akuyankhula mopepera."

"Amati chani?"

Ndinamangika kuti ndiwatulutse mau omwe anayankhula aja kenako ndinangomudekhetsa koma ntima ukundipweteka ndizomwe amachita Thandie.

Patatha masiku awiri ndinawaona ana aja atayamba kutolerana pang'ono pang'ono . Ndikamabwera kuntchito ndimawapeza pampando akucheza . Tsiku lina David anatenga galimoto yanga kutengana ndi Thandie kupita pa kalulu stadium kumakaonela Mpira limodzi . Thandie anasiya kundipeza kuti ndimuthandize Homework, m'malo mwake amapita kuchipinda cha David ndikumaphuzitsana. Apa umoyo wanga unayamba kumva kukoma polingalira kuti ana anga ayamba kumvana . ..............


Tikumanenso mu part 4


FUKIZ MW

Address

Blantyre
2022

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when FUKIZ MW posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share