30/06/2024
Zinathera mwa agogo a mphini ndi okondedwa awo pa ndalema.Adanka nazo zija zomati kukacha zidzukulu zapeza kale ndowe za mbuzi kapena ng'ombe zanyeka kale.Mmenemotu mkoko wogona utachita kale dongosolo m'banda kucha.Mbuluwuli zikuyanja phulusa, zisanadziwe kudzola mafuta.Zimvekere patali 'ngandee' kununkhira.Kamphepo katanyamula uthenga kupititsa kwa mdzukulu wa a Ngozo,"Tchukumiza gogo wako kwa a Nzanani zayamba kuthulika."
Mwezi uwale akakanika chifukwa chosowa mwezi,kunalibe kusungulumwa.Iyi ndiyo nthawi imene mdzukulu amakadzipapatiza kwa gogo wake kukasaka tulo kudzera m'kumvetsera nthano ndi nkhani zosiyanasiyana.Akamafotokoza kumakhala ngati ukuonera kanema.Ngakhale kanemayo anali asanafalikire kwenikweni koma kukhala ndi gogo kumakwanira pa kanema.Mdzukulu aliyense khutu lake limakhala lili tcheru kuopa ukandimverere.
Naye mdzukulu wa mtauni akumaona tchuthi kuchedwa kuti akacheze ndi gogo wake kumudzi.Chikoka chinalipo ndithu mu nyengo izo moti mikoko yogona imakhala pa ulemerero polandira ana kuchoka mphepo zonse zinayi,sukulu zikatsekeredwa.
Nanga Kodi zimenezi zinatha?Ngati sizinathe,chimene chinabweza m'mbuyo ubale umenewu nchiyani?Yankho pa nkhani imeneyi ndiloti,sizinathe.Chilungamo nchoti mikoko yogona Ina inabwerera m'mbuyo chifukwa cha mantha.Mantha anabwera chifukwa chokhala iwo zikwangwani za uthakati.Munthu aliyense amene wakalamba amatengedwa ngati walandira kalata zomuyenereza ufiti.Wina akangoti,"gogo uyu ndi mfiti."Pamenepo basi zavuta.
Moto umene ankasonkhera zidzukulu uja pano ukumasonkhedwa ndikuponyapo nkhalamba.Sizotinso paikidwe chimanga kapena mbatata ayi.Nkhalamba kungolakwitsa mayankhulidwe,basi imeneyi ilandira maduka.Poona izi,achikulire ambiri anabwezeretsa phala kunkobwe.
Nanga Kodi nkhalamba iliyonse ndi mfiti?Apapa yankho lake adzalipeza aliyense payekha akadzakalamba.Chachikulu tingopempha ngati alipodi ena amene amachitadi izi,kuzileka ndibwino.Inde;tisapweteketse achete.
Kwa achinyamata tonse tidziwitsane kuti tikamanena chingerezi choti 'Happy Birthday' ndiye kuti pang'onopang'ono tikukalamba.Chichewa chimanenetsa kuti chaona mnzako chapita mawa chili kwa iwe.Idzafika nthawi yoti mano akukana kukhala mkamwa,tsitsi nalonso layamba kusuluka.Pamenepa mpamene mudzadane ndi mtengo wokuzungulirani kuopa ungadzakhale nkhuni za ufiti wanu.
Tsono popeza nkhani nkamnyamata pano tingochepetsapo gaga mdiwa.Nkhani ili pano ndi yokhudza munthu amene sitimutchula dzina lake lenileni.Munthu ameneyu anayamba kumalondolalondola anthu awiri amenenso maina awo enieni sitiwatchulanso pano.Mosafuna kupolokeza zinthu,tatiyeni tingowadziwa anthu olondoledwawa ndi maina awa:
Gogo:Nachilongo
Mdzukulu:Zipewe
Nayonso mphongo yowalondolayi tiyeni tiidziwe ndi dzina lachingerezi loti 'Follower' kapena osavutikanso ndi zambiri koma kungoti 'Folowa'
Maina tabisa dala ndicholinga choteteza chifukwa mukawadziwa Gogowa,mwina atha kuona mbonaona takamba kale zija.Nayenso Folowa akadziwika,mukayamba kumuulula zowalondolazi mapeto ake sitimva nawo zambiri.Kulondola kwa munthu ameneyu sikwachindunji.
Gogo Nachilongo amenenso mudzi wawo sitiutchula,amagwirizana kwambiri ndi mdzukulu wawo wamkazi,Zipewe .Izitu zimachitika ngakhale a Nachilongo Ali ndi zidzukulu zina.Akakhala ndi enawo samakamba zochuluka koma akakhala poduka mphepo ndi Zipewe kumakhala akumamukambira nthano ndi nkhani zosiyanasiyana.Apapa mongopenekera titha kungonena kuti nawonso amakhala ndi mantha monga ndi mmene talongosolera pachiyambi.
Tsono mwa chikhadzakhadza,Folowa anakumanizana nawo.Iye anasirira nakhala ndi chikumbumtima cha agogo ake onse omwe anapita kulichete.Iye amayetsetsa kuwalondo kulikonse ndipo amasunga mawu awo mwa chinsisi.Awiriwa samadziwa za izi chifukwa akadangodziwa,unali mulandu.
Ine ndinapempha kwa Folowa kumva nawo nkhanizi ndipo inu mukakonda muzimva kuchokera kwa ine T.A.Chisale.
Media