25/05/2023
KAJOKE ALAMULIDWA KUBWEZA NDALAMA KU MA BANKER
Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo mdziko muno la Football Association of Malawi (FAM) lagamula kuti katswiri osewera kutsogolo kwa timu ya Nyasa Big Bullets Hassan Kajoke abweze ndalama zokwana 3.9 million kwacha ku timu ya Silver Strikers.
Malingana ndi chigamulochi, katswiriyu akuyenera kuchita izi pasanathe masiku asanu ndipo kuti kupanda kutero ndalamayi adzaipereka ndi chiongola dzanja.
Bungweli latinso Kajoke sakuyenera kusewera masewero aliwonse kuno pokhapokha atabweza ndalamayi komanso ina yomwe adapatsidwa ngati malipiro ake a January ndi February ku ma bankers.
Kumbali ina, ma bankers awapezaso olakwa posatsata malamulo ndipo agamulidwa kupereka ndalama yokwana 900 000.
Omuyimilira Kajoke , Ken Mvula nayeso akuyenera kupereka 500 000 atapezekanso olakwa pa nkhaniyi, ndalamazi malingana ndi FAM, zikuyenera kuperekedwa pasanathe masiku asanuso.
Pomaliza chigamulochi chati yemwe sakukhutira ndi izi atha kumang'ala kuti chiwunikidweso, koma akuyenera kugwapo ndi dipo lokwana 800 000.
Wolemba: Brenda kamowa