07/09/2026
Copied #
"Nkhuyu zodya ana zipota akulu"🙆♀️😭
Headmaster wa Kathyuka primary school ,TA Simphasi ku Mchinji waopseza k*t school sitsekulidwa term ikubweray ngat sapatsidwa ndalama zake za chipepeso zomwe ndipafupi fupi K300 000.
Nkhan yi ik*t mwana wa Headmaster a sukuluyi amayendetsa ngolo..ndye mudziwa inu poyendetsa ngolo kumakhala kukuwilira.,koma tu izi sizinasangalatse a2 ena ammudzi kuphatikizapo a group a Kathyuka, ati ponena k*t amakhala ngat akuyeserera Gule wamkulu, chosecho ali osavinidwa/osameta.
Zitatero, a group a Kathyuka anaitanitsa akulu akulu aku Madzi k*t amugwire mnyamatayu ndikumpitisa ku Dambwe k*t akumuphuzitse chikhalidwe.
Mwa " chimvano cha mamvu" akulu akulu akumadzi anasonkhanitsa namtindi wazilombo zotchedwa KAMANO ndipo zinazungulira nyumba ya m'phuzitsi wamkulu pa school, Komatu pa nthawi yi mk*t mwana atamutsina kale Khutu a2 ena k*t Paipa pano, Madzi achita Katondo, ndipo sanazengereze koma anati Phazi thandize ndipo analiyatsa liwiro la Mtondo wa Dowoka 🏃♀️ 🏃♀️
Apatu mwanayu anaponda njoka kunchira, ndipo zilombo zinalusa ndikuyamba kupha nkhuku za Headmaster ndipo atambala a nkhongono okwana 7 sizinayendere pa tsikuli😭
Gule wankulu sanalekere pomwepa anagwira a headmaster ndikuwakwapula ija amat STONES ali mdothi, adzuke kick ngat ija ya VAN DAMME, apatu kunali k*tikita kuyiwala k*t mu2 yi adapta ku KOLEJI🙆♀️
Mwa mwayi m'phuzits wina ndi amene anapulumutsa m'phuzits mzawoyu.
Nkhan itapita ku polis ya Kamwendo a group a kathyuka inawathina kwambiri, ndipo anawapeza olakwa, ati poitanitsa zilombo ndikubweretsa chisokonezo pa malo a school, komanso kuika chiopsezo moyo wa munthu, ndipo agemulidwa k*t alipire ndalama yokwana K 280 000 popha nkhuku komaso kumenya mphuzitsi yu.
Tsiku lothera kulipira ndalamayi ndi Lolemba likudzali, ndipo m'phuzits wopandidwa yu waopseza k*t ngat sapatsidwa ndalama auza aphuzits onse k*t asatsekulire school yo popeza moyo wawo uli pa chiwoosezo.
Timve maganizo anu kodi wolakwa ndani?
COPIED