The Giraffe Malawi Online News

The Giraffe Malawi Online News Get the latest Local and International news updates. News concerning Politics, sports, Health etc

 Mu chaka Cha 2025, dziko la Malawi lichititsa chisankho chapatatu pofuna kusankha atsogoleri ena atsopano. Ngati mbali ...
03/02/2024



Mu chaka Cha 2025, dziko la Malawi lichititsa chisankho chapatatu pofuna kusankha atsogoleri ena atsopano. Ngati mbali imodzi yokonzekera chisankhochi, zipani zochuluka zili pakalikiliki kuchititsa misonkhano m'madera osiyanasiyana m'dziko lino.

Koma funso n'kumati, kodi chiyembekezo cha a Malawi chili m'chipani chiti kuti masomphenya a Malawi 2063 awoneke tsogolo lake makamaka poonetsetsa kuti Malawi akhale okomera wina aliyense?

Ichi ndi chifukwa chake Giraffe ikufuna kumva maganizo anu kuti ngati a Malawi, chiyembekezo chanu chagona m'chipani chiti? N'chifukwa ninji mkuganiza kuti chipanicho chikhoza kuthandiza kutukula dziko la Malawi pa chuma kuti masomphenya a Malawi 2063 adzatheke?

kutsatira ndi kukonda tsamba lathu la Giraffe pa Facebook (Like and follow) #

Zithunzi: MEC

 Education expert, Benedicto Kondowe says the growing trend of university students facing expulsion for cheating is worr...
30/01/2024



Education expert, Benedicto Kondowe says the growing trend of university students facing expulsion for cheating is worrisome.

This follows the expulsion of 3 students and suspension of other 14 students from Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) for cheating.

Kondowe has told Giraffe that the situation is however not necessarily a reflection of students' incompetence but could indicate issues within education sector.

He said: "Some of the contributing factors to this could be academic pressure, inadequate support and lack of emphasis on ethics."

However, Kondowe has advised universities to enhance academic integrity measures and foster the value of ethics to tackle these challenges collectively to ensure the quality of education and the credibility of graduates.

In October, 2023 University of Malawi (Unima) also expelled five students on the the same misconduct.

By Lumbani Kazeze

Photo: Csec

 Chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive Party (DPP)  chadzudzula anthu omwe akuti ndi otsatira a     Kondwani...
30/01/2024



Chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive Party (DPP) chadzudzula anthu omwe akuti ndi otsatira a Kondwani Nankhumwa kamba kotentha zovala za makaka a chipanichi ku Ndirande mu mzinda wa Blantyre.

Malinga ndi kalata yomwe Giraffe yapeza imene asindikiza ndi mneneri wa chipanichi, a Shadric Namalomba, iwo akuganiza kuti anthuwa anatentha katunduyu poonetsa kusakondwa ndu kuchotedwa kwa a Nankhumwa mu chipanichi.

A Namalomba atinso, mchitidwewu ndi wamakedzana ndipo zaonetsa kulephera kwa anthuwa kuthandiza dziko lino kuti lituluke mu nsinga za mavuto a chuma omwe lili nawo mwa zina.

Wolemba: Brenda Pensulo

 Teachers Union of Malawi (Tum)has introduced an annual licence fee of K40, 000 to its members amidst unresolved  K500  ...
23/01/2024



Teachers Union of Malawi (Tum)has introduced an annual licence fee of K40, 000 to its members amidst unresolved K500 monthly fee issue.

According to the new fee, both full-time and auxiliary teachers will be subjected to the same annual deduction, an issue that has brought a mixed reaction among teachers across the country.

some teachers have argued that nurses are subjected to only K18,000 annually while Tum has decided to heavily wound them ina already staggering economy.

Teachers have for long complained of how their mother body (Tum) has conducted itself when it comes to matters of their welfare despite being deducted a monthly fee of K500 initially.

By Evans Gondwe

 "Mpandeni galuyo kuti mudziwe mbuye wake"Uwu ndi mkuluwiko omwe ambiri m'masamba amchezo akuninkhana. Izi zikutsatira c...
22/01/2024



"Mpandeni galuyo kuti mudziwe mbuye wake"

Uwu ndi mkuluwiko omwe ambiri m'masamba amchezo akuninkhana.

Izi zikutsatira chikalata chomwe chipani cholamula boma cha Malawi Congress Party (MCP) chatulutsa dzulo choonetsa kukhumudwa kwawo kamba kakuchotsedwa m'chipani kwa akuluakulu ena monga a Kondwani Nankhumwa, Kenneth Msonda komanso Grezelder Jeffrey.

Kodi mkuluwikowu ungakhale owona? Giraffe ikufuna kumva kuchokera kwa inu kuti ipeze chomwe chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke nyanga.

Kumbukirani kutsatira ndi kukonda (Like & follow) tsamba lathu la mchezo la Giraffe pa Facebook.

 M'modzi wa akuluakulu a chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) omwe anachotsedwa mchipanichi, a Kenneth Msonda ...
22/01/2024



M'modzi wa akuluakulu a chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) omwe anachotsedwa mchipanichi, a Kenneth Msonda ati alibe malingaliro osintha chipani kamba koti amene awachotsa mchipanichi siphata la chipanichi.

A Msonda ati pomwe iwo ndi anthu ena monga malemu Bingu Wamtharika, a Uladi M***a, Joyce Banda, Patricia Kaliyati ndi a Zikhale Ng'oma amayambitsa chipanichi, gulu lawachotsa m'chipanichili kunalibe.

"Palibe kusintha chipani. Mudzi sitisiyira alendo obwera. Pamene timayamba chipanichi, omwe atichotsa mchipaniwo anali kunja kwa dziko lino pomwe ena anali ali ku bungwe la EGENCO kuba ma units a magetsi," atero a Msonda.

Izi zadza tsiku limodzi a Msonda atalengezanso kuti kukhala kuthana mu chipanichi, iwo atachotsedwa mchipanichi pamodzi ndi akuluakulu ena.

Wolemba-Lumbani Kazeze

 Self claimed South African based Human Rights activist Ben Longwe has claimed that Billy Malata was arrested to conceal...
21/01/2024



Self claimed South African based Human Rights activist Ben Longwe has claimed that Billy Malata was arrested to conceal the evudence on who sponsored him to obtain a court injunction against Peter Mutharika to contest in 2025 elections.

In an audio circulating on social media platforms, Longwe however, says Malata did not expose people but threatened to reveal their identities by holding a press brief if the perpetrators would not settle his payment balance.

"The involvement of the state in arresting Malata and keep him at Maula prison is questionable. This is so because we are suspecting that government took part in sponsoring DPP in fighting so that the party go to 2025 elections without candidates," he said.

Meanwhile, the activist has assured the courts that he will be a witness in the case so that Malata is served with justice.

The former DPP member was apprehended on 13th January, 2024 charged with defamation against Mutharika and his followers.

By Evans Gondwe

 Malawi's prolific striker, Tabitha Chawinga has netted twice to help PSG collect maximum points, thrashing the 12th ran...
20/01/2024



Malawi's prolific striker, Tabitha Chawinga has netted twice to help PSG collect maximum points, thrashing the 12th ranked, Boardeaux 8 goals to 1.

Chawinga's brace takes her tally to 7 goals in the league and 9 in all competitions since she joined the French powerhouse in 2023.

This Victory means PSG are ranked second trailing the leaders Lyon Fc with 5 points.

Reported by Evans Gondwe-Mzuzu

 Chipani cha DPP kudzera mkalata yomwe wasindikiza ndi mneneri wamtsogoleri wachipanichi a Shadrick Namalomba, chachotsa...
20/01/2024



Chipani cha DPP kudzera mkalata yomwe wasindikiza ndi mneneri wamtsogoleri wachipanichi a Shadrick Namalomba, chachotsa mamembala odziwika bwino mchipanichi monga a Kondwani Nankhumwa, Glezelder Jeffrey, Ken Msonda, Nicholas Dausi komanso a Cecilia Chazama.

Perekani maganizo anu pa ganizo lomwe chipanichi chapanga. Mkuganiza kuti chiganizochi ndichanzeru pomwe akuluakulu a chipanichi ali pakalikiliki kofuna kukonzanso chipanichi? Nanga otchotsedwawo mungawalangize zotani?

Giraffe ikufuna imve maganizo anu pankhaniyi.

Kumbukirani kutsatira tsamba lathu la Giraffe.

 Namondwe DPP-2024Chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) chachotsa a Kondwani Nankhumwa yemwe anali wachiwiri kw...
20/01/2024


Namondwe DPP-2024

Chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) chachotsa a Kondwani Nankhumwa yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi kuchigawo chakumwera asanachotsedwe kukhala mlangizi wa mtsogoleri wachipanichi mu Disembala chaka chatha.

Enanso omwe achotsedwa mchipanichi ndi a Cecilia Chazama omwe anali mlangizi wa mtsogoleri wachipanichi, a Grelzeder Jeffrey omwe anali mlembi wamkulu wachipanichi, a Nicholas Dausi, Joe Nyirongo, a Kenneth Msonda komanso a Mark Botomani.

Mwa ena, a Ralph Jooma awachotsa pa udindo wawo oyang'anira zachuma mchipanichi ku komiti yaikulu pomwe a Uladi M***a amayimitsa kutenganawo mbali mchipanichi kwa miyezi isanu ndi inayi(9).

Chipani cha DPP chakhala chisakugwirizana pankhani ya utsogoleri wachipanichi chichokereni m'boma chaka cha 2020.

Wolemba-Lumbani Kazeze

 Mkulu wa kampani ya TNM yomwe imathandiza mpikisano wa Super League, a Michel Hebert ati awonjezera ndalama yolimbirana...
19/01/2024



Mkulu wa kampani ya TNM yomwe imathandiza mpikisano wa Super League, a Michel Hebert ati awonjezera ndalama yolimbirana matimu kuchoka pa 150 million kwacha kufika pa 450 million kwacha pa chaka.

Iwo alengeza izi madzulo a lero lachisanu kumwambo wopereka mphoto kwa osewera, aphunzitsi, olemba nkhani komanso osanthula masewero omwe achita bwino mchaka cha 2024 ku Mount Soche Hotel m'mzinda wa Blantyre.

"Chaka cha 2024 chikhala chapamwamba chifukwa tiwonjezera ndalama zampikisanowu ndi katatu. Tikufunanso kuti ziphaso zolowera kumpira zonse zidzidzagulidwiratu pa mpamba tsiku la masewero lisanafike," atero a Hebert.

Mwa zina alonjezanso kuti kampaniyi ifikiranso madera akumudzi ndi thandizo la chuma kuti athe kufukula luso lobisika ndocholinga chotukula moira m'dziko lino.

Mpikisano wamchaka cha 2024 ukuyembekezereka kuyamba mu mwezi wa April.

Wolemba-Lumbani Kazeze

 Patrick Mwaungulu wakhala katswiri yemwe wadoda mpira mwapamwamba kuposa onse mchaka cha 2023.Umu ndi momwe zayendera m...
19/01/2024



Patrick Mwaungulu wakhala katswiri yemwe wadoda mpira mwapamwamba kuposa onse mchaka cha 2023.

Umu ndi momwe zayendera malingana ndi mphoto zina zomwe osewera mpira,olemba nkhani komanso osanthula nkhani achitira mchaka changothachi. Ndipo opambana onse atenga chikwama cha ndalama zokwana K300,000 kupatulako magawo ena.

Rookie of the season (Youngest Player)
Robert Gomez Size

Best Goakeeper
Innocent Nyasulu

Goldenboot
Clement Nyondo

Midfielder of the season
Patrick Mwaungulu

Player of the season
Patrick Mwaungulu K2,000,000)

Defender of the season
Stanley Sanudi

Coach of the year
Calisto Pasuwa

Olemba nkhani
Print media
Joy Ndovi

Radio Journalist
Patrick Simango

Television journalis
Hankey Chimtengo

Online Journalist
Anthony Isaish Jr.

Sport Analyst
Garry Chirwa

Best Radio Commentator
Bright Buju Kanyama

Best sport photographer
Bobby Kabango

Most Improved team
Chitipa United (K2,000,000)

Wolemba-Lumbani Kazeze

 Mtsogoleri wa Football Association of Malawi (FAM), a Fleetwood Haiya ati awonetsetsa kuti ndalama zomwe matimu a mu TN...
19/01/2024



Mtsogoleri wa Football Association of Malawi (FAM), a Fleetwood Haiya ati awonetsetsa kuti ndalama zomwe matimu a mu TNM Super League amalimbirana zifike pa 500 miliyoni kwacha chaka chino.

Iwo atsimikiza izi lero madzulo kumwambo opereka mphoto kwa matimu komanso osewera omwe anachita bwino chaka chatha m'mpikisano wa Super League.

A Haiya ati izi zitheka ndithandizo lochokera ku mbali zokhudzidwa zomwe zingafune kutenganawo mbali pofuna kutukula masewerowa.

"Nthawi yatha yoti ndalama zolimbirana zidziperekedwa ngati thandizo. Ndikofunika kuti iwowa nawonso ayambe kupeza phindu," atero a Haiya.

Iwo atinso malingaliro awo ndiwoti mpikisanowu ufike pamulingo wapamwamba kuti timu ya dziko lino ikhalenso ya mphamvu.

A Haiya anasankhidwa pampando wa mtsogoleri wa FAM chaka chatha mwezi wa December.

Wolemba: Lumbani Kazeze

 Katsiwiri oyimba Patience Namadingo watulutsa nyimbo yake yoyamba mchaka cha 2024.Mnyimboyi yomwe waitchula kuti "Aka N...
19/01/2024



Katsiwiri oyimba Patience Namadingo watulutsa nyimbo yake yoyamba mchaka cha 2024.

Mnyimboyi yomwe waitchula kuti "Aka Nkoyamba" Namadingo akupempha Mulungu kuti amustogolere muchina chilichonse popeza alibe experience.

Nyimboyi ikuyamba modekha ndi zida zosakanizidwa mwaluso ndipo zing'wenyeng'wenye zinkuka numakwera pang'ono mpaka kufika pa chi indeinde wa mayimbidwe amapiano.

Mundime yoyamba, akufotokoza kuti sanakhaleko ndi moyo kapena chuma ndipo ndikofunika Mulungu yekha amutsogolere. ayende naye pogona ngakhale podzuka poti alibe experience inailiyonse.

Ndipo vesi yachiwiri akuyamba ndi mafunso monga; kodi alipo anadzipatsa moyo yekha? alipo anayamba wabadwapo kawiri? Ndipo akumapereka mayankho kuti palibe ngakhale m'modzi ndipo aliyense anabadza kamodzi ndipo adzafa kamodzi. Malemba akuti ndi Yesu yekha amene adzabwere kawiri.

Nyimboyi (Audio) yajambulidwa ndi katswiri wa ku Malawi DJ Megi ndipo zithunzi zake zajambulodwira ndi Vinny Visuals ndi Ron C m'dzilo la America.

Nanunso wonerani mwina nkuperekako ndamanga yanu.
https://youtu.be/WzytO-4C0nw?si=oiXxHfzcOlCIKEch

Wolemba: Lumbani Kazeze

 Mafumu ena m'maboma aChilhomwe ati sakugwirizana ndi kukwezedwa ufumu kwa Mfumu yaikulu Kaduya ya ku Phalombe kamba kot...
19/01/2024


Mafumu ena m'maboma aChilhomwe ati sakugwirizana ndi kukwezedwa ufumu kwa Mfumu yaikulu Kaduya ya ku Phalombe kamba koti si mfumu ya Chilhomwe koma m'Mang'anja.

Mafumuwa awuza atolankhani lero lachisanu ku likuli la mfumu Ngongoliwa ku Thyolo kuti boma silinaunikire madando omwe iwo anapereka m'mboyomu okhudza ufumuwu kudzera m'makalata ochuluka omwe akhala akulemba.

Izi zadza patangopita tsiku limodzi president Lazarus Chakwera atakweza udindo a Kaduya kukhala mfumu yaikulu.

Wolemba: Lumbani Kazeze

 Lilongwe District Council has ordered all refugees and asylum seekers who left Dzaleka Refugee Camp to relocate to the ...
19/01/2024


Lilongwe District Council has ordered all refugees and asylum seekers who left Dzaleka Refugee Camp to relocate to the camp.

In a letter signed by Lilongwe District Commissioner, Lawfard Palani, the council says the reasons for their relocation were already made clear by the ministry of Homeland Security.

"We are reminding all the concerned refugees and assylum seekers to go back as per order without having to wait for police and other law enforcement agencies," reads part of the statement.

In May, 2023 Lilongwe District conducted a relocation exercise moving all refugees and asylum seekers from other localities to Dzaleka Camp on security threat grounds.

By Evans Gondwe

 Despite Suspending all international trips in 2023, president Lazarus Chakwera is back to default as he is set to fly o...
18/01/2024



Despite Suspending all international trips in 2023, president Lazarus Chakwera is back to default as he is set to fly out of the country to Kinshasa Democratic Republic of Congo (DRC) tomorrow, 19th January,2024.

Ministry of Foreign Affairs, in a statement says, Chakwera will hold bilateral talks with president-elect Felix Antoine Tshilombo of DRC regarding regional security matters that affect Malawi Defence force troops, currently in the eastern part of the host country on the side lines of the inauguration ceremony of recent elect president Tshilombo.

Chakwera initially suspended all foreign trips, as one way of reducing public expenditure to lessen the economic stress the country is facing.

The trip to Congo means the president has travelled over 40 times on foreign trips since he attained presidency in 2020.

By Evans Gondwe

 Malawi Local Music ace, Katelele Ching'oma has passed on.According to his elder brother, Elvis Ching'oma says Katelele ...
18/01/2024



Malawi Local Music ace, Katelele Ching'oma has passed on.

According to his elder brother, Elvis Ching'oma says Katelele died in the wee hours of today, Thursday at Kamuzu central hospital in Lilongwe after failure to beat liver disease.

Elvis, who was also Katelele's producer says his brother was sent to Kamuzu for medical attention from Dedza where he used to stay.

May his soul rest in peace.

By Evans Gondwe.

Address

Masauko Chipembere High Way
Blantyre

Telephone

+265996968806

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when The Giraffe Malawi Online News posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to The Giraffe Malawi Online News:

Videos

Share