19/07/2025
news๐ฐ๐ฐ๐ฐ๐ฐ
ZACHISONI ๐๐๏ธ
Apolisi ku Dowa amanga a Pemphero Puleti, azaka 24 amene anapha msilikali wa Malawi Defence Force (MDF) Lachiwiri sabata ino.
A Puleti anapha msilikali yu, a Chiswansangu Nyirongo, azaka 30, m'mudzi wa Kalazi, T/A Chiwere m'bomali ndipo amagwira ku Mvera Support Battalion.
Pakati pa usiku, a Puleti anapita kunyumba kwa msilikali yu, ndipo atalowa m'nyumba anamubaya pa mimba ndi chitsulo kenako mk*thawa.
Anzawo akuntchito anawatengera a Nyirongo kuchipatala komwe anamwalira akulandira thandizo.
A Puleti awamanga k*tsatira kafukufuku yemwe apolisi anachita, ndipo akawonekera ku khothi kukayankha mlandu wakupha.