Cardinal Henry

Cardinal Henry Unschooled Social, Political commentator - Activist osalowela nkalasi

20/05/2026

I totally agree.

His opportunity is just a phone call away, from a former President to the current President, and be like, Amangwetu, m***andizeni mnyamata asatuwe patawuni๐Ÿ˜€๐Ÿ˜€ heheheheh

Basitu.

Ife kunja kuno a DPP akutukwana a UDF๐Ÿ˜€๐Ÿ˜€

Its all about standing true to principles and doing it for the people.

Emergency meeting at 3pm.

https://youtu.be/O_qm5jfZpiQ

Podcast Malawi

20/05/2026

What we always echoe on the emergency meeting.

Here is from one who have been in the system and is involved and understands how things work.

Emergency Meeting is coming at 3pm.

https://youtu.be/O_qm5jfZpiQ

Podcast Malawi

14/05/2026

Uthenga opita ku MCP ndi apule awo๐Ÿ˜Ž

Mwina mwaiwala๐Ÿคฃ๐Ÿคฃ๐Ÿคฃ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ

Dziko lanji lopanda ma standards magaye??๐Ÿ™Œ๐Ÿ™ŒAti inu donation ndi donation basi. Osangothokoza bwanji. Chopasidwa amakana?...
12/05/2026

Dziko lanji lopanda ma standards magaye??๐Ÿ™Œ๐Ÿ™Œ

Ati inu donation ndi donation basi. Osangothokoza bwanji. Chopasidwa amakana? Vuto ma values a kuvutika kwa mmanyumba mwathu takulowesa mu system which MUST have standards.

Ngati amwenye awowo agula akoko, mufuna mundiuze kuti a whole Blantyre City Council singagule a proper fire truck? Apopo kuteleko if they had plans to procure a proper fire truck they will pause it, in the name of tapeza kale ina and the money will be used kwina mwinaso misused when that "Heavyduty fire extinguisher" cant even put off fire pa chiwaya cha chips.

All am saying is, our public offices must have standards and we shouldnt accept anything bellow the set standards, period.

Ichi abwezeleni azithimisila ma shop awo mu Limbe mo akamapsa๐Ÿ˜€๐Ÿ˜€๐Ÿ™Œ๐Ÿ™Œ

Wake up Malawi๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ๐Ÿ˜€

Ife sukulu stinaimbe kwenikweni koma timakondwa ndi anthu omwe sukulu anaimba bwino lomwe. Komaso timafuna tikamapasidwa...
12/05/2026

Ife sukulu stinaimbe kwenikweni koma timakondwa ndi anthu omwe sukulu anaimba bwino lomwe.

Komaso timafuna tikamapasidwa informatiom izikhala yokwanila yoti isamapeleke mafuso chifukwa olo tifuse mulibe nthawi yotiyankha.

Abwana a nyuwani a ku Small and Medium Enterprises Development Institute - SMEDI avutisa media officer yemwe amalemba ka profile kawoka. Mwina ataafusa bwana kuti apeleke info anapeleka nde mwana wa media anangopanga copy and paste.๐Ÿ˜€๐Ÿ˜€ nayeso osafusa.

Uthengawu umayenela ukhale wotele:

Kondwani Kachamba is a PhD candidate in Economics (University of Malaysia osangoti Malaysia๐Ÿ˜€ mukangoti Malaysia olo kusakako tikayambila pati?) with muiltiple advanced degrees( apapa amayenela awayale ma Masters wo, ma sukulu omwe anapeleka ma Masters, ndi dzaka zomwe anapanga graduate osangoti MSc in Enterprenuership, Malawi. Aaaaaaa Malawi ndi University??). And a BSc in Business Management (From where? and when๐Ÿ˜€). Ti ma certificate of attendance tinato toti olo administrative assistant osainisa ma attendance sheet amalandila nawo training ikatha was not necessary for such a high office.

Kenako amayenela akunge experience yao ya bwanawa. Ma senior position omwe achita hold and the name of the organizations or companies he has worked for and they could have included even his positions in self owned enterprises highlighting his achievements.

Izizi ndanenazi sindikungonena ayi, go and check how MITC, NOCMA, MERA, MACRA introduced their CEOs/EDs.

Ngati anthuwo alibe maphunzilo koma mwaasankha chifukwa amayankhula mwa nzelu, fine and good. Paja kuno timati sukulu siyofunika mma position bola kusata ngini basi๐Ÿ˜€๐Ÿ˜€๐Ÿšฎ๐Ÿšฎ๐Ÿšฎ, just dont lie to us with incomplete information.

Ndatha ine wanu๐Ÿ˜€

Donation๐Ÿ˜€๐Ÿ˜€๐Ÿ˜€Amwenye ena apeleka donation ku Blantyre City Council ya ka fire truck akaka. Magaye let us be honest, akaka ...
12/05/2026

Donation๐Ÿ˜€๐Ÿ˜€๐Ÿ˜€

Amwenye ena apeleka donation ku Blantyre City Council ya ka fire truck akaka.

Magaye let us be honest, akaka olo mu limbe muja ikupsa bench ya kaunjika, sikafunika kuyenda ma trip atatu kuti moto uthime aka?๐Ÿ˜€๐Ÿ˜€

Ma donation enawa amangotilanda mphamvu zathu ndi ulemu wathu pachabe. Imagine someone controlling you for giving you this๐Ÿ˜€.

Komaso anzathu a ndalama, before donation chonde muzipita kukafusa othandizidwa mavuto awo komaso khumbo lawo lakasovedwe ka mavutowo. I dont think this is what BCC can buy if they are to buy a fire truck.

Let us avoid taking in donations we can easily buy on our own.

Tizitolele a Malawi. ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ

Kodi ife tatumiza ndani ku Msonkhano ofunikawu???  Paja apule sakumayenda ndi ma austerity measures wa. Koma tatumiza nd...
12/05/2026

Kodi ife tatumiza ndani ku Msonkhano ofunikawu???

Paja apule sakumayenda ndi ma austerity measures wa. Koma tatumiza ndani oti atha kukapempha meeting ndi Macron ndikukambilana ma deal anzelu??

Definetely the one organizing Macron's diary will priotize Presidents and give them more time than a Minister representing someone.

Atatipweteke ndi ma Austerity measures๐Ÿ˜ก๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ

The Amaryllis hotel sagaLast week nnakuuzani kuti za hotel zi nnasiya kuzisata chifukwa chilungamo chinakhota kalekale n...
11/05/2026

The Amaryllis hotel saga

Last week nnakuuzani kuti za hotel zi nnasiya kuzisata chifukwa chilungamo chinakhota kalekale nchira ndipo zomwe mukuyembekezela zitha osaoneka.

Facts1: Pension Fund Trust inapeleka 90 billion kwacha as part payment out of total transaction amount of 120 billion kwacha.

Fact 2: There was a withdrawal of 5 billion kwacha from National bank, money related to the same sale.

Allegedly: When Amaryllis Hotel got the money, they used part of the money to pay of ngongole yomwe anatenga ku National bank pomanga hotel. Ngongole iyiyi akhala akuvutika nayo for years. Thanks to pension fund trust๐Ÿ˜€

As it stands, despite Pension Fund having paid 90 billion kwacha, achina Yusuf ndamene akuyendesabe hotel ndipo kulibeko ma signs a transition or hand over.

Nde lekani kuzitaisa nthawi kumasatila olo kumaonela ma inquiry a PAC aja ndipo I regret going to bed at 3 am this other day ati kuonesesa chilungamo chichitike. Mxiiiiiii๐Ÿ˜€๐Ÿ˜€

Anyway byeeeee. Week ya welo amalawi anzanga๐Ÿ˜€๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ

SALE SALE SALE6 of these bikes are up for sale. These are JH125LInspired by the Honda XL bike.Sizotiso hit my inbox for ...
09/05/2026

SALE SALE SALE

6 of these bikes are up for sale.

These are JH125L

Inspired by the Honda XL bike.

Sizotiso hit my inbox for pricing ayi,

Imozi ikupita pa MK3,500,000 mukafuna kutenga zonse mtengo wake ugwaso koooopsa, mupezeka mwatenga zonse pa MK19,500,000 mmalo mwa MK21,000,000.

Serious buyers only๐Ÿ˜Ž๐Ÿ˜Ž

Talk to me on +265881927707 - Serious buyers only.

07/05/2026

Andale anu ndi anthu odabwisa.

Pena kumva izi usakunziwa munthu yo uziona ngati ku Malawi anachoka 2006 nde wabwela dzana and this was his first experience of Malawi's roads.

Our beloved President has been in Malawi for almost 20 years now.

He served as Minister of Justice and then Minister of education during the academic freedom, if my memory serves me well.

He later became the President of Malawi for a good 5 years and the condition of some of these roads were worse (M1 road from Kanengo to Mzimba), the M5 road was bad, the M1 road from Blantyre -Lilongwe was as it is with few maintanances here and there.

Here is my point, if we continue clapping hands when our leaders talk about our problems as if they are new and have been caused by someone from the opposition side then we will not see development. We will clap hands and joke about it and that will be it.

Mavuto ambili akuno has been around for over 2 decades.

Kuno anthu njala inayamba kuwapha kalekale mma early 2000, mankhwala nzipatala sanakhalepo okwanila for years, kwacha has been loosing its value ever since, miseu yabwino kuno ndiyowelengeka for years, kuno takhala tikumanga zinthu moyesezela for years miseu ndi ma bridge yoti imatha kusukunuka ndi mvula.

Wake Malawians, its 2026. ๐Ÿคจ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ

Munyengo ya EIS ya MRA.Three months ago while travelling from Msumba, I travelled with one businessman from Mzuzu. I rem...
06/05/2026

Munyengo ya EIS ya MRA.

Three months ago while travelling from Msumba, I travelled with one businessman from Mzuzu. I remember my boss asked this man, Kodi mukuti simukumvana pati ndi MRA nkhani ya new system yi?

And the guy laughed. And he said, Bwana mukuziwa chani? Ifetu sitimadana ndi kupeleka nsonkho, aliyese wa bimizisi amaziwa kuti tuyenela kutelo ndithu. Koma vuto pa machine anyuwaniya ndi nkhani ya kapezekedwe ka forex.

Nde analongosola motele:

Forex pa black market panopa which is the real situation and the only place where you can get any amount ili pa 4,000 MWK/$. Chifukwa mma bank mu akungogawa ma 2 pin and business wise nzosayenda kuti utenge 2 pin nkumati ukukaoda.

Nde tiyelekeze wakaoda katundu wa $10,000 yomwe wagula pa black market pa MK4,000/$ imene ndi 40,000,000 MWK.

Nde tiyelekezezo kuti wakagulisa katundu uja nkupeza ndalama yokwana 43,000,000 MWK zomwe zikutanthuza kuti phindu leni leni ndi 3,000,000 MWK.

Now, MRA powelengesa nsonkho sikutengela pa rate yoodela forex ya 4 pin ija ayi koma official rate, ya 1,750 MWK/$):

Nde nsonkho wa katundu uja ku MRA mmabuku mwawo akuwelengesa motele:

Ndalama zogulira katundu $10,000 ร— 1,750 = 17,500,000 MWK

Zomwe mwagulisa zomwe angazipeze mmabuku anu ndi 43,000,000 MWK.

Phindu loti lidulidwe nsonkho ndi 25,500,000 MWK

Umene nsonkho wake womwe ndi 30% ikukwana 7,650,000 MWK

Zosatila zake ndizoti phindu leni leni lomwe wapanga iweyo motengela ndi mene unagulira forex yokaodela katundu ndi 3,000,000 MWK pamene a MRA akuti ayi ndithu ndalama zathu ndi 7,650,000 MWK kupangisa bizimisi kubesa ndalama zokwana 4,650,000 MWK pa nsonkho kuti bizimisi iziyendabe.

Nde m***a kuona kuti apapa business ikudula chifukwa tikuyendela black market rate pokaoda zinthu pamene nsonkho tikutchajidwa mwa rate yoziwika ndi boma. Izizi sizoona and ndikupweteka ma business.

Atalongosola izizi tonse tinaamvesadi. Am not sure ngati vuto la system ndi lokhali mwinaso ena akuionela mbali zina. Moti nkuyankhula kwao kunationesa kuti zomwe akuyenela kuchita aboma nkuyesesa kuti anthu azipeza forex yonse pa official rate, and in so doing sangamve kuwawa kulikonse popeleka nsonkho, koma ngati satelo ndipo abizimisi azipeza forex pa black market, zikutanthauza kuti boma likhala likufinya zakunsi anthu ochita malondawa.

Mwamva inu a Malawi Government??? ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ

Address

Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Cardinal Henry posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share