
03/06/2025
Kuchokera mmawa pa 4 mpaka pa 8 mwezi uno wa June, Asilamu mazanamazana padziko lonse akhala akuchita Hajj, kukwaniritsa msichi ya chisanu yofunikira kwambiri kwa Msilamu wina aliyense.
Ulendo umenewu umasonyeza kutsatira mwachindunji machitidwe a Atumiki a mbuyo komanso kuzichepetsa kwawo ndikuzipereka pamaso pa Allah.
Kulowa Ihram
----------------
Asanayambe Hajj, anthu ochita Hajj-wa amayenera kuziyeretsa kaye paokha. Abambo amavala nsalu ziwiri zoyera zosasokedwa, pomwe amayi amavala zovala zoyenera ngati momwe amayenera kuvalira nthawi zonse. Kachitidwe kameneka kamaonetsa anthu kukhala ofanana pamaso pa Allah komanso kugonjera. Ndondomeko imeneyi imatchedwa Ihram.
Tsiku loyamba: Kufika ku Mecca komanso Ulendo wopita ku Mina
------------------------------------------------------------------------
Akafika ku Mecca, ma Hujjaj amayamba ulendo wawo ndi Tawaf, kumeneku ndi kuizungulira Kaaba kasanu ndi kawiri. Izi zikuwonetsa umodzi wa opembedza Mulungu mwa choonadi. Kenako amachita Sa’i, kumeneku ndi kuyenda kasanu ndi kawiri (7) pakati pa mapiri a Safa ndi Marwa, pokumbukira mayi Hajara panthawi imene ankafunafuna madzi kuti mwana wake Ismail amwe atathodwa ndi ludzu.
Kenako, akachoka kumeneku amayenda kupita ku Mina, mtunda wa makilomita 8 kuchokera ku Kaaba. Ndipo amadzagonapo usiku mu msasa waukulu, kupemphera ndikuchita ma Ibadah osiyanasiyana.
Tsiku lachiwiri: Tsiku la Arafah
---------------------------------
Madzulo ake, amayenda kupita ku phiri la Arafat, mtunda wa makilomita 15. Malo amenewa amachita pemphero la Wuquf, komwe ndi kuyimirira pomwe amachita mapemphero osiyanasiyana ndi kupempha chikhululukiro kwa Allah. Limeneli ndi gawo lofunika kwambiri la Hajj.
Usiku wake amayenda kupita ku Muzdalifah, kumeneku amakachita mapemphero a Maghrib ndi Isha. Pamenepa, amasonkhanitsa miyala yomwe adzagwiritse ntchito pa Ramy al-Jamarat (yogendera Satana) ndipo usiku onse amakhala ali pa malo amenewa kuchita ma Ibadah osiyanasiyana.
Tsiku lachitatu:Tsiku la Eid al-Adha ndi Kugenda Miyala
--------------------------------------------------------------
Ku Mina, ma Hujjaj amagenda miyala isanu ndi iwiri (7) kwa Satana, chimene chili chizindikiro chokana zinthu zoipa ndi machimo.
Kenako amazinga nyama ndi kupereka nsembe, pokumbukira chikhulupiriro cha Abraham pamene ankafuna kupereka nsembe mwana wake pofunitsitsa kutsatira lamulo la Mulungu. Nyama imeneyi imaperekedwa kwa osowa.
Ndipo kenako abambo amameta tsitsi lawo, ndipo amayi amapungula pang’ono tsitsi lawo, chizindikiro cha kuyambiranso moyo wauzimu.
Kenako amayenda kubwerera ku Mecca kuchita Tawaf al-Ifadah, kuzungulira Kaaba kachiwiri, kumene kumasonyeza kumaliza magawo akuluakulu a Hajj.
Tsiku lachinayi ndi lachisanu: Kugenda Miyala ndi Tawaf Yomaliza
------------------------------------------------------------------------
Kwa masiku awiriwa, ma Hujjaj amapitiriza kugenda miyala ku zipilala zitatu zonse zimene zili pa Mina. Akamaliza, amachita Tawaf al-Wada, kuzungulira Kaaba komaliza.
Ulendo uwu si umangokwaniritsa lamulo la chipembedzo chokha ayi, koma umabweretsa mtendere wauzimu, umodzi ndi chikondi pakati pa anthu ochokera m'mayiko osiyanasiyana. Tipemphe Allah kuti atipatse kuthekera kuti tsiku lina nafe tidzachite Hajj. Aameen!
Zithunzi: AP Photo, Getty Images