
07/09/2025
"Zomwe anthu ena aku Area 25 ku Lilongwe achita pogenda akuluakulu omwe amakonzekela msonkhano wawo ndi zodandaulitsa.
ziwawa zotere, zili ndi kuthekera kodzetsa mkwiyo wa anthu m'madera ena.
Izi zodandaulitsa kuti dziko lino likukuza m'bado wokonda ziwawa.
Ndipo uwu ndi uchitsiru wa anthuwo komanso omwe anawatuma",;- watero mtsogoleri wa chipani cha Odya Zake Alibe Mlandu yemwenso ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, a Michael Usi.