21/07/2026
LUSO LA MANJA NDIYE TSOGOLO LA DZIKO.
Luso la manja ndiye tsogolo la dziko, awa anali mawu omwe anayankhula nthumwi ya a Khansala a Ndirande-Nkolokoti Ward olemekezeka MAI KAMPHONI ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre.
Olemekezekawa anayankhula pa mwambo woyendera sukulu yophunzitsa luso lophika ndi kuchereza alendo ya AYIYEYE SITE SERVICES, Hospitality and Tourism Training School ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre.
Mukuyankhula kwawo iwo anati luso la manja lithandidza ophunzirawa kukhala wodzidalira pawokha pa chuma akamaliza maphunzirowa.
Pomaliza kuyankhula olemekezekawa analimbikitsa achinyamata amumzindawu kuti ino sinthawi yochita njengunje koma kusintha kaganizidwe.
Ndipo poyankhalapo nkulu wa sukuluyi Bambo Lameck Kadewere anathokodza kwambiri pakubwera kwa olemekezekawa ndikuzawalimbikitsa ophunzirawa.
Sukuluyi inakhazikitsidwa ndicholinga chofuna kutukula luso la kaphikidwe komanso kuchereza alendo.
Sukuluyi ikupezeka ku Machinjiri, mu mzinda wa Blantyre.