01/08/2025
Kodi Mukudziwa ?
Nkhumba ndiyoletsedwa kudya osati kwa asilamu okha koma ngakhalenso kwa akhristu, koma kuti chabe Mulungu akayankhula chinthu Mu Quran asilamu amanvetsera, kutsatira ndikukhanzikika pa malemba, nchifukwa chake zimaoneka ngati kusadya nkhumba nzachisilamu, koma ayi ndi chilengedwe kuti munthu asamadye nkhumba.
Qur'an: 2 v 173...nkhumba ndiyoletsedwa
Qur'an: 5 v 3.... Nkhumba ndiyoletsedwa
Qur'an : 6 v 145.... Nkhumba ndiyoletsedwa
Qur'an : 16 v 115..... Nkhumba ndiyoletsedwa
Mulungu analetsa ndipo asilamu anamvera ndikutsatira...
Bible: Leviticus11 v 7-8 ...Nkhumba ndiyoletsedwa
Bible: Deuteronomy 14:8... Nkhumba ndiyoletsedwa
Mulungu analetsa ndipo akhristu sanamvere ndipo sanatsatire..
Quran: 2 v 85.... Akukhulupilira gawo Lina la buku ndikusakhulupilira gawo Lina, Ndiye anthu a mchitidwe uwu, malipiro awo, ndi kunyozeka pa Dziko lapansi, ndipo pa kiyama adzabwenzeretsedwa ku chilango chowawa.
Mtendere ndi Madalitso a Mulungu apite kwa Abraham Mose Yesu ndi Muhammad..
Sautul-Huda