Patsinde Radio Station

Patsinde Radio Station PATSINDE RADIO..
0884062436/0997288885
(for business)

Apolisi ku Mponela m'boma la Dowa alanda njinga zamoto makumi awiri ndi zinayi(24)chifukwa chomphwanya malamulo apa msew...
18/08/2026

Apolisi ku Mponela m'boma la Dowa alanda njinga zamoto makumi awiri ndi zinayi(24)chifukwa chomphwanya malamulo apa msewu.

Malingana ndi Ofalitsa nkhani ku polisi ya Mponela Macpatson Msadala,izi zachitika lero pomwe alanda njingazi Malo osiyana siyana ochitira malonda,kusatira ntchito yapadera yoyendera ndi kuwunika oyendetsa njinga zamoto yomwe inatsogoleredwa ndi inspector Leston Masambo amene ndi owona za malamulo apa msewu.

Pa ntchitoyi , apolisi amayang,ana kwambiri njinga zamoto zomwe zimamphwanya malamulo monga kuyendesa njinga zamoto zomwe sizinalembesedwe,kuyendesa popanda inshuwaransi yovomelezeka komanso kugwiritsa ntchito matayala ok*tha kapena owonongeka.

M'mawu ake Masambo wati ntchitoyi yayenda bwino ,ndipo apolisi ku Mponela apitiliza ntchitoyi m'masiku akubwerawa pofuna kuchepesa ngozi zapamsewu,choncho wapempha eni njinga zamoto komanso oyendetsa njingazi k*ti azitsatira malamulo onse okhudza pamseu.

Hello Sunday...πŸ’₯🎯
16/08/2026

Hello Sunday...πŸ’₯🎯

Hello!!!Patsinde Radio Station !!!! stay tuned
15/08/2026

Hello!!!

Patsinde Radio Station !!!! stay tuned

Happy Sabbath!!!!Patsinde Radio Station!!!stay tuned
09/08/2026

Happy Sabbath!!!!

Patsinde Radio Station!!!stay tuned

  Mphekesera zoti akhoza kupita ku timu ya Arsenal zatha tsopano.Vinicious Junior yemwe ndi osewera m'mbali komanso k*ts...
06/08/2026



Mphekesera zoti akhoza kupita ku timu ya Arsenal zatha tsopano.

Vinicious Junior yemwe ndi osewera m'mbali komanso k*tsogolo kwa timu ya Real Madrid watikitiranso kontilakiti yatsopano k*timuyi kufika mu chaka cha 2032.

Izi zili chomwechi pomwe timu ya Arsenal imayembekezera k*ti osewerayi akhoza kupita k*timuyi, tsopano zafera m'mazira.

Team ya Malawi ya atsikana yomwe imadoda mpira wamiyendo yapitilira mu ndime ina.Izi zikudza pomaliza ndi ma poyintsi as...
06/08/2026

Team ya Malawi ya atsikana yomwe imadoda mpira wamiyendo yapitilira mu ndime ina.

Izi zikudza pomaliza ndi ma poyintsi asanu ndi imodzi mu gulupu C imene munali ma team monga Malawi, zambia, Egypt komanso Nigeria.

Ngakhale timuyi yagonja pa masewero ake apa 05 August 2026, 2:1 ndi team ya Zambia yapitilirabe potengera ndi m'mene yachitira mu gululi yomwe amaitcha head to head pa chingerezi.

Mu ndime yotsatira yama timu asanu ndi atatu timu ya Malawi ikumana ndi timu ya South Africa.
John Chisuse....... Lilongwe

06/08/2026

Bungwe la Malawi health Equity Network lapempha magulu osiyanasiyana, azipembezo, atolankhani, mafumu k*ti ayenera k*tengapo gawo polimbikitsa anthu k*ti ana alandire katemera wa polio.

Wapampando wabungweli George Jobe wayankhula izi pomwe unduna wa zaumoyo ndi ukhondo walengeza za kampeni wa katemera wa polio mdziko lonse wa ana kuyambira pa 11 mpaka 14 august 2026.

Jobe wati makolo amene amakhulupilira zipembezo zomwe safuna kupita kuchipatala ayenera awonetse chikondi Kwa ana awo k*ti akalandire katemera ameneyu.

Katemera wa polio ndiwa ulendo wachinayi ndipo akuyenera kulandira ndi ana amene sanakwanise zaka khumi mdziko lonse mosatengera k*ti analandirapo kale katemerayu kudzera mkampeni wammbuyo kapena mndondomeko ya katemera wa nthawi zonse.

Ulendo uno unduna wa zaumoyo ndi ukhondo wati ukufuna ufikire ana 7,069,865.

Hey πŸ‘‹πŸ‘‹ Thursday line up!! stay active!!!! Patsinde Radio Station !!!!
06/08/2026

Hey πŸ‘‹πŸ‘‹

Thursday line up!! stay active!!!!

Patsinde Radio Station !!!!

MGWIRIZANO UKUFUNIKA PA OIMBA NDI OMVERA NYIMBO ZA UZIMU MDZIKO MUNOIzi zadza ndi gulu loimba nyimbo za uzimu mdziko mun...
05/08/2026

MGWIRIZANO UKUFUNIKA PA OIMBA NDI OMVERA NYIMBO ZA UZIMU MDZIKO MUNO

Izi zadza ndi gulu loimba nyimbo za uzimu mdziko muno la Great Angels choir lomwe lapempha mgwirizano kwa oimba ndik*tsatira nyimbozi k*ti akhale ogwilizana.

Gululi layankhura izi kudzera pa tsamba lawo la mchezo kumasanaku k*ti mgwirizano wa oimba nyimbo za uzimu ndiwofunika kwambiri mdziko muno, kotero gululi latsimikiza k*ti ngat pangakhale kugwirizana zinthu zambiri zikhoza kupita patsogolo.

John Chisuse_Lilongwe


Mwamuna wa zaka 26  wamangidwa chifukwa chobaya mpeni woyendetsa kabaza ndikumubera njinga ya motoApolisi ku lilongwe am...
04/08/2026

Mwamuna wa zaka 26 wamangidwa chifukwa chobaya mpeni woyendetsa kabaza ndikumubera njinga ya moto

Apolisi ku lilongwe amanga Bryan Jere wa dzaka 26, pa mlandu omuganizila k*ti wabaya ndimpeni woyendetsa kabaza ndikumubera njinga yake ya moto nthawi 10 koloko usiku pa 1 August 2026, m' Dera la area 9 ku Lilongwe.

Malingana ndi lipoti a Apolisi ,usiku wa tsikulo woyendetsa kabazayo anali atangotsitsa kasitimala ku area 9 ndipo amabwelera ku town ya Lilongwe pamene athu awiri anamubisalira panjira. anthuwa Akuganizilidwa k*ti anamubaya ndi mpeni pachifuwa asanayese kumulanda njinga yake ya moto.

Ngakhale k*t anavulala kwambiri ovulazidwayo anakwanitsa kugonjetsa m' modzi mwa okayikilidwayo.

Alonda omwe anali pafupi anamva kufuula kwa wozunzidwayo ndipo anathamangira kukamuthandiza..

Pambuyo pa kafukufuku wa a polisi,njinga yamoto yomwe inabedwa inapezeka lolemba m' nyumba Ina ku area 36 komwe inabisidwa ndi wokayikilidwayo.

Apolisi akupitiliza kusaka wokayikilidwa wachiwiri yemwe sakudziwika Komwe Ali.

Bryan Jere amachokera m' mudzi wa Mzukuzuku,Mfumu yaikulu (T/A) Mzukuzuku m' boma la Mzimba ndipo akuyembelezera kuonekera ku khoti posachedwapa k*ti akayakhe mlandu wakuba mwachiwawa.

Wolemba : Christina Mdolo

Address

Box 2214 Blantyre
Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Patsinde Radio Station posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share

Category