05/07/2025
*BUS π DEPOT*
Bus inayima pa stage ndipo ena anatsika ena anakwera, modzi mwa okwerawo anali mzimai yemwe mmanja mwake ananyamula kamwana kakhanda .Tsoka ndilo bus inali itadzadza panalibe malo oti angakhale mmalo mwake anangoimilira ukunkono wina atafumbatila mwanayo kwinaku ndikugwilira chitsulo champando kupangila kuti asagwe. Bus inayenda mtunda wautali mayiyo akadali chiimire nkhanda lili manja,ulendo uli mkati nkhandalo linayamba kulira koma maiyo anasowa kuti ayamwitsa bwanji ali chiimire chomwecho,panalibeso ngakhale m'modzi yemwe anapeleka mpando wake kuti maiyo akhalepo.
Kenako driver atawona kuti maiyo wasungulumwa anayimitsa bus yo pambali nayankhula motere :.... "Mai tabwerani ndi mwanayo mudzakhale pampando wangawu kuti muthe kumutothoza". Anthu ataona izi anadziwa kuti mayiyu akakhala pa mpando wa driver yo ulendo uyima choncho onse anayamba kukanganirana mayiyu nkumuitanisa pa mimpando yawo kuti adzakhale.
*Phunziro* : ```Umakhala osafunikira pamavuto,abwenzi amathawa, abale amangokuyang'ana ukuvutika koma Mulungu akazangokukodolani kuti zakhaleni apa ndipomwe abwezi azakheleso nyomi pambuyo pako.
Pano ndinu osafunikira kamba ka nyengo zomwe mukudusamo koma Mulungu akangoti waitani muzakhala ofunikira.Amen``` .