
04/08/2025
ANTHU AYEMBEKEZERE MPIKISANO WAPAMWAMBA (MDFA).
Komiti yoyendetsa masewero ampira wamiyendo m'boma la Mangochi ya Mangochi District Football Association (MDFA) yatulutsa ndandanda wamasewero amumpikisano wa Castel Cup wa chaka chino.
Izi ndi malinga ndi mayere omwe komitiyi pamodzi ndi matimu omwe akutenga nawo gawo mu mpikisanawu anali nawo loweruka pa bwalo la zamasewero la Mangochi
Poyankhula ndi Lilanguka Sports Desk mlembi wamkulu wa komitiyi Islamu Rajabu wati anthu ayembekezere mpikisano wa Castel wapamwamba chaka chino.
Apa iwe wati alengezabe malo komanso masiku omwe mpikisanowu uyambe koma wapempha matimu kuti akhale okonzeka.
Ndipo ndandawu uli motere:
1-Kalonga Stars 🆚 Majuni Super Market
2-Chiponde Hammers 🆚 Namwera United
3-Philirongwe United 🆚 Black Jack
4-Namias United 🆚 Chipoka Rangers
5-Chawe Bullets 🆚 MMF Marines Reserve
6-Galaxy 🆚 Madelco Super Stars
7-Tech 🆚 Kondwan Mbumba
8-Makawa Young Navy 🆚 Chimbende united.
Timu ya Chipoka united inafika mu ndime ya national level chaka chatha pomwe inatuluka mumpikisanowu itagonja ndi timu ya Mighty Wandereres ndi zigoli 10 kwa chimodzi masewero omwe anachitika pa bwalo la Kamuzu mu nzinda wa Blantyre.
Kampani ya yopanga ndikugulitsa mowa ya Castel ndi yomwe imathandiza mpikisanowu ndi ndalama zokwana k450 million , ndipo timu ya Mighty wanderers ndiyomwe inakhala akaswiri ampikisanowu.
Wolemba : Patrick Makweza