01/06/2022
Aroma 13:11-14
Ndipo citani ici, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano cipulumutso cathu ciri pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupira. Usiku wapita, ndi dzuwa layandikira; cifukwa cace tibvule nchito za mdima, ntibvale camuna ca kuunika. Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'cigololo ndi conyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai. Koma bvalani inu Ambuye Yesu-Kristu, ndipo musaganizire za thupi kucita zofuna zace.
Mulinazo zambiri zimene mukuziwona zokondweretsa moyo wanu inu nkumati apa nde chinyamata chikuyenda bwino, koma ziwani kuti zonsezo ndizachabe ngati mwainu mulibe Yesu. Chopambana zonse kuti tizanjoye ndi moyo uno unkukhala ndi Yesu Amen.