
14/10/2025
MWAI WA NTCHITO
Team Ndi Chifukwa Chani (TNCC) ikufuna Katswiri yemwe amatha kumeta kuti azigwila ntchito m'nchipinda chometa anthu (Barbershop).
Zoyeneleza za Munthuyu
- Akhale Munthu oti ali ndi Malawi School Certificate of Education (MSCE)
- Akhale kuti anagwilako ntchito yometa kwa Zaka zopyolera zitatu (3).
- Akhale oti amadziwa kumeta kametedwe konse (Style) komwe anthu amameta kutengela kuongoka, kubulungila ndi kupindika kwa Mitu yawo.
- Akhale Munthu odziwa kucheza ndi kucheleza makasitomala.
- Asakhale wambili yotolatola kapena kuti Mbava.
Ntchitoi munthu ameneyu azigwilira mu M'zinda wa Lilongwe.
KAFUSILIDWE KA NTCHITOI ( How to apply )
- Tumizani Curriculum Vitae (CV), Chithunzi mukumeta ngati chilipo komaso Certificate yanu ya MSCE ku nambala iyi +265 994 689 540
CHINA..
Kwa Iwo omwe alibe Certificate ya MSCE koma ali ndi ekisipiliyensi ya ntchitoi ndipo ali ndi kuthekela kwa zonse zoyenelazi athaso kulembela.
____________