Likoma FM 107.6Mhz

Likoma FM 107.6Mhz Voice of Islanders

Ofesi yowona k*ti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo ku Likoma yati amayi akukumana ndi nkhanza zochuluka m...
16/10/2025

Ofesi yowona k*ti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo ku Likoma yati amayi akukumana ndi nkhanza zochuluka m'bomali.

Izi ndimalingana ndi mulangizi mu ofesiyi a Emily Newa omwe ati ofesi yawo ikulandira ma ripoti komanso madandaulo kuchokera kwa amayi ochuluka omwe akuchitilidwa nkhanza.

"Madandaulo omwe tikulandira ndi kugonedwa ndicholinga chak*ti amayi agule nsomba kapena Usipa mosavuta, kuletsedwa mpata osonkhana ndi anzawo m'magulu abanki nkhonde komanso kusapatsidwa ndalama panyumba." Atero a Newa.

Iwo ati izi zikupita patsogolo kaamba koti m'boma la Likoma kulibe mabungwe olimbikitsa nkhani zamaufulu omwe amalimbikitsaso k*thana ndi nkhanza.

Poyankhapo m'modzi mwa amayi omwe amamenyelera ufulu wa amayi mdziko muno mayi Barbara Banda ati kukhala mzimayi sichifukwa kotero abambo asazunze amayiwa potengera mpata oti ndi Amayi.

Mayi Banda omwenso ndiwapampando wa amayi omwe amachita malonda mdziko muno wati amayi asamadziwonere pansi ndipo adziwonetsa chilungamo pomwe apatsidwa mpamba wochitira mabizinesi ndicholinga choti amuna awo adziwakhulupirira.

: Oliver Malibisa.

Pomwe kwatsala masiku awiri k*ti tifike tsiku la anakubala apolice m'boma la Likoma ati anthu omwe akukonzekera tsikuli ...
12/10/2025

Pomwe kwatsala masiku awiri k*ti tifike tsiku la anakubala apolice m'boma la Likoma ati anthu omwe akukonzekera tsikuli adzasangalale mwa umunthu.

Titalankhula ndi ofalitsa nkhani pa Police ya Likoma a Andrew Kusimbwa wati nthambi zonse zapolisi zokonzekera kupitiliza kugwira ntchito yawo mwa ukadaulo patsikuli.

Kusimbwa wapempha amayi komanso atsikana k*ti patsikuli adzasunge chikhalidwe polemekeza mabanja awo pak*ti m'nyengoyi ambiri amalowelera pomwa mowa mwauchidakwa komanso kuchita zinthu zina zosayenera.

"Kusambira pomwe usakudziwa, kuyendetsa njinga moposa muyeso, kukwera mabwato ndizina mwazomwe zingabweretse ngozi patsikuli", atero Andrew Kusimbwa.

Nawo mayi Gloria Chikhola omwe ndi wamvula zakale, ati tsikuli ndilolemekeza anakubala ndipo apempha amayi omwe akukonzekera tsikuli k*ti adzasangalale mosunga umunthu wawo.

Chaka chilichonse m'dziko lino amayi amakondwerera tsikuli pa 15 October.

: Oliver Malibisa.

11/10/2025

Big shout out to my new rising fans! Likoma Secondary School, MIC HAEL

Mwiniwake wa malo ogona alendo omwe akuwatcha k*ti Mwayi Wanga Guest House m'boma la Likoma ati malowa awatsegulira pa 1...
11/10/2025

Mwiniwake wa malo ogona alendo omwe akuwatcha k*ti Mwayi Wanga Guest House m'boma la Likoma ati malowa awatsegulira pa 12 mwezi uno.

A Yamikani Mwambafula awuza Likoma Radio k*ti pakadali pano chilichonse chokonzekera mwambowu chilimchimake ndipo ati patsikuli anthu ayembekezere kudzasangalatsidwa ndi oyimba osiyanasiyana kuphatikizapo Gibo Piason.

A Mwambafula awonjezera k*ti Guest House yi ili ndizipinda zokwana 39 komanso ma charlets 10.

"Ndapanga izi podziwa k*ti chilumba cha Likoma ndimbali imodzi yamalo okopela alendo m'dziko lino ndipo ndinaona k*t ndithandizile kuchepetsa vuto lamalo ogona alendo".

Iwo atinso nthawi zina alendo akabwera ochuluka ku Likoma amasowa malo ogona kaamba kakuchepa kwamalo ndipo ati ndichiyembekezo chawo k*ti Mwayi Wanga Guest House ichepetsa vutoli.

Malowa omwe amangidwa mwamakono ali ndimalo wodyela komanso malo omwe makasitomala awo adzitha kumaonela mpira ndizina kudzera pa DSTV.

: Martin Mnkhwamba.

09/10/2025

Zanyengo, 9/10/2025.

Tiyembekezere nyengo ya mphepo ndi ya mitambo yapatalipatali komanso mvula yowaza ya mabingu m'madera ena usiku uno ndi mawa m’mawa.

Mawa masana, kudzakhala nyengo yamphepo ndi ya mitambo yapatalipatali komanso mvula yowaza ya mabingu m'madera ochepa.

Langizo: Tiyembekezere mphepo zamphamvu zosinthasintha zomwe zikhoza kuyambitsa mafunde pa nyanja zathu zonse. Choncho onse ogwiritsa ntchito nyanja zathu, kuphatikiza asodzi, akupemphedwa kukhalabe osamala.

Mphepo iziomba momverera kuchokera kumvuma.

Loweluka kudzakhala kwanyengo yamitambo yapatalipatali komanso mvula yowaza ya mabingu m’madera ena.

: Chiletso Bisweck.

09/10/2025

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Kalima Wa Kalima John, Martinez Santos Morgan, Adah Amakanjirah, Kingsley Moyo, Thoko Mbendera, Joseph William Godsent Kollie, Prudence Yagama, Felisberto Asante Nkhoma, Wezzie Kanyika, Cassper Kamwendo, Innocent Chilembwe, Patrick Gama, Auckland Martinez Mjima, Khoh-Bzy Mw, Elvis Khaid Masano, MIC HAEL, Cosmas Azimuthal Prosper, Katema Christopher, Tairea Mchule, Emmanuel Jr Nahosi, H**e Chirwa, Kamodzi Wiseman, Zuze Kuntonda Sinjan, Kay Oww Platnumz, Malinga Lamine Jr.

Team ya Chiponde fc ndi akatswiri  a Castel Challenge Cup m'boma la Likoma.Pa 5 October 2025 team ya Chiponde fc yakwani...
06/10/2025

Team ya Chiponde fc ndi akatswiri a Castel Challenge Cup m'boma la Likoma.

Pa 5 October 2025 team ya Chiponde fc yakwanitsa kuvala ukatswiri wa Castel Challenge Cup m'boma la Likoma itagonjetsa team ya Try Again FC kudzera m'ma penarty masewero omwe anathela 3_3 mu 90 minutes.

Kudzera m'ma penatewa anyamata a Chiponde FC apeza chipambano ndi zigoli zitatu pomwe team ya Try Again FC inapeza chigoli chimodzi k*tsatila kuphonya kwa Chipatso mkali, Martin Thawe komanso Willium Songa zomwe zinapangitsa k*ti masewerowa akomere Chiponde FC 3_1.

Pak*tha pa masewerowa mphusitsi wa Chiponde fc Khedila Mhonie anayamikila anyamata ake pogwira ntchito yotamandika, "timayenera kuwina game mu 90mins momwemo chifukwa ife ndamene timakhala ndi mpira koma popeza Try Again ndi team yaikulu ife tingothokoza kaamba ka chipambanochi."

Khedila wawonjezera k*ti pakadali pano maso awo akuyang'ana ku mtunda komwe akhale akulowela posachedwapa.

Chiponde FC yalandila ndalama zokwana 1million kwacha ndipo Try Again FC omwe ndima runners up alandila k300,000.

: Martin Mnkhwamba.

05/10/2025

Voice of Islanders

04/10/2025

Nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwanyengo yati lero, tiyembekezere nyengo ya mphepo ndi ya mitambo yapatalipatali m’madera ambiri komanso mvula ya mawawa m’madera ena usiku uno ndi mawa m’mawa.

Nthambiyi yati mawa masana, kudzakhala kwanyengo ya mphepo ndi ya mitambo yapatalipatali m’madera ambiri komanso mvula ya mawawa m’madera ena.

Nthambiyi ikuchenjeza k*ti mphepo ya mwera ipitilira kuomba pa nyanja ya Malawi ndi nyanja zina choncho onse ogwiritsa ntchito nyanjazi kuphatikiza asodzi, akupemphedwa kukhalabe osamala.

Mphepo Iziomba mochokera kumwera chaku mvuma.

Muchikalata chake nthambiyi yati Lolemba kudzakhala nyengo yamphepo, yamitambo yapatalipatali komanso ya mvula yamawawa m’madera ena.

: Chiletso Bisweck.

01/10/2025

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Francis Travis Francas, Kelvin Nyambose, Dyna Malama, Nathan Watsopano Kussah Wyson, Cyhook Mercy Aayz, Hope Mw, Sammy Chimzy Ndilowe, Layz Layz, Kendrick Steven Malinda, Divad Mumos

Team ya Try Again FC yafika mu ndime yotsiliza mu chikho cha Castel Challenge Cup itagonjetsa Nkhwazi FC 2 kwa du.Izi zi...
29/09/2025

Team ya Try Again FC yafika mu ndime yotsiliza mu chikho cha Castel Challenge Cup itagonjetsa Nkhwazi FC 2 kwa du.

Izi zili chonchi k*tsatila masewero omwe anachitika Lamulungu lapitali pa Madimba Community Ground mndime ya Semi final pakati pa Nkhwazi fc ndi Try Again fc.

Zigoli ziwiri zomwe Adam Mustapha anamwetsa nzomwe zapangitsa k*ti Try Again ifike ndime yotsiliza ndipo anyamata a Nkhwazi fc anakumane ndi kiyama pomwe atuluka wopanda dipo mchikhochi.

Zateremu team ya Try Again FC idzakumana ndi Team ya Chiponde fc mu ndime yotsiliza ya mchikhochi.

Team ya Try Again yafika mundime yotsiliza kachitatu kuchoka momwe chikho cha Castel Cup chinakhazikitsidwa mchaka cha 2023.

: Martin Mnkhwamba.

27/09/2025

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Symon Karjel Nkhomzy, Charles Stephano, Franklyn Mphamba, Favour G Everton, Charles Mbewe, Gladys Mason, Remmy Bou Kathingo, Boston Mhaji, Israel Lucus, Annette Chembe, Austnez Phreps, Ashie Wa Jemah, Jussah Ndiphwanya Mapondera, Esnart Milanzi, Felix Thyoka

Address

P. O Box 77
Likoma

Opening Hours

Monday 06:00 - 17:00
Tuesday 06:00 - 17:00
Wednesday 06:00 - 17:00
Thursday 06:00 - 17:00
Friday 06:00 - 17:00
Saturday 08:00 - 17:00
Sunday 08:00 - 17:00

Telephone

+265991417373

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Likoma FM 107.6Mhz posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Likoma FM 107.6Mhz:

Share

Category