18/10/2025
Mwana wa mkazi wa Chisilamu, niqaab ndi mphatso yochokera kwa Allaah.
Si chovala chokongoletsera kapena chofuna kupezera ma likes, koma chitetezo cha ulemu wako ndi chizindikiro cha kulemekeza Mulungu wako.
Pamene ena akugwiritsa ntchito TikTok kuvina ndi kudzikongoletsa seeking attention ya Anthu osakhala Attention ya Allaah, iwe khala wosiyana ndi iwo chifukwa wasankha kusunga khalidwe.
Koma ngati niqaab yawoneka pa ukuvina, zimachotsa tanthauzo lake.
Ulemerero wa niqaab si mmene anthu amakuwonera, koma mmene Allaah akukuonera.
Kuvina pa TikTok, ngakhale mutaphimba nkhope, kungakoke chidwi cha amuna ndi kusokoneza omwe amaona nyasizi.
Zimenezo zimakhala chiopsezo cha fitnah, ndipo sizigwirizana ndi umunthu wa mkazi wosiririka.
TikTok imakopa chidwi cha anthu, koma osalola chidwi cha anthu kuchotsa ulemu wako.
Choncho, musachite kuti anthu akukonde,
koma muchite kuti Allaah akukonde. Musapereke Mpata kwa Anthu Omwe akusakasaka njira zotukwanira akazi ovala motere kuti ndimongobisalira koma ndi Ashawuwo.
Ulemerero wa mkazi si thupi lokha kapena maonekedwe,
koma mu khalidwe, mtima, ndi kulemekeza malamulo a Allaah,
Khalani chitsanzo, osati chidwi.
Khalani ofatsa, osati masewera mukuchitawa
Khalani ndi niqaab yomwe imalemekezedwa ndi anthu komanso imavomerezedwa ndi Allaah.
May ALLAH the Almighty Guide us all
Kinanah Jannah.
WASSALAM ALAYKUM WARAHMATULLAH WABARAKATUH