20/02/2026
*ZAMASEWELO MADZULO ANO* ⚽🏃🏾
Inu mawatu kuli kanthu kokanthula ndi SIZASI pamene tikufuna kupeza mbiya ng'ambe kapena kuti chidakwa choziwa kumwa mowa.
Ndipo nditha kukutsikimizilani pano kuti Matimu a Goshen City Dedza Dynamos FC komanso FCB Nyasa Big Bullets achita zokonzekera zawo zotsiliza lero pokonzekera ndime yotsiliza ya mpikisano wa chikho cha Castel Challenge yomwe iseweredwe pa Bingu National Stadium Loweluka pa 21 February, 2026.
Ndipo Kumbali ya timu ya Goshen City Dedza Dynamos FC, aka mkoyamba kufika ndime yotsiliza ya mpikisanowu pomwe timu ya FCB Nyasa Big Bullets yafika kachiwiri ndime yotsiliza ya mpikisanowu kaamba koti m"chaka cha 2023 anafikanso ndime yotsiliza ndipo anapambana.
Nawo osewera akale a timu ya Goshen City Dedza Dynamos FC, Khumbo Banda komanso Lameck Gamphani akuyembekezeka kukhala mbali imodzi ya timu ya Bullets yomwe ikuphunzitsidwa ndi Gilbert Chirwa yemwenso anaphunzitsako timu ya Goshen City Dedza Dynamos FC m''chaka cha 2023.
Polankhula zokhudza masewerowa, Chirwa wati osewera ake adzikonzekeretsa bwino masewerowa ndipo chidwi chawo chili potenga ukatswiri wa chikhochi.
Pomwe Alex Ngwira wa Goshen City Dedza Dynamos FC wati akudziwa kuti mbiri ili patsogolo pawo ndipo osewera ake ngokonzeka kumalizitsa ntchito yomwe ayiyamba kale.
Ndipo osewera kutsogolo mu timu ya FCB Nyasa Big Bullets yemwenso ngochokera ku Dedza Maxwell Phodo Gasten ndiye akutsogolera ndandanda wa osewera omwe agoletsa zigoli zochuluka pomwe wagoletsa zigoli zisanu ndi ziwiri pa masewero anayi.
Musayiwale kuti *Mayamiko Kanjere* ndiye ayimbire masewero a ndime yotsilizayi yomwe mphoto yake ndi K55 million komanso kudzigulira malo mu mpikisano wa Confederation Cup ku timu yopambana.