Urban Trends

Urban Trends Chimbota Radio: Your hub for arts, culture, entertainment, and sports across Malawi. Tune in now.
(1)

Dekhani bwana iwongoka ikawuma  cement wake ndiwotero
29/08/2026

Dekhani bwana iwongoka ikawuma cement wake ndiwotero

Koma tanyozeka nkhani ya Chule ija yakwera mtunda🤣🤣😂😂
24/08/2026

Koma tanyozeka nkhani ya Chule ija yakwera mtunda🤣🤣😂😂

Olo mmene wagwilidwila Mfutiwo eeeee😢😢😢🚶‍♂️🚶‍♂️Apolisi ku Lilongwe amanga bambo wa zaka 31 zakubadwa kaamba komuganizira...
19/08/2026

Olo mmene wagwilidwila Mfutiwo eeeee😢😢😢🚶‍♂️🚶‍♂️
Apolisi ku Lilongwe amanga bambo wa zaka 31 zakubadwa kaamba komuganizira kuti amalowetsa mfuti mdziko muno komanso kupezeka ndi mfuti popanda kalata zomuyenereza kukhala ndi mfutizo.

Wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za polisi ya Lilongwe a Khumbo Sanyiwa ati apolisi amanga bamboyu a Christian Ndovi lachiwiri lapitali atawapeza ndi mfuti ziwiri ndi zipangizo zina zokhudza mfuti.

Iwo ati apolisi alanda mfuti zina ziwiri zomwe anadziwitsidwa kuti bamboyu anagulitsa kwa munthu wina ku area 43 mu mzindawu.

Iwo ati bamboyu akaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kumene akayankhe mlandu wopikula mfuti kunja, kupezeka ndikugulitsa mfuti mosatsata lamulo.

Zambia Updates :MP akuchotsa malata ake pa church yomwe anakometsa pakampeni, kaamba koluza zisankho mu dziko la Zambia ...
18/08/2026

Zambia Updates :

MP akuchotsa malata ake pa church yomwe anakometsa pakampeni, kaamba koluza zisankho mu dziko la Zambia 🙌

Pena ngati timamenya ndi azibambo pena ai😊Congratulations Malawi inuyo mwapanga ndipo no need to worry 😊
16/08/2026

Pena ngati timamenya ndi azibambo pena ai😊Congratulations Malawi inuyo mwapanga ndipo no need to worry 😊

Ambili mukumuziwa uyu omasulira ma film amadziwika ndimaina awa apolo G zone  entertainment wamwalira atadwala nthawi yo...
13/08/2026

Ambili mukumuziwa uyu omasulira ma film amadziwika ndimaina awa apolo G zone entertainment wamwalira atadwala nthawi yochepa

rest in peace dolo

Awatapa Ana ajaAna anayi okhala m’misewu, azaka zapakati pa 12 ndi 17, amangidwa ku Blantyre chifukwa chokayikiridwa kut...
12/08/2026

Awatapa Ana aja
Ana anayi okhala m’misewu, azaka zapakati pa 12 ndi 17, amangidwa ku Blantyre chifukwa chokayikiridwa kuti akhala akuchita zigawenga zolanda anthu komanso kuba, zomwe zinaoneka m’mavidiyo omwe akufalikira pa malo ochezera a pa intaneti.
Anayiwa anamangidwa Lachitatu nthawi ya 1:30 masana ndi Detective Christopher Pangeti pamodzi ndi apolisi ochokera ku Blantyre Criminal Investigations Department.
Akufufuzidwa pa milandu yokhudza kuba, kuwopseza anthu, kuchita zachipongwe komanso kusonkhanitsa zida, potsatira zochitika zomwe akuti zinachitika m’dera la Ginnery Corner.
Apolisi ati ana anayiwa ali m’manja mwa apolisi ndipo kafukufuku ukupitilira pa milandu yomwe akukayikiridwayi.

12/08/2026

Ana amasikini atasatu townimu.
Komatu izi Prophet Mkupamame ananenapo zaka zapitazo kuti ana mukamawapatsa ma K5 tsiku lina akakula adzafuna kuziimila paokha. Ngati sitisamala town yathu, zinthu zitha kukhala zovuta kwambiri mtsogolo.
Tsopano ana amasikini aja akukula ndipo ayambanso kusowetsa mtendere. Chonde 🙏, ngati n’zotheka, tiyeni tichitepo kanthu mwamsanga zinthu zisanafike poipa kwambiri.
Town yathu ndi yathu tonse. Tiyeni tichitepo kanthu lero.

Komatu Liwonde kwayaka Moto😂😂ngati za mu filmtu anyway akuti Apolisi ku Liwonde amanga mayi wazaka 21 a Tiyamike Mkandaw...
11/08/2026

Komatu Liwonde kwayaka Moto😂😂ngati za mu filmtu anyway akuti

Apolisi ku Liwonde amanga mayi wazaka 21 a Tiyamike Mkandawire omwe akuwaganizira kuti amanamiza anthu kuti ndi namwino pa chipatala chachikulu cha Machinga.

Malinga ndi mneneri wa polisi ya Liwonde a Ngwashape Msume, a Mkandawire amavala unifolomu yoyera pachipatalachi zomwe zidadabwitsa anthu ena ogwira ntchito pamalowa.

Atampanikiza ndi mafunso, mayiyu adanama kuti amachita maphunziro ake aunamwino.

Apa nkhaniyi idatulidwa ku polisi, pomwe apolisi adakwanitsa kumanga mayiyu yemwe akuyembekezeka kukaonekera kubwalo lamilandu posachedwapa .

Kachikena Agide kkkk Mayi  Rabecca Selemani awapeza ndi vindalama vimene adabela mzika Ina ya Ameleka imene imagona ku L...
11/08/2026

Kachikena Agide kkkk
Mayi Rabecca Selemani awapeza ndi vindalama vimene adabela mzika Ina ya Ameleka imene imagona ku Liwonde Sun. Iwowo amagwila ntchito yokolopa ndipo mu room ya Monica Grant adatolamo 1.9 mita ya Malawi ndi $500 ya ameleka.
Ai zikomo

Address

Machinjiri
Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Urban Trends posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share