
13/08/2025
ZINA MWA NKHANI ZIKULUZIKULU ZOMWE ZINALIKO DZULO
1️⃣ Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera ati ali ndi malingaliro ofuna kukweza ndalama ya Constituency Development Fund (CDF) kuchoka pa K220 million kufika a K500 million. Mzaka 5 zapitazi, a Chakwera akweza CDF kuchoka pa K30 million kufika pa K220 million.
2️⃣ Mtsogoleri wa chipani cha UTM, a Dr. Dalitso Kabambe, ati akalowa m'boma pa 16 September adzakhazikitsa migodi yopitira 10 kuphatikizapo umodzi omwe uzidzatenga mafuta ndi gasi pansi pa nyanja ya Malawi.
3️⃣ Chipani cha MCP, kudzera kwa mneneri wa chipanichi a Jessie Kabwila chati a Micheal Usi ngati Ali ndi ombuni oti anthu ena m'boma akuchita katangale abweletse poyera komanso atule pansi udindo wawu Vice President ngati atopa mmalo moipitsa mbiri za anthu ena.
4️⃣ A Micheal Usi yemwe ndi mtsogoleri wa chipani cha Odya Zake Alibe Mlandu wati mu boma lili panoli muli mbamva zotheratu ndipo walangiza anthu kuti asalorenso mbava zimenezi kwawanamiza ndi zinthu zoti sangazikwanitse kuchita.
5️⃣ A Jane Ansah, yemwe ndi running mate wa mtsogoleri wa chipani cha DPP pa chisankho chapa 16 September ati amayi alemekezeka kaamba kakusankhidwa kwawo kukhala running mate.
6️⃣ Prophet Shepard Bushiri, yemwe ndi mtsogoleri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering (ECG), the Jesus Nation wapempha andale kuti alonjeze zinthu zomwe angazakwanilitse kuchita mmalo moonjeza bodza.
7️⃣ Bungwe la MEC lati silidzachititsa chisankho cha phungu wa nyumba ya malamulo ku chigawo chaku Lilongwe Chilobwe Constituency chifukwa a Chakakala Chaziya alowa opanda Opikitsana nawo.
8️⃣ Bwalo la milandu ku Mkukula m'boma la Dowa lagamula a Shadreck Nkhanizimatha a dzaka 39 kukakhala kundende zaka 17 atapezeka olakwa pa mlandu ogwililira mwana obeleka okha wa dzaka 16.
9️⃣ A police m'boma la Mulanje amanga a Petrol Manuel and Chikondi Antonio and a Malawian Humphrey Koloko ochokera m'dziko la Mozambique atapezeka ndi mafuta a petrol okwana 170 litres omwe amafuna kupititsa m'dziko la Mozambique.
🔟 Banki ya FCB yapereka K500,000 kwa osewera aliyense wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets powathokoza chifukwa chotenga chikho cha Airtel Top 8 komanso kulimbikira kwao mu ligi ya TNM.
Innoma-Journalist