26/08/2025
π¨ PETER MUTHARIKA AYANKHULA MOKWANA!
Mtsogoleri wa DPP, Prof. Peter Mutharika, wati misonkhano yomwe akuchititsa sabata ino yanyozetsa onse amene amawafunira zoyipa.
Iye wayankhula izi ku Nkhotakota, atachokera ku Mzuzu komwe anachititsa msonkhano waukulu.
Mutharika wati akabwerera mβboma pa 16 September, DPP idzalimbana ndi njala, kukonza misewu ndi kukonza chuma cha dziko chomwe akuti chasokonekera mu boma lomwe lilipo.
Misonkhano ikupitirirabe ndipo ulendo wotsatira ndi pa msika wa Kaphatenga ku Salima.
Kodi mukuona ngati Mutharika ali ndi mwayi wobwerera mu boma?
π Lembani maganizo anu!