01/06/2026
Boma latsutsa mphekesera zokhudzana ndi mkumano wa Nduna
Ofesi ya Mtsogoleri wa dziko lino ndi Nduna ya OPC yatsutsa
mphekesera zimene zikuyenda mmasamba a mchezo zonena kuti Mtsogoleri wa dziko lino Pulofesa Arthur Peter Mutharika sanatsogolere mkumano wa nduna umene unachitika sabata yathayi, ndikutsindika kuti iwo akhala akutsogolera mkumanowu chiyambireni ntchito yawo.
Malingana ndi chikalata chimene ofesiyi yatulutsa ndipo chasayinidwa ndi Mlembi wa Mkulu wa boma, a Justin Saidi, a Mutharika amatsogolera misonkhano yonse chikhalireni pa mpando pa 16 Sepitembala chaka cha 2025.
“A Pulezidenti amatsogolera mkumanowu mogwirizana ndi mphamvu zimene anapatsidwa kwa iwo mu Malamulo a Dziko lino komanso malingana ndi udindo wawo,” chatero chikalatachi.
Ofesiyi yapempha Amalawi kugwiritsa ntchito ufulu wa kayankhulidwe moyenera ndikupewa kufalitsa nkhani zosatsimikizika zimene zimachotsa chikhulupiriro cha anthu mu nthambi za boma.