26/08/2025
Zochitika ๐ฅ
Apolisi ku Lilongwe amanga mneneri Zelesi Divason ndi atumiki ake atatu powaganizira kuti amasunga mokakamiza mnyamata wina yemwe ali ndi matenda a mu ubongo, yemwe iwo amati amuukitsa ku akufa.
Malinga ndi wachiwiri kwa mneneri wa apolisi ya chigawo cha Central West a Foster Benjamin, mneneri Divason ndi atumiki akewo analosera kuti mwana wa mayi Mary Chelewani yemwe anachita kuphedwa mu 2023, auka ndipo abwelera kwa mayi ake.
Kutsatira chikhulupiliro, mayi Chelewani akuti anaona mnyamata yemwe anaoneka ngati mwana wawo ku Area 36 ndipo nthawi yomweyo anamutenga nkumupititsa kwa mneneri Divason.
"Ngakhale mnyamatayo anali ndi nkhope yosiyana ndi mwana wa mayi Chelewani yemwe anamwalirayo, mneneri Divason akuti anatsimikizira mayi Chelewani kuti mwana wawo ndiyemweyo ndipo wauka. Mneneriyu akuti anauza mayiyo kuti asunge mnyamatayo ndipo azipemphera tsiku lililonse kuti nkhope ya mnyamatayo ibwelere ndikufanana ndi nkhope yomwe mwana wawo anali nayo," atero a Benjamin.
Koma patatha masiku, mayi wina anakanena ku polisi ya 36 kuti mwana wake wa zaka 27 wasowa ndipo mayiyo anati mnyamata amasungidwayo ndi mwana wake.
Pakadali pano apolisi amanga mneneri Divason wa zaka 40, aneneri ake; Emily Chanunkha (35), Konsolata Osikala (46), ndi Flora Gamulani (42) ndipo apatsidwa mlandu obisa kubedwa kwamunthu komanso kuzembetsa munthu zomwe ndi zosemphana ndi lamulo 264 la penal code.
Kumangidwa kwawo kukudza pomwe enanso ku Mchinji ndi ku Area 36 anamangidwanso kutsatira kunamiza anthu anthu kuti aukitsa akufa.
Wolemba Cathy Maulidi