09/07/2025
Apolisi ku Chitipi ku Lilongwe, amanga abambo awiri omwe anaba njinga yamoto ya kabaza yomwe iwo anakwera pa 4 Julayi 2025, nthawi ya 9 koloko usiku kufupi ndi Admarc komwe mwini njingayi anamenyedwa.
Malingana ndi mneneri wa polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, abambowa ndi Vincent Phiri wa zaka 20 ndi Smart Banda wa zaka 30 ndipo onse amakhala ku Area 36.
Iwo ati patsikuli awiriwa anakwera njingayi ku Area 36 atamuwuza mwini njingayu kuti akupita ku depoti ya Lilongwe.
Koma atafika pa Admarc abambo awiriwa anamumenya wa njingayu ndi kuthawa ndi njingayo.
Patapita masiku awiri apolisi a kafukufuku ku Chitipi, anamva mphekesera kuti abambo awiriwa ali ndi njinga. Atachita kafukufuku wawo, apolisi anamanga awiriwa komanso njingayi inapezeka.
Oganiziridwawa akawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mlandu wakuba.
Phiri amachokera m’mudzi mwa Swayibu , Mfumu yayikulu Msanama, m’boma la Machinga, pamene Banda amachokera m’mudzi mwa Nameta Mfumu yayikulu Chimaliro, m'boma la Thyolo.
Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA
Wojambula chinthunzi cha oganiziridwa – Lilongwe Polisi