Home made cooking oil, crisps, soap and yoghurt

Home made cooking oil, crisps, soap and yoghurt we teach people how to make some things at home to minimise expenditure as prices are increasing eve

17/05/2024

Keep on following this page. share the page so that others may also benefit.
Today, I will post on how we can make shampoo and dishwash liquid.

have a blessed day. ❤️❤️

14/05/2024

Brown sugar, white sugar and rock sugar are all made from sugar cane. Today I will try to turn sugar cane into sugar.

14/05/2024
08/05/2024
Kapangidwe ka sugar njira yosavuta:zofunikamzimbe yokhwima bwino ikuluikulu 3-5potomtondo or blendersefachoyanikira. kap...
05/05/2024

Kapangidwe ka sugar njira yosavuta:

zofunika

mzimbe yokhwima bwino ikuluikulu 3-5
poto
mtondo or blender
sefa
choyanikira.

kapangidwe cake

sendani mzimbe
dulani timapisi ta size ya bwino
ikani mu mtondo/blender
sinjani mpaka juice wa mumzimbemo athe
madzi kapena juice mwachotsa mumzimbemo
ikani mu mpoto,
ikani pamoto wa medium
zibwate ndithu mpaka phala la brown liyambe kuoneka
takasani,
ziphala zija zikayamba kulimbako
khuthulirani malo abwino oti muumitsirepo sugar wanu.
ikani padzuwa
chiphala chija chiuma ndithu
ikani mu mtondo or blender yanu, sinjani
sugar watheka
ngati mukufuna ku mu grader, sefani.

sugar watheka timwe tea.
YEMWE ANGAPANGE SUGAR KUGWIRITSA NTCHITO FORMULA IYI, ATIONETSE KUTI TISILIRE NAWO.

04/05/2024

Lero tipanga sugar: mzimbe ili mbweee!! sugar akusowa komanso kudula. ifeyo tea timwa basi.

24/04/2024

tipange surf/ powdered soap

zofunika

madzi 8 litres
palm oil 4 litres
jelly powder 2 table spoon
perfume 2 drops
caustic soda 2kgs
pelo
chotakasila
plastic paper
color m***a kuika kapena ai.
anthu awiri. otakasa ndi osakaniza

kapangidwe

tenga mawese/palm oil oti watenthesa Azizira ika mumadzi okwana 8 litres. takasa
ika jelly powder, takasabe
ika perfume, takasabe
tenga caustic soda 2kgs uzingowaza mu zomwe waphatikiza kale zija, otakasayo asasiye azingotakasa
ayamba kupanga mabulu ouma, takasabe. akafikapo, yalani plastic paper ija padzuwa, khuthulirani pamenepo. zisiyeni ziziuma. surf/ powdered soap uyu atha kutenga 3-5 days kuti aume bwinobwino. Akauma, m***a kumaphwanya mabulu ndi manja kapena kugwiritsa ntchito sefa.

watheka ameneyo gwiritsani ntchito.

pangani share kwa anzanu, muma group kuti ena athandizike.

zikomo

24/04/2024

Tiyambe ndi soap opaka/wa tablet.

zifunika

palm oil/ mawese 4 litres
madzi 8 litres
jelly powder 2 table spoon
color/ dye 2 table spoon
perfume 2 drops
caustic soda 1kg
chikombole
plastic paper
chotakasira
pelo ya 20 litres
anthu awiri. wina azithira zifunikazo, wina azitakasa.

kapangidwe

tenga mawese/ palm oil ( 4 litres) wilitsa. atenthe kuchotsa chiwisi. Phula, ika mu pelo lomwe uzipangira soap
tenga madzi (8 litres) ika momwe muli mawese/palm oil. yamba kutakasa.
thira Jelly powder. osasiya kutakasa
thira dye. takasabe
thira perfume osasiya kutakasa.
paja ndanena kuti mukhale anthu awiri. wina otakasa wina osakaniza zofunikira musopo

tenga madzi 2 litres
tenga caustic soda 1 kg, sungunula mu madzi a 2 litres aja. takasabe mpaka caustic soda asungunuke.
tenga izi wasungunulazi ika momwe unaphatikiza mafuta ndi Zina muja, otakasa asasiye aziingotakasa.
ayamba kulimba. takasabe
tenga plastic paper yala, ika chikombole ika pamwamba pa plastic paper
khuthula soap wako mu chikombole
vundikira ndi plastic paper
dikira kwa 2 hours
chosa plastic paper.
soap watheka. koma timudikirebe kwa 24-48 hours kuti caustic soda athe mphamvu.
dulani ma size akukonda kwanu. gwilitsani ntchito.

pangani share kuti anzanunso athandizike.

tsiku lina izakhala live video kuti muzaone mmene zikhalira.

zikomo

24/04/2024

Takonzekano. tiyambepo kukupatsani ma recipe a momwe mungapangire zinthu monga soap, shampoo, juices, sugar mandasi ndizina. izi zithandiza kuphweketsa moyo. zinthu zadula, chonde tiyeni tiziyesera.

Address

Lilongwe
P.O.BOX1988,LILONGWE

Telephone

+265995615301

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Home made cooking oil, crisps, soap and yoghurt posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Home made cooking oil, crisps, soap and yoghurt:

Share