16/09/2024
Bungwe loyendetsa zamayeso la MANEB mogwilizana ndi unduna wazamaphunziro masanawa akuyembekezeka k*tulutsa zotsatira zamayeso a form 4 a chaka chino.
Nduna yazamaphunziro a Madalitso Kambauwa Wirima komanso mkulu wabungwe la MANEB professor Dorothy Nampota ndiwo akuyembekezeka k*tsogolera msonkhano wa atolankhani oulutsa zotsatirazi omwe uchitikire mumzinda wa Lilongwe.
(09/16/2024)