30/09/2023
CHITITSANI CONVENTION PASANATHE MASIKU 90.
Judge wa bwalo lalikulu la milandi justice Simeon Mdeza walamula chipani chotsutsa boma cha DPP kuti chichititse msonkhano waukulu osankha atsogoleri achipanichi pasanathe masiku 90.
Bwaloli lalamulaso kuti zonse zimene mkumano waukulu wachipanichi unagwirizana pa 3 July 2023 Ku nkopola lodge kumangochi ndizosavomerezeka.
Mwazina nthumwi kumkumanowu zinamvana kuti a Peter Mutharika ndiwo akaimire chipanichi pa chisankho cha 2025 komaso anasankha committee yosungitsa mwambo yomwe imatsogozedwa ndi a Goerge Chaponda.
Bwaloli lapezaso DPP yolakwa posatsatira chigamulo cha court cha pa 5 may 2022.
Mtsogoleri wa chipanichi mchigawo cha kummwera Kondwani Nankhumwa, mlembi wachipani Grezedder Jeffrey, msungichuma Jappie Mhango ndi ena ndi omwe anakasuma ku court.