Thocco Davis Mw_sports & news

Thocco Davis Mw_sports & news sports news and fixtures 😓 maturity ❌

03/12/2025

BULLETS YAONJEZERA NZERU ZA APHUNZITSI AWO

Timu ya FCB Nyasa Big Bullets inachititsa maphunziro a aphunzitsi atimuyi kuyambira timu yaikulu, yaing'ono, yachisodzera komanso ya amayi pofuna uonjezera upangiri wa aphunzitsiwa.

Maphunzirowa anachitika kutsatira mgwirizano wa timuyi ndi sukulu yosula aphunzitsi a mpira ya SK Academy ys mdziko la Britain ndipo amaphunzitsa ndi a Dan Quigley ndi a David Ramjee lachiwiri ku Blantyre.

Maphunzirowa anapereka upangiri kaphunzitsidwe, kuika nzeru zapadera pa masewero, kaganizidwe komanso mphamvu ndipo sukuluyi yati aphunzitsi anali ndi njala yofuna kuphunzira kwambiri ndipo zithandize kuti akhale ndi osewera abwino omwe aziwathandiza kutenga zikho.

Mphunzitsi watimu yaikulu, Peter Mponda, wati maphunzirowa anali opambana omwe awathandizire pomwe akuyenda mu masewero akumapeto amu ligi ya TNM.

''Linali tsiku lopambana kwa aphunzitsi a Bullets ndipo maphunzirowa atitsuka upangiri wathu pa kuganiza, mphamvu, kaphunzitsidwe ndi kuwerenga masewero. Ndi masewero asanu atsalawa mu ligi zitithandiza kuchotsa phuma komanso kukonzekeretsa kaganizidwe ka osewera,'' anatero Mponda.

Iye anatinso izi zithandizire kuti osewera akamachoka kutimu yaing'ono azikhals kale ndi kaseweredwe komanso nzeru zofanana ndi kutimu yaikulu yawoyo.

03/12/2025

Man city fans any word to Brentford so far?

Ambiri akuti even draw is enough🤣

03/12/2025

Dzulo Erling Haaland wapanga mbili pamene wakwanitsa zigoli 100 mu Premier League atasewera masewero 111 okha. Palibe osewera wina aliyense amene anakwanitsa kugoletsa zigoli zochuluka chonchi pa masewero 111 okha mu mbili ya mpikisanowu.

02/12/2025

💔 Why so soon

Rest strong legend 🕊🕊

02/12/2025

Nyumba ya malamulo masanawu ikhala mphindi imodzi ya chete kukhunza imfa ya osewera mpira wakale wadziko lino Essau Kanyenda yemwe wamwalira lero

Phungu wa dera la nsanje south west a Walter Nyamilandu ndamene apempha izi mnyumbayi ponena kuti kaswiriyu wathandiza kwambiri timu ya mpira wamiyendo ya dziko lino.

Black MambaMSHRIP🕊💔
02/12/2025

Black Mamba

MSHRIP🕊💔

02/12/2025

Chimodzi mwa zigoli za Essau Kanyenda yemwe amadziwika ndi dzina loti black mamba

Rest well legend🕊💔😭

Now confirmed Essau Kanyenda the black mamba is no more😭May his soul rest in peace💔
02/12/2025

Now confirmed Essau Kanyenda the black mamba is no more😭

May his soul rest in peace💔

02/12/2025

Haaland

Queens in Pool 1
02/12/2025

Queens in Pool 1

02/12/2025

Timu ya mpira wa manja ya dziko lino, ya Malawi Queens ili mugulu 1 momwe muli matimu a South Africa, Botswana komanso Tanzania mumpikisano wa Africa Netball Cup omwe dziko lino likhale likuchititsa.

Ndipo timu ya a bambo ya Kings ili mugulu 2 momwe mulinso matimu a Eswatini, Kenya komanso Namibia.

Izi zikutsatira mayere omwe achitika.

Ku amayi, mugulu 2 muli matimu monga Uganda, Zimbabwe, Namibia komanso Kenya pamene kwa bambo mugulu 1 muli matimu a South Africa, Zimbabwe, Botswana komanso Uganda.

Mpikisanowu uyamba pa 8 mpaka pa 14 December 2025 pa bwalo la Griffin Saenda Sports Complex mu nzinda wa Lilongwe.

02/12/2025

Caicedo's suspension means he'll miss these three Chelsea games:

• Leeds United away
• Bournemouth away
• Everton at home

Caicedo was awarded a red card when chelsea plays with arsenal in English premier league on Sunday

Address

Davis Sports And Funs
Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Thocco Davis Mw_sports & news posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share