22/07/2025
Mwamukumbukila Musa John?
Bwalo la milandu ku Limbe lalamula Musa John kuti apereke K150,000 kamba kophwanya ma galasi a malo ena omwera mowa pa Kachere ku Blantyre.
Oyimira boma pa milandu a Monica Muotchamanja anauza bwalo kuti John analedzera nkupita pa malo ena omwera mowa pomwe anayambitsa mpungwepungwe kenako kuphwanya magalasi apamalowa.
John M***a anapempha bwalo kuti limukhululukire kamba koti amathandiza mayi ake ndi abale ake koma oweruza mulandu a Chrissy Kachingwe analamula John kupereka K150,000.
John yemwe ndi wa zaka 20 anamangidwako mbuyomu kaamba kopezeka ndi chamba chochuluka .
(by Chikondi Mphande-Blantyre:07/21/25)
Source | Zodiac news