Malawi Boxing News

Malawi Boxing News The page gives Boxing events as it unfolds.
(1)

Visit Us anytime for updates🥊🥊🥊🥊 Call/WhatsApp+265998434434 or +265993412980 Amatuer and Malawi Professional Boxing page)

13/07/2025

Media yaku Zimbabwe yatipanga tag nkhani ya Lano paja anati adzabweza chipongwe chomwe anapangidwa ndi Charles Manyuchi.

Paja naye wapuntha Gogodo posachedwa.

🥇Bantamweight (54kg)🏆 GOLD: Bwembya Dexter – Zambia 🇿🇲🥈 SILVER: Wasili Richard – Malawi 🇲🇼🥉 BRONZE:* Moyo Crein – Zimbab...
12/07/2025

🥇Bantamweight (54kg)

🏆 GOLD: Bwembya Dexter – Zambia 🇿🇲
🥈 SILVER: Wasili Richard – Malawi 🇲🇼
🥉 BRONZE:
* Moyo Crein – Zimbabwe 🇿🇼
* Mokhitli Reabetsoe – Lesotho 🇱🇸

Waison Dick amene amadziwika ndi dzina lakuti General Bangwe atamenyedwa ndi Mayamiko Mozland anadandaula kwa Salim Chaz...
12/07/2025

Waison Dick amene amadziwika ndi dzina lakuti General Bangwe atamenyedwa ndi Mayamiko Mozland anadandaula kwa Salim Chazama Kuti anapatsidwa chifwamba chomwe chinkafuna kumupha pa ring.

Ulendo uno pa 27 July, 2025 ku Bremat Multpurpose Hall General, Bangwe akubweraso pa ring ndipo watola Mike Phiri. Anthu omwe anaonerako Mike Phiri akuti uyuso ndiwankhaza ndipo General Bangwe akonzeke mokwanira.

"Mwana uyu ndiwama uppercut oyipa, ndipo mphuno ya Bangwe ikalandikira zibakera" wina otsatira nkhonya watinong'oneza. Kodi General aiphula ulendo uno?, Zonse ndipo 27 July.

12/07/2025

Richard Wasili ndiwankhonya amene wakwanitsa kubwera ndi medal ya silver ngakhale zavuta kupambana nkhonya yake yomaliza pamene amakumana ndi katswiri waku Zambia.

Uwu unali mkumano wadzifwamba
12/07/2025

Uwu unali mkumano wadzifwamba

12/07/2025

Snowden Munyanje (in white vest) kulimbitsarana matupi ndi Chikondi Makawa, komatu kunali kupatsana zibakera ngati ayambana.

11/07/2025

Atapeza chipambano munkhonya yake yoyamba Richard Wasili madzulo alero akulowaso mu ring ndipo asinthana zibakera ndi katswiri waku Zambia.

Wasili ndi amene akuonetsa tsogolo lotibweretsera medal ngati angapeze chipambano.

Youth Boxing Promotion ikutitengeraso ku Bremat Multpurpose Hall pa 27 July, 2025, ulendo uno Israel "The money machine"...
11/07/2025

Youth Boxing Promotion ikutitengeraso ku Bremat Multpurpose Hall pa 27 July, 2025, ulendo uno Israel "The money machine" kamwamba komaso Hannock "The hard nocker" Phiri ndiomwe akutengerana pakati pa zingwe zinayi munkhonya yaikulu patsikuli.

Salim chazama mkulu wa Youth Boxing Promotion walengeza kuti.Jonathan wakanda muteba waku DRC ndiyemwe akutengerana muka...
10/07/2025

Salim chazama mkulu wa Youth Boxing Promotion walengeza kuti.
Jonathan wakanda muteba waku DRC ndiyemwe akutengerana mukachipinda komata ndi Brendon Denes wochokela dziko la Zimbabwe pa 27th July ku bremat multpurpose hall. Amene agonjetse mzake apa ndiyemwe akudzaswana ndi waku Malawi.

Muteba akuchokera kogonjetsa Ezra Sifoliano waku Malawi ndipo naye Denes akuchokera kogonjetsa Dickson Saidi waku Malawi

10/07/2025

Dzama Ishmael (in red trunks) wakumalawi wagonja kwa Mogolodi Samuel waku Botswana.

Pakadali pano pa ankhonya akumalawi okwanira 4 omwe asewera mmodzi yekha ndi amene wapeza chipambano ndipo atatu agonja, mumpikisano wa region 5 omwe ukuchita ku Namibia.

09/07/2025

Lero zativuta

Deborah Mtenje(in red trunks) waku Malawi wagonja kwa Namibia’s Mischa Araes waku Namibia, mu mpikisano wa region 5 omwe ukuchita ku Namibia.

Ngakhale zavuta komabe naye Deborah Mtenje waonetsa kuti ndiomenya wabwino.

09/07/2025

Chidule Hanneck (in red trunks) wochokera ku Malawi wagonja pama points ndi Mapalo Joseph Chada ( in blue trunks) waku Zambia. Mu mpikisano wa region 5 omwe ukuchita ku Namibia.

Address

Lilongwe

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Malawi Boxing News posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Malawi Boxing News:

Share