23/08/2025
Akabambe alemba izi pa tsamba lawo la Facebook:
Osalola kunamizidwa ndi anthu osachita nalo bodza manyanzi olo atakhala m'busa, ngakhale malemba ananena momveka bwino kuti ambiri aneneri onyenga adzadzuka masiku otsiriza. MCP komanso Achakwera analonjeza amalawi 4 million jobs mu 2019. Ife tinalonjeza 1 million jobs, akanika kukwaniritsa 1 million jobs akuti manifesto yathu sinali realistic, nanga 4 million yawoyo apanga create how many jobs, koma pakati pa 4 million jobs and 1 million jobs who was not realistic?
Fertilizer anapanga promise K25,000.00 paliponse from Nsanje to Chitipa (universal subsidy program), kawerengeni manifesto yawo ya 2019 muzipeza. Actually, costing of universal subsidy from Nsanje to Chitipa was way expensive than making K4,495.00 to a few people. Lero, ngakhalenso anapanga adopt idea ya K4,495.00 which worked in the only first year Dr. Chilima was part of the cabinet analepheranso to sustain.
Nkhani iri apa ndi dyera. Anthuwa ankawona ngati Boma limangoziyendera ngati wamisala. Zoti someone has to control and work behind the scene sankadziwa, we trusted the economy on pastors, bambo m'busa, mwana m'busa, mpongozi naye m'busa, lero economy has been m'busalized, aliyense angolira mayo mayo, tonse ndife alazalo aumphawi amasikini, akafa nsiyanji.
Ndimanena mobwerezabwereza kuti ulendo uno osapereka Boma kwa anthu omwe alibe zoziyenereza kuyendetsa economy yathuyi. It's really sad that a pastor can stand and disown his own promises. Palibe anawakakamiza abusa to adopt UTM manifesto in 2020, anali ndi ufulu opitiliza ndi Hi 5. Zomwe akupanga apa zusonyeza kuti abusa aja ngosakhulupilika, don't trust him on anything, not even with a bottle of brandy.
Amalawi tiphunzire kumawona small things and taking lessons from there. Zimathandiza kupewa mavuto ambiri patsogolo. Kukakana akukana leroli, mukuona ngati 2030 sadzakananso? Ife tikuti let's vote for change, vote for Dr. Kabambe, the only leader who shall up and account for every promise he made. Mwanamizidwa nthawi yayitali palibe waona kusintha, Singapore sitinamuone, try us, change is here