MBC 2 OntheGo

MBC 2 OntheGo The official MBC TV 2 page.
(1)

Kodi kudzafika kukhala  CEO wa Sports Council unali ulendo otani?  Zonsezi mu program ya Madolo Pamasewero sabata ino nd...
13/05/2026

Kodi kudzafika kukhala CEO wa Sports Council unali ulendo otani? Zonsezi mu program ya Madolo Pamasewero sabata ino ndi Ivy Chinangwa


‎   ‎M'modzi mwa amkhalakale pamingoli Lawrence Khwisa wati zonse zokhudza phwando lamaimbidwe la Lulu @25 Concert  zili...
13/05/2026



M'modzi mwa amkhalakale pamingoli Lawrence Khwisa wati zonse zokhudza phwando lamaimbidwe la Lulu @25 Concert zili mchimake.

‎Phwandoli ndi lokondwerera kuti watha zaka 25 akuimba maka kuchokera pomwe nyimbo yake inamveka koyamba pa wailesi.

‎Katswiriyu wati kudzisunga, kukhulupilira mulungu komanso kuphunzira tsiku ndi tsiku ndi chinsinsi chokhacho chomwe amagwiritsa ntchito.

‎Lawi ndi Namadingo ndi omwe akamuthandizire oimbayu kuphhwandoli kumapeto a mwezi wa August chakachino.

‎Wolemba: Emmanuel Chikonso

゚viralシ

13/05/2026

Catch Get Up and Go
Mon-Sat 6AM - 8AM

Koma nkhani zina abale. 😂😂🙌
.......
゚viralシ

13/05/2026

Good morning on Wednesday 🔥🔥
Mwatumiza kale ma good morning kwa anthu onse ofunikira?

Waishosha yatentha pomwe matimu akupitilira kupumitsa aphunzitsiPomwe FDH premieship yangotha sabata yachitatu, matimu o...
12/05/2026

Waishosha yatentha pomwe matimu akupitilira kupumitsa aphunzitsi

Pomwe FDH premieship yangotha sabata yachitatu, matimu omwe sadayambe bwino mumpikisanowu akulephera kuugwira pomwe akupititsa aphunzitsi awo kutchuthi chokakamiza pofuna kusintha kachitidwe kamatimuwa.

Mphindi zapitazi Kamuzu Barracks yalengeza kuti yapititsa kutchuthi mphunzitsi wake Tione Mhone komanso wachiwiri wake Joseph Chilapondwa kamba kakusachitabwino kwatimuyi.

Kamuzu Barracks, idagonja masewero oyamba ndi Silver Strikers komanso Luannar Mitundu FC ndipo yafanananso mphamvu ndi timu ya Karonga United mu sabata yachitatu.

Padakalipano timuyi yasankha Kenwood Nkhoma kukhala mphunzitsi wogwirizira.

Kuimitsidwa kwa aphunzitsi a KB kwadza patangotha sabata imodzi nayo Ekhaya itapititsanso mphunzitsi wake Ennos Chatama kutchuthi atangotsogolera masewero awiri okha omwe adafananitsa mphamvu amodzi komanso kugonja amodzi.

Iyiyi ndiye ndi Waishoshadi..

By: Foster Maulidi


12/05/2026



M'modzi mwa oimba mdziko muno Amidu Ellan yemwe anatchuka ndi nyimbo ya 'Udikerebe' wati anthu ayembekezere nyimbo zatsopano pomwe wamaliza kuphika mingoliyi.

Amidu wati pano ganizo ndilofuna kufikira anthu ochuluka kuposa kale.

゚viralシ

‎ ‎‎Mtsogoleri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering a Shepherd Bushiri ati alandira kupepesa kwa katswiri oimba ...
12/05/2026



‎Mtsogoleri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering a Shepherd Bushiri ati alandira kupepesa kwa katswiri oimba Peter Sambo yemwe pakatipo wakhala akulemba zonyozetsa mneneriyu pamodzi ndi banja lake komanso mpingowo pa masamba amchezo.

Peter Sambo masiku apitawo kudzera pa Facebook anapepesa a Bushiri omwe anali atawuza maloya awo kuti atengere nkhaniyi ndi oimbayu kubwalo lamilandu.

‎Kudzera mchikalata chomwe atulutsa a Bushiri ati amvetsetsa kuti a Sambo amachita izi kamba ka uthenga olakwika komanso mkwiyo omwe anali nawo.

‎"Kupepesa komanso kuvomereza kulakwa kwawo ndikunena kuti afufuta zomwe analemba ndikusonyeza kugonja komanso kudzichepetsa kwawo. Ine ngati munthu okhulupirira ndawakhululukira a Sambo, " atero a Bushiri.

Mneneriyu wapempha anthu kuti adzigwiritsa bwino ntchito masamba amchezo mmalo mofuna kuwononga ena kapena kuwapititsa pansi.

‎Wolemba: Emmanuel Chikonso
‎ ゚viralシ

Stay tuned for more programs on MBC2onthego 🔥🔥 Mukudikira iti ?
12/05/2026

Stay tuned for more programs on MBC2onthego 🔥🔥
Mukudikira iti ?

12/05/2026

Good morning on a Tuesday 🔥🔥
Kuli bwanji kumeneko?

11/05/2026

NEWS ON 2 @ 6PM

Stay tuned to MBC2onthego for more programs🔥🔥
11/05/2026

Stay tuned to MBC2onthego for more programs🔥🔥

Address

Malawi Broadcasting Corporation Box 162 Lilongwe
Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when MBC 2 OntheGo posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to MBC 2 OntheGo:

Share

Category