
25/07/2025
A Timothy Mtambo omwe ndiwachiwiri kwa mtsogoleri wachipani Cha AFORD ati ndi okhumudwa ndi mgwilizano omwe chipani cha AFORD ndi DPP apanga.
Amtambo ayankhula izi lero pamsonkhano wa atolankhani omwe akuchititsa ku Ufulu Gardens mumzinda wa Lilongwe.
Mwazina Iwo anati sangaikire kumbuyo ganizoli chifukwa cha zofooka za chipani cha DPP monga kulephera kuyendetsa bwino dziko, kukondera mitundu ndi zina.
(Blessings Khumzana Mwale, 25/07/25)
Tate online