
01/09/2025
https://www.facebook.com/reel/1301022618472966/?app=fbl
"Tipanga Nawo MW2063 Back-to-School Project Fundraising Show: A day to Remember!
We were thrilled to partner with Ace Jizzy and Bee Jay at Don Bosco College Hall for an unforgettable fundraising show! The energy was electric, and the generosity was inspiring. Thanks to everyone who supported us in our mission to bring education to underprivileged youth. Together, we're making a difference! "
Anyasulu ndi Brian, (Ace Jizzy komanso Bee Jay) akuyembekezeka kuyatsa moto usiku uno ku Don Bosco, Area 23 mu mzinda wa Lilongwe, komwe kuli phwando lamayimbidwe lomwe akonza ndi a bungwe la Active Youth Organisation (AYOD).
Malingana ndi mkulu wa bungweli a Vitumbiko Visangwika Ngwira, phwandoli alikonza ndi cholinga chofuna kupeza 10 million Kwacha yoti athandizire ophunzira osowa okhala mozungulira delari, omwe apanga chisankho chobweleranso ku sukulu.
Bungweli lati likufuna kuthandiza ophunzira 35 omwe ndi aku sekondale komanso ena aku koleji zosula luso la manja.
Ntchitoyi ili pansi pa Tipanga Nawo Malawi 2063 Back to School Project.
(by Innocent Kumchedwa -Lilongwe;08/31/25)