09/12/2025
Apolisi ku Lilongwe amanga msungwana wa zaka 18 Prisca Leman kamba komuganizira kuti wapha chibwezi chake Kingsley Magombo wazaka 25, pomubaya ndi sizasi.
Malingana ndi mneneli wa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu izi zachitika loweluka pa 6 December kwa Katantha chaku Area 38.
A Chigalu ati patsikulo awiriwa adapita ndithu limodzi kokamwa mowa kwa Kaphiri, kenaka anatengana kupita kwa mnyamatayu (Kingsley), komwe iyeyu anali ndi kachisakasa kake kogulitsira mowa.
Koma akuti atafika kunyumba kuja, amayi ake a Kingsley, adamuuza kuti safuna kumuwonanso ali ndi msungwana ameneyo, (kunena Prisca) ndipo adati azipita kwawo.
Koma awiriwa ngakhale adakalipidwa, sanamvere langizoli, ndipo adapitilira kukalowa mchisakasa muja amagulitsira mowa. Kenaka akuti, awiriwa ali m'menemo mkangano unabuka pakati pawo, omwe unadzetsa ndeu. Apolisi ati, ndeu ili mkati Prisca anatulutsa sizasi ndikubaya chibwezi chakechi pa mtima.