Love Beyond Status Radio

Love Beyond Status Radio LBS "where true love exists" https://Lbsradio-dexterity.radioca.st/stream

Our radio station offers honest talks on love, relationships, and daily challenges like finance, gender based violence, and mental health to promote understanding and empowerment.

  Mlembi wamkulu wa Boma, Justin Saidi, wati malemu Brian Banda anali ndi masomphenya ofuna kusintha Malawi Broadcasting...
10/08/2026


Mlembi wamkulu wa Boma, Justin Saidi, wati malemu Brian Banda anali ndi masomphenya ofuna kusintha Malawi Broadcasting Corporation (MBC) kukhala bungwe lotumikira anthu onse m’dziko muno.
Saidi wati mtsogoleri wa dziko komanso anthu ena ambiri akumva chisoni ndi imfa ya Banda, yemwe anali ndi masomphenya okweza kayendetsedwe ka MBC.
Iye wapempha ogwira ntchito onse ku MBC kuti apitirize masomphenya omwe Banda anali nawo pa kayendetsedwe ka bungweli.
Saidi wati analankhula ndi Banda sabata yatha ndipo wati imfa yake yamukhudza kwambiri.
“Ine ndayankhula naye last week yomweyi. Pakumva kuti wamwalira ndi zachisoni. Ambuye amulandire. Atichitire chisoni. A President akulira nanu ndipo sakutayani,” atero Saidi.
Mwambo waMaliro a malemu Brian Banda ukuchitikira ku M’banda Village, Chileka, Blantyre.
Wolemba: Chrispin Tsitsamanja

 Mlembi wamkulu wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP), Peter Mukhito, wati malemu Brian Banda ankamvetsa bwi...
10/08/2026


Mlembi wamkulu wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP), Peter Mukhito, wati malemu Brian Banda ankamvetsa bwino mphamvu ya kulankhulana ndi anthu.

Mukhito wati Banda ankadziwa kuti maikolofoni sinali chida chongofalitsira nkhani, koma ankagwiritsa ntchito mapulogalamu ndi zokambirana zake kuti abweretse nkhani za ndale pafupi ndi anthu wamba komanso kulimbikitsa atsogoleri kufotokoza za zomwe amachita.

Mukhito wanena izi pa mwambo wa maliro a malemu Brian Banda omwe akuchitikira ku M'banda Village, ku Chileka mumzinda wa Blantyre.
Walemba: Chrispin Tsitsamanja

 Banja Lati Imfa ya Brian Banda Yawabweretsera Chisoni ChachikuluAkubanja la malemu Brian Banda, omwe anali mtolankhani ...
10/08/2026


Banja Lati Imfa ya Brian Banda Yawabweretsera Chisoni Chachikulu

Akubanja la malemu Brian Banda, omwe anali mtolankhani wodziwika bwino, ati imfa yawo yabweretsa chisoni chachikulu pa moyo wawo komanso m’banja.

Poyankhula m’malo mwa akuchimuna, a Bwanali ati Banda amwalira ali ndi zaka 46, ndipo wasiya mkazi komanso ana 6.

Mmodzi mwa ana a malemuyu wati bambo awo anali msanamira wa banja, choncho imfa yawo yawapweteka kwambiri.

Malemu Brian Banda anali mtolankhani wodziwika ndipo amagwirapo ntchito ku Times Group ndipo amwalira Ali Director General wa Malawi Broadcasting Corporation (MBC).

Wolemba: Chrispin Tsitsamanja

 Wapampando wa bungwe la Malawi Broadcasting Corporation (MBC), Benson Tembo, ati imfa ya Brian Banda ndi tsiku lowawa k...
10/08/2026


Wapampando wa bungwe la Malawi Broadcasting Corporation (MBC), Benson Tembo, ati imfa ya Brian Banda ndi tsiku lowawa kwambiri kwa bungweli komanso kwa anthu omwe amatsatira ntchito za MBC.

Tembo ati Banda anabwera ku MBC ndi cholinga chokweza ntchito za bungweli kuti lizitumikira bwino anthu a ku Malawi, ndipo kuchoka kwake kwasiya kusiyana kwakukulu pa ntchito za bungweli.

Iwo ati Banda anali munthu womvetsetsa, wokonda kugwira ntchito mwaukadaulo komanso wolimbikitsa ena kuti azichita bwino ntchito yawo.

Tembo wayamikira Banda chifukwa cha ntchito yomwe wagwira ku MBC, ponena kuti cholowa chake chidzapitiriza kukumbukiridwa.
olemba: Chrispin Tsitsamanja

 Felix Washon, nkulu wa bungwe la atolankhani la MISA Malawi, walimbikitsa atolankhani kuti azilemba nkhani zoona komans...
10/08/2026


Felix Washon, nkulu wa bungwe la atolankhani la MISA Malawi, walimbikitsa atolankhani kuti azilemba nkhani zoona komanso zokhala ndi umboni wogwirika, ponena kuti izi ndi zofunika kwambiri pa ntchito ya utolankhani.

Washon ananena izi pa mwambo wa maliro a Brian Banda, yemwe anali mtsogoleri ku MBC, womwe unachitikira ku Chileka mumzinda wa Blantyre.

Washon wayamikiranso moyo wa malemu Banda, pomufotokoza ngati mtolankhani yemwe ankafalitsa uthenga molimba mtima komanso mopanda mantha.
By Chrispin Tsitsamanja

  Kuli Mkoke-mkoke Lamulungu la pa 26 July 2026 ku Bangwe pomwe matimu a William Fc komanso Falujah Fc akhale akugiligis...
08/08/2026


Kuli Mkoke-mkoke Lamulungu la pa 26 July 2026 ku Bangwe pomwe matimu a William Fc komanso Falujah Fc akhale akugiligishana mu ndime yotsiliza ya mpikisano wa Bangwe Football Bonanza pa bwalo la Naizi.

Matimu okwana khumi ndi asanu ndi imodzi ndi omwe anatenga nawo mbali mu mpikisanowu omwe unayamba myizi ingapo yapita.

Timu ya William Fc inafika ndime yotsiliza itagagada anyamata a Griffin Star, Ndipo anyamata a Fallujah Fc nawo anafika mu ndime yomweyi atakwapula anyamata ochokera kwa Ntopwa a Soccer Giants ndi kuwaonetsa khomo lotulukira la Mpikisano-wu.

Timu yomwe ikhale katswiri wa Bonanza ikuyembekezeka kulandira ndalama zokwana Mk20,000.00 pomwe timu yomwe ithele pa nambala ya chiwiri ipite kwawo ndi ndalama yokwana Mk100,000.00 Kwacha.

Soccer Giants, komanso Griffin Star sasewera masewero awo a mu ndime yofuna kupeza yemwe akhale pa nambala ya Chitatu komabe akhale akulandira ndalama zokwana Mk50,000.00 timu ina iliyonse kamba kofika mundime-yi.

Malinga ndi modzi mwa omwe akuyendetsa Bonanza Mfumu William wauza LBS Radio kuti, Padakali pano zokonzekera Zonse zili m'chimake kuti ma timuwa akhale akulimbirana ndalama zankhanikhanizi.

Mfumu-yi yati ikuyembekezera masewero opambana pomwenso akuyembekezeka kulandira alendo osiyana-siyana omwe amayendetsa masewero ampira wa miyendo mu nzinda wu.

Bonanzayi ndi ya ndalama zokwana 500,000 Malawi Kwacha.

Wolemba: Frank Bashir Wailesi
25/07/2026

 Thupi la yemwe anali mkulu wa wailesi ya boma ya Malawi Broadcasting Corporation (MBC) a Brian Banda likuyembekezera ku...
08/08/2026


Thupi la yemwe anali mkulu wa wailesi ya boma ya Malawi Broadcasting Corporation (MBC) a Brian Banda likuyembekezera kulowa m'manda lolemba pa 10 August 2026 ku mudzi kwawo ku Chileka mu mzinda wa Blantyre.

Malingana ndi woyankhulira Wailesi ya boma a Chisomo Mwamadi, ati mwambo okatenga thupi la malemu Banda uchitika la mulungu Pa 9 August 2026 kuchokera ku nyumba ya chisoni ya Mthunzi 11:00 m'mawa ndipo lizakhala likulowera ku kachisi la World of Faith ku Chilobwe mu mzinda wa Blantyre.

Ndipo thupili lizakhala likulowera ku mudzi kwawo lolemba pa 10 August komwe likuyembekezera kuzalowa m'manda mudzi mwa M'banda pafupi ndi bwalo la ndege la Bakili Muluzi International Airport mu nzinda wa Blantyre.

Wolemba: Frank Bashir Wailesi
08/08/2026

 Multiple sources confirm the passing of Brian Banda, the Director General of Malawi Broadcasting Corporation (MBC). Acc...
08/08/2026


Multiple sources confirm the passing of Brian Banda, the Director General of Malawi Broadcasting Corporation (MBC).
According to reports, Banda died after a brief illness at Mwaiwathu Hospital in Blantyre.

His sudden departure has shocked colleagues and the public alike, as he was a prominent figure in the country’s media industry.

LBS will continue to follow this developing story and provide updates as more information becomes available.

 Kuli Mkoke-mkoke Lamulungu la pa 26 July 2026 ku Bangwe pomwe matimu a William Fc komanso Falujah Fc akhale akugiligish...
26/07/2026


Kuli Mkoke-mkoke Lamulungu la pa 26 July 2026 ku Bangwe pomwe matimu a William Fc komanso Falujah Fc akhale akugiligishana mu ndime yotsiliza ya mpikisano wa Bangwe Football Bonanza pa bwalo la Naizi.

Matimu okwana khumi ndi asano ndi imodzi ndi omwe anatenga nawo mbali mu mpikisanowu omwe unayamba myizi ingapo yapita.

Timu ya William Fc inafika ndime yotsiliza itagagada anyamata a Griffin Star, Ndipo anyamata a Fallujah Fc nawo anafika mu ndime yomweyi atakwapula anyamata ochokera kwa Ntopwa a Soccer Giants ndi kuwaonetsa khomo lotulukira la Mpikisano-wu.

Timu yomwe ikhale katswiri wa Bonanza ikuyembekezeka kulandira ndalama zokwana Mk200.0000, pomwe timu yomwe ithele pa nambala ya chiwiri ipite kwawo ndi ndalama yokwana Mk100.0000 Kwacha.

Soccer Giants, komanso Griffin Star sasewera masewero awo a mu ndime yofuna kupeza yemwe akhale pa nambala ya Chitatu komabe akhale akulandira ndalama zokwana Mk50.0000 timu ina iliyonse kamba kofika mundime-yi.

Malinga ndi modzi mwa omwe akuyendetsa Bonanza Mfumu William wauza LBS Radio kuti, Padakali pano zokonzekera Zonse zili m'chimake kuti ma timuwa akhale akulimbirana ndalama zankhanikhanizi.

Mfumu-yi yati ikuyembekezera masewero opambana pomwenso akuyembekezeka kulandira alendo osiyana-siyana omwe amayendetsa masewero ampira wa miyendo mu nzinda wu.

Bonanzayi ndi ya ndalama zokwana Mk 500.0000 Malawi Kwacha.

Wolemba: Frank Bashir Wailesi
25/07/2026

https://onlineradiobox.com/mw/lbs/ https://Lbsradio-dexterity.radioca.st/stream
https://liveonlineradio.net/lbs-radio
we are also on A2z app

  Timu ya Goshen City Dedza Dynamos yakhala timu yoyamba m'chaka Chino kugonjetsa timu ya FCB Nyasa Big Bullets pa masew...
25/07/2026


Timu ya Goshen City Dedza Dynamos yakhala timu yoyamba m'chaka Chino kugonjetsa timu ya FCB Nyasa Big Bullets pa masewero omwe analipo Loweluka pa 25 July 2026 pa bwalo la Dedza Stadium m'boma la Dedza.

Chigoli chimodzi chochokera kwa Marco Chiwaya pa mphindi 41 za mchigawo choyamba chinali chokwanira kuti mapalestina akwanitsa kuyenda chimanga manja m'boma la Dedza.

Awa ndi masewero oyamba Bullets kuti chaka chino igonje pomwe yakwanitsa kusewera masewero okwana khumi ndi amodzi (11) ndipo yakwanitsa kupambana masewero okwana asanu ndi kufananitsa mphamvu masewero asanu ndipo yagonja masewero amodzi.

Mumasewero ena timu ya Blue Eagles Yakwapula Mikango yofira yaku Zomba ndi zigoli zitatu kwa ziwiri (3-2) Masewero omwe analipo pabwalo la Nankhaka mu mzinda wa Lilongwe.

Chitipa United Yagonjetsa timu ya Ekhaya ndi chigoli chimodzi kwa duuu (1-0) chomwe anagoletsa katswiri otchedwa Chancy Kaonga mchigawo chachiwiri chamaserowa.

Civil Service United yalephera kutenga mapointsi onse mmasewero omwe anali nawo ndi asilika akukaning'ina a Moyale Baracks chigoli chimodzi kwa duu.

Nkhala kale ku timu ya Moyale Baracks Black Alliseni ndi yemwe anabweletsa Chimwemwe kumbali ya asilikali wa mu nthawi yowonjedzera pomwe masewerowa anali 0-0.

Masewero ena amu FDH Bank Premiership akhale akupitilira Lamulungu la 26 July 2026.

Wolemba: Frank Bashir Wailesi
25/07/2026

https://onlineradiobox.com/mw/lbs/ https://Lbsradio-dexterity.radioca.st/stream
https://liveonlineradio.net/lbs-radio
follow us on A2Z app too

Address

P. O. Box 5207
Limbe
MW1

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Love Beyond Status Radio posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Love Beyond Status Radio:

Shortcuts

Share