Pasimba

Pasimba Muli bwanji abale ndi alongo nose??

Ine moyo ukuyenda ndithu Yehova akutisungabe ndimafuna kukudziwitsani kuti proglam yapasimba inasintha nthawi yomwe imayamba panopa ikumayamba 10:30 usiku lachitatu

27/12/2024

Anthu omwe mumanvera maganizo awo pa wailes paja ndi chifukwa chakuti, ali mu group ya whatsap. inuso maganizo anuwo ndiwofunika kwambili perekani ma numbers anuwo ndikupangeni add nanuso muzinjoya ndi Mij fm πŸ˜€πŸ˜€πŸ˜€πŸ˜€

24/12/2024

Iiiii koma milipo???

13/07/2024

Mongokumbutsana paja tinanena kuti pasimba program izibwerezedwa lero loweluka nthawi ya 10:00 usiku moti lero ilipo ndithu pasimba kwainu amene lachitatu inakuphonyani simunanvere lero tikhale limodzi
Chunani Mij 92.8 fm kapena 93.0 fm kulikose kumene muli kuti tikhalire limodzi usiku uno.

Mij fm radio zaife amakamba ndi anthu πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ˜…πŸ˜…πŸ˜…

11/07/2024

CHIDZIWITSO CHAPADELA

KWATOSE OMWE TIMAKONDA KUNVERA PROGRAM YAPASIMBA TACHITIKA MWAI WAWUKULU KUCHOKERA KU NTHAMBI YOKOZA MA PROGRAM APA WAILES AKUNO KU MIJ FM MOTSOGOZEDWA NDI MABWANA ATHU NDIFE OKONDWA KUKUZANI KUTI TSOPANO PROGRAM YAPASIMBA IZINVEKA KAWILI PASABATA LACHITATU 10:30 USIKU KOMASO KUBWELEZEDWA LOWELUKA 10:00 USIKU PA MIJ FM 92.8FM KOMASO 93 .0 FM ZIGAWO ZOSE ZADZIKO LINO LA MALAWI

Mij fm radio zaife amakamba ndi wanthuπŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯

10/07/2024

Amai akudandawula akuti amauna awo amanva abwino akamawagona akusambamo yale ndi meneyo

19/05/2024

NDIBISENI DZINA KOMA NDIKUFUNA NDIPEMPHE NAWO NZERU PANO PASIMBA.

Ine ndi ntsikana wazaka 24 ndinakwatiwa chaka chino ndi Mamuna wanga tose anyamata ndithu.

Chandibweretsa panopa ndi kusanvana kwapakati pathu pankhani yomwe ikuchitika munyumba mwathu tikamaliza kugonana chomwe chikumachitika ndichakuti akangomaliza Mamuna wanga kuti wakodzera kupita kanthawi pang'ono kungodzuka kuti kaya nditaketake monga nkazi wapakhomo basitu ndikumangowona zithu zokhala ngati madzi zikuyendelera kuchokera kumaliseche kwanga kutsikilira mumiyendo izi zimachitika nthawi zose yomwe tagonana. Ndiye ine ndakhala ndikuwawuza kuti kusatenga pakatiku ndikukayikila kuti umuna wanu amuna anga ndiwopanda mphavu pakufunika tiyende kuti vutoli lithe. Ndinangoti ndayankhula mawu amenewa amuna anga akuti ndizipita ndine hule ndakhala ndikugonana ndi amuna ambili iyeyu sindingamupusitse chifukwa uyeyu akuti Ali ndi mwana yemwe anabereka kwa nkazi wina yemwe anapanga naye chibwezi ineyo ndisanakumane naye ndipo mwanayo amamuthandizadi.

Azilangizi ineyo ngati ndalakwitsa mundiwunikileko koma mwezi uno wa 8 ine mimba sindikutenga ndipo nthawi zina akangomaliza kundigona m'mimba mumandipweteka kwambiri. Panopa akuti ndizipita banja latha ndine hule.

Chonde ndithandizeni maganizo
Zikomo kumpando.

19/05/2024

Dzulo panaponyedwa Topic yomwe ndinkhani yachokela kwa abambo Ena kudandawula za nkazi wawo.

Zikomo kwatose omwe munatengapo gawo maganizo anu awulutsidwa pa program yapasimba.

18/05/2024

Topic ya lachitatu pa 22 May 2024

Akufuna kuthandizidwa maganizo.

Ndine bambo wazaka 34 ndipo ndili ndi ana awili omwe ndinabereka ndi nkazi wanga woyamba yemwe banja langa tinasiyana pazifukwa zina ndipo ndipo anachoka mochita kundithawa kupita kwa abale ake ku Blantyre pepani ngakhale ndayambila pakati Kati nkhaniyi koma timati tikasemphana maganizo ndi nkazi wangayu chowawa chimakhala chakuti amatenga ndalama yomwe wayiwona nkumapita kumudzi kwawo kapena kwa abale ake ndipo amamulandila ndiye vuto lomwe lilipo ndilakuti akazi anga akafika kwawo amakonda kundiyipitsa posakamba cheni cheni chomwe chachitika kuti tisemphane maganizo m'malo mwake amakonda kukamba zongondiyipitsa zowonetsa kuti ndikuwazuza ndipo ndichifukwa chake abwerako kubanja ndipo abale awo amawalandila nkumakhala nawo mopanda kundifusako maganizo anga. Ndiye chaka cha mu 2023 akazi angawa anapitaso kwa akulu awo titayambanaso ndipo anachoka kunyumba ine kulibeko ndinachita kudziwa ndi ana kuti iwo akuti anyamuka akupita ku Blantyre kwa abale awo pamenepo nkuti atawawuza abale awowo kuti ngati asiyilire kuti azikhalabe ndineyo pabanja iwo amwa mankhwala ndipo akozekere kuzanyamula maliro awo kutsazikana kukhala komwe akuyankhulana pa foniku.

Abale awo atanva nkhaniyi anatumiza transport yomwe inawafikitsa kwa akulu awo ku Blantyre ine nsakudziwa ndili kuntchito ndikuyimba Fon kuti nditumize ndalama ya ndiwo ndipomwe anandiyankha kuti ndalama nditumizile mwana chifukwa iwo achokako kunyumba akupita kwa akulu awo ndipo sakabweraso ndinafusa kuti bwanji banja latha?? Anandiyankha kuti eya latha. Zodabwitsa atafika kwa abale awo sanandidziwitse kalikose kuti akazi anga afika alikwawoko ai mpaka ndinakhala kwa 3 weeks ndipamene ndinalandila Fon yondiwuza kuti ndiwakhululukile akufuna kubwelela kunyumba kwawo azindikila kuti analakwitsa.

Komabe alangizi akazi angawa ichi chinangokhala chizolowezi chomatero zomwe ineyo zimandisowetsa ntendere kwambili nditani???





Azi

18/05/2024

Mulibwanji nose amene muli mu group ino yapasimba??

Kuyambila lero lino group ino yapasimba iyamba kugwila ntchito yake mosiyana ndi mene zimakhalira mbuyomu

Panopa tiyamba kumaponyapo nkhani zomwe timakhala tikulandila kuchokera kwa azathu omwe amanvera program yapasimba pa wailes ndicholinga chofuna kuwathandiza maganizo awo pankhani yomwe apempha kuti tiwathandize maganizo.

Ndiye nkhani isanaponyedwe pa wailes iziyamba yaponyedwa ku group kuno kuti tose tiperekepo maganizo anthu ndipo matanizo anthuwo aziwulutsidwa pa radio nthawi ya program yapasimba 10:30 usiku lachitatu.

Chofunika kumachita nkutengapo gawo pankhani yomwe taponya pa group ino popereka maganizo anu.

Ndiye ngati mungafune muzipereka dzina lanu ndikomwe mumakhala kuti tizigwilitsa ntchito powulutsa maganizo anuwo.

Mutu uziyamba kuponyedwa 10:30 mamawa wa loweruka ndi lachinayi.

Mij fm radio zaife amakamba ndi anthu 92.8Fm kumwera ndi 93 .0 Fm pakati ndi zigawo zina zamalawi





Pa

27/11/2023

Uthenga wachisoni

Uncle P,,mai awo atisiya ku kasungu
Pepani Uncle P,, kuluza Mai ndichinthu chopweteka kwambili.

26/11/2023

Amene mukufuna kulowa ku WhatsApp group ya pasimba tipatseni ma numbers anu Uncle p akupangeni add. Zikomo

Address

Manase
Manase

Opening Hours

Monday 09:00 - 17:00
Tuesday 09:00 - 17:00

Telephone

+265880729955

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Pasimba posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share